1Nawu ulosi wonena za chipululu
cha m'mbali mwa nyanja.
Tsoka lidzafika kuchokera ku dziko lochititsa mantha
monga m'mene kamvulumvulu amakunthira
kuchokera ku chipululu.
2Ndaona zinthu zoopsa m'masomphenya:
wofunkha akufunkha,
woononga akuwononga.
Ankhondo a ku Elamu, yambani nkhondo!
Ankhondo a ku Mediya, zingani mzindawo.
Ine Chauta ndidzathetsa mavuto onse
amene adadza ndi Babiloni.
3Nchifukwa chake zimene ndidazimva ndi
kuziwona m'masomphenya zija zandichititsa mantha,
ndipo ndamva nazo ululu ngati mkazi amene akuchira.
Ndikuvutika nazo zimene ndilikumva.
Ndikuda nazo nkhaŵa zimene ndikuwonazi.
4Mtima wanga ukugunda,
ndipo ndikunjenjemera ndi mantha.
Ndakhala ndikulakalaka chisisira,
koma chisisiracho chandibweretsera zoopsa.
5Iwo akukonza tebulo ndi kuyala mphasa,
alikudya