Eks. 34 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Miyala ina iŵiri(Deut. 10.1-5)

1Chauta adauzanso Mose kuti, “Sema ina miyala ngati iŵiri yakale ija, kuti ndilembepo mau omwe anali pa miyala yoyamba udaphwanya ija.

2Ukonzeke m'mamaŵa, ndipo nthaŵi yam'maŵa, ukwere phiri la Sinai kuti udzakumane nane pamwamba pa phiripo.

3Usabwere ndi wina aliyense, ndipo wina asaoneke pa mbali iliyonse ya phirilo. Nkhosa kapena ng'ombe zisadzadye pa tsinde la phirilo.”

4Motero Mose adasema ina miyala iŵiri ngati yakale ija, ndipo kutacha m'maŵa, adakwera phiri la Sinai monga momwe Chauta adamlamulira. Anali atanyamula miyala iŵiri ija.

5Tsono Chauta adatsika mu mtambo, naimirira pomwe panali iyepo, ndipo adatchula dzina lake loti Chauta.

6Eks. 20.5, 6; Num. 14.18; Deut. 5.9, 10; 7.9, 10 Adayenda pamaso pa Mose nanena mokweza kuti, “Chauta, Chauta, Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika, ndiponso wokhulupirika kwa anthu ake.

7Amaonetsa chikondi chake kwa anthu zikwi zambirimbiri, ndipo amaŵakhululukira mphulupulu zao, zoipa zao, ndi machimo ao. Koma sadzalekerera ochimwa, ndipo adzalanga ana ndi zidzukulu chifukwa cha zoipa za atate ao, mpaka mbadwo wachitatu ndi wachinai.”

8Pamenepo Mose adagwada pansi napembedza.

9Kenaka adati, “Ngati mwandikomera mtima, Inu Chauta, ndikukupemphani kuti mupite nafe. Anthuŵa ngokanika, koma Inu mutikhululukire zolakwa zathu ndi machimo athu, ndipo mutilandire ife, kuti tikhale anthu anu.”

Abwerezanso kuchita chipangano(Eks. 23.14-19; Deut. 7.1-5; 16.1-7)

10Pambuyo pake Chauta adati, “Ndidzachita nanu chipangano. Ndidzachita zozizwitsa zazikulu pamaso pa anthu ako onseŵa, zimene sizidachitikepo ndi kale lonse pa dziko lonse lapansi, pakati pa mitundu ina yonse. Anthu onse amene ali ndi iweŵa adzaona zimene Ine Chauta ndingathe kuchita, chifukwa zimene ndidzachita kudzera mwa iwe nzoopsa zedi.

11“Muzimvera malamulo amene ndakulamulani leroŵa. Ndidzapirikitsa Aamori, Akanani, Ahiti, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi.

12Musamale kuti musachite chipangano ndi anthu a ku dziko limene mukupitakolo, kuwopa kuti chingadzakhale msampha wokuchimwitsani.

13Deut. 16.21 Muzigwetsa maguwa ao, muwononge miyala yao yopatulika imene adaimiritsa, ndipo mugwetse mitengo yao yopatulika yopembedzerapo.

14Musadzapembedze mulungu wina aliyense, chifukwa Chauta amene dzina lake ndi Kansanje, ndi Mulungu wansanjedi.

15Anthu a ku dziko limenelo, musadzachite nawo chipangano, chifukwa akamadziipitsa popembedza milungu yao nkumaiphera nsembe, kapena adzakuitanani kuti mudye nao chakudya cha nsembe zaozo.

16Mwina ana anu aamuna angathenso kumadzakwatira ana ao aakazi. Tsono akazi ameneŵa akamadziipitsa potumikira milungu yao, adzakopa ana anu aamuna kuti azidzatumikiranso milungu yaoyo.

17 Eks. 20.4; Lev. 19.4; Deut. 5.8; 27.15 “Musadzipangire milungu yosungunula.

18 Eks. 12.14-20; Lev. 23.6-8; Num. 28.16-25 “Muzichita chikondwerero cha buledi wosafufumitsa monga ndidakulamulirani. Muzidzadya buledi wosafufumitsa pa masiku asanu ndi aŵiri pa mwezi wa Abibu, chifukwa ndi mwezi umenewu pamene inu mudachokako ku Ejipito kuja.

