Daniel Greek 7 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Daniele aona zinthu m'masomphenya

1Chaka choyamba cha ufumu wa Belisazara wa ku Babiloni, Daniele atagona pabedi pake adalota maloto ndipo adaona zinthu kutuloko. Tsono adalemba malotowo, mwachidule adanena kuti:

2Ine Daniele ndidaona zinthu kutulo usiku. Ndidaona nyanja yaikulu, itavunduka ndi mphepo zinai zamumlengalenga.

3M'nyanjamo mudatuluka zilombo zinai zikuluzikulu zosiyanasiyana.

4Choyamba chinali ngati mkango, koma cha mapiko ngati a chiwombankhanga. Ine ndikuyang'ana, mapiko ake adakadzuka, ndipo chilombocho adachinyamula nachiimiritsa pa mapazi aŵiri ngati munthu. Adachipatsa nzeru zonga za munthu.

5Kenaka ndidaona chilombo china chachiŵiri, chonga chimbalangondo. Chinali chonyamuka kumodziku, m'kamwa mwake munali nthiti zitatu pakati pa manoŵa. Ndipo adachilamula kuti, “Dzuka, udye nyama yambiri.”

6Pambuyo pake ine ndikuyang'ana, ndidaona chilombo china chonga kambuku, chili ndi mapiko anai ambalame pamsana pake. Chilombo chimenechi chinali ndi mitu inai, ndipo adachipatsa mphamvu zolamulira.

7Nditaona zimenezi kutuloko usiku, ndidaonanso chilombo chachinai chochititsa mantha, choopsa kwambiri, ndiponso champhamvu kwabasi. Chinali ndi mano aakulu achitsulo. Chinkati chikapwepweta, nkudya, kenaka nkumapondereza zonse zotsala. Chinkasiyana ndi zilombo zonse zoyamba zija, popeza kuti chinali ndi nyanga khumi.

8Pamene ndinkaganiza za nyangazo, ndidaona kuti nyanga ina yaing'ono ikumera pakati pa nyangazo. Nyanga zitatu mwa zoyamba zija adazizula, kuti inayo ipeze mpata. Pa nyanga imeneyi panali maso onga a munthu ndiponso pakamwa, pamene pankalankhula zodzitama.

Daniele aona Mkulu uja amene analipo chikhalire

9Ine ndikuyang'ana,

ndidaona mipando yaufumu ikuikidwa pa malowo,

ndipo Mkulu amene analipo chikhalire

adakhala pa mpando umodzi.

Zovala zake zinali zambee ngati chipale,

ndipo tsitsi lake linali loyera ngati ubweya wa nkhosa.

Mpando wake unali wonga wa malaŵi a moto,

mikombero yake ngati moto woyaka.

10Mtsinje wa moto udatuluka nkumayenda patsogolo pake.

Panali chinamtindi cha anthu omtumikira,

panalinso chinamtindi china chochuluka kupambana chinacho.

Chimenechi chidaima pamaso pake.

Tsono bwalo lidayamba kuweruza,

ndipo mabuku adatsekulidwa.

11Ndidayang'anitsitsa chifukwa cha mau onyada amene nyanga ija inkalankhula. Ndikuyang'ana choncho, chilombocho chidaphedwa, ndipo mtembo wake udaonongedwa nkuponyedwa pa moto.

12Zilombo zina zotsala, ngakhale adazilanda mphamvu zolamulira, adazilola kukhala ndi moyo pa kanthaŵi.

13Pamene ndinkaonabe zinthu m'masomphenya usiku,

ndidaona wina ngati mwana wa munthu

akutsika ndi mitambo yakumwamba.

Atayandikira Mkulu amene analipo chikhalire uja,

ena adamperekeza kwa Mkuluyo.

14Pamenepo adampatsa ulamuliro, ulemerero ndi ufumu,

kuti anthu a mitundu yonse, a mafuko onse

ndi a zilankhulo zosiyanasiyana azimtumikira.

Ulamuliro wake ndi wamuyaya, sudzatha.

Ufumu wake ndi wosagaŵikana,

ndipo sudzaonongedwa.

Amasulira zinthu zoziwona m'masomphenya zija

15Ine Daniele, ndidavutika mumtima mwanga, ndipo zimene ndidaziwona m'masomphenya zidandichititsa mantha.

16Ndidapita kwa mmodzi mwa amene adaaima pamenepo ndipo ndidampempha kuti andifotokozere tanthauzo la zimenezi. Motero adandikambira nandifotokozera tanthauzo lake.

17Adati “Zilombo zinai zazikulu zija ndi mafumu anai amene adzaoneka pa dziko lapansi.

18Koma oyera mtima a Mulungu Wopambanazonse adzalandira mphamvu za ufumu, ndipo adzakhala nazo mpaka muyaya, nthaŵi zosatha.”

19Tsono ndidafuna kudziŵa tanthauzo lake la chilombo chachinai chija, chimene chinali chosiyana ndi zinzake zonse, choopsa kwambiri, cha mano achitsulo ndi zikhadabo zamkuŵa, chimene chinkati chikapwepweta, nkudya, nkupondereza zotsala zonse ndi mapazi ake.

20Ndidafunanso kudziŵa tanthauzo lake la nyanga khumi za pamutu pake zija, ndiponso za nyanga ina ija imene idaaphuka nigwetsa zitatu zija pophukapo. Imeneyi ndi nyanga ija imene inali ndi maso ndi pakamwa polankhula zinthu zonyada, ndipo inkaoneka yaikulu kupambana zina zonse.

21Ine ndikuyang'ana, nyanga imeneyo idachita nkhondo ndi anthu oyera mtima, ndipo idaŵapambana,

22mpaka pamene mkulu amene analipo chikhalire uja adafika. Tsono chiweruzo chidakomera oyera mtima a Mulungu Wopambanazonse. Pamenepo nthaŵi idakwana pamene oyera mtimawo adalandira ufumu.

23Tsono adandiyankha kuti,

“Chilombo chachinaicho chikusonyeza ufumu wachinai

umene udzaoneka pa dziko lapansi.

Udzasiyana ndi maufumu ena,

ndipo udzagonjetsa dziko lonse lapansi.

Udzalipondereza ndi kuliphwanya pafupipafupi.

24Nyanga khumi zina zikusonyeza mafumu khumi

amene adzatuluka mu ufumu umenewu.

Pambuyo pake padzabwera mfumu ina

yosiyana ndi mafumu ena akale.

Imeneyo idzagonjetsa mafumu atatu.

25Idzalankhula mau otsutsana ndi Mulungu Mphambe,

ndipo idzazunza opembedza Mulunguyo.

Idzayesetsa kusintha masiku achikondwerero

ndi malamulo a chipembedzo.

Ndipo oyera mtima aja adzalamulidwa ndi mfumu imeneyi

pa zaka zitatu ndi theka.

26Koma a pa bwalo lamilandu adzaiweruza,

ndipo adzailanda ulamuliro wake

kuti potsiriza pake uwonongeke ndi kutheratu.

27Ufumu, ulamuliro,

ndi ukulu wa maufumu onse pansi pa thambo zidzaperekedwa

kwa mpingo wa oyera mtima a Mulungu Wopambanazonse.

Ufumu wao udzakhala wamuyaya,

olamulira onse a dziko lapansi

azidzaŵatumikira ndi kuŵamvera.”

28Zinthu zathera pano.

Koma ine Daniele maganizo angawo andiwopsa,

ndipo nkhope yanga idatumbuluka,

koma ndinkakumbukira ndithu zimenezi mumtima mwanga.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help