19Eks. 13.2 Mwana wamphongo aliyense woyamba kubadwa ndi wanga, pamodzi ndi wa zoŵeta yemwe, ndiye kuti ng'ombe ndi nkhosa zanu zomwe.

20Eks. 13.13 Koma muzidzaombola mwana woyamba kubadwa wa bulu, pakupereka nkhosa m'malo mwake. Mukapanda kumuwombola, muzidzamthyola khosi. Mwana aliyense wachisamba wamwamuna, muzidzachita choombola. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaonekere pamaso panga opanda kanthu kumanja kodzapereka.

21 Eks. 20.9, 10; 23.12; 31.15; 35.2; Lev. 23.3; Deut. 5.13, 14 “Muzigwira ntchito pa masiku asanu ndi limodzi, koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, musagwire ntchito iliyonse, ngakhale pa nthaŵi yolima kapena yokolola.

22Lev. 23.15-21; Num. 28.26-31; Lev. 23.39-43 Muzichita chikondwerero cha masabata, ndi chikondwerero cha kukolola tirigu woyambirira, ndi chikondwerero cha kututa zokolola zonse pakutha pake pa chaka.

23Amuna onse azibwera pamaso pa Ine Chauta, Mulungu wa Aisraele, katatu pa chaka.

24Ndidzapirikitsa mitundu inayo pamene inu mukufika, ndi kukuziriza malire a dziko lanu. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzafune kulanda dziko lanulo nthaŵi zitatuzo za pa chaka, pamene mudzadziwonetse pamaso pa Ine Chauta, Mulungu wanu.

25 Eks. 12.10 “Musapereke buledi wofufumitsa pamene mukupereka kwa Ine magazi a nsembe yanga. Nyama iliyonse yophera nsembe ya Paska, musaisunge mpaka m'maŵa.

26Deut. 26.2; Deut. 14.21 Muzibwera ndi zokolola zoyamba ndi zabwino kwambiri ku Nyumba ya Chauta, Mulungu wanu. Musaphike kamwanakanyama mu mkaka wa make.”

27Chauta adauzanso Mose kuti, “Lemba mauŵa, chifukwa potsata mau ameneŵa, ndikuchita chipangano ndi iwe ndi Aisraele onse.”

28Tsono Mose adakhala pamodzi ndi Chauta kumeneko masiku makumi anai, usana ndi usiku, osadya kanthu. Ndipo Chautayo adalemba pa miyala iŵiri ija mau onse a chipanganocho, ndiye kuti Malamulo Khumi aja.

Mose atsika kuphiri kuja

29 2Ako. 3.7-16 Pamene Mose adatsika phiri la Sinai atanyamula miyala iŵiri yaumboni ija, sadadziŵe kuti nkhope yake njoŵala chifukwa cholankhula ndi Chauta.

30Aroni ndi anthu onse aja atayang'ana Mose, adaona kuti nkhope yake njoŵala. Ndipo adachita mantha osafuna kumuyandikira.

31Koma Mose adaŵaitana, ndipo Aroni pamodzi ndi atsogoleri a Aisraele aja atabwera kwa iye, Moseyo adayamba kulankhula nawo.

32Pambuyo pake Aisraele onse adasendera pafupi, ndipo Mose adaŵapatsa malamulo onse amene Chauta adaamuuza ku phiri la Sinai lija.

33Mose atamaliza kulankhula nawo, adadziphimba kumaso.

34Nthaŵi zonse Moseyo ankati akaloŵa m'chihema kukalankhula ndi Chauta, ankachotsa nsalu yophimba kumaso ija mpaka atatuluka. Tsono atatuluka, ankauza Aisraele aja zonse zimene Chauta wamulamula kuti anene.

35Ndipo anthuwo ankaona kuti nkhope yake njoŵala, koma Moseyo ankadziphimbanso kumaso mpaka nthaŵi ina yakuti apitenso kukalankhula ndi Chauta.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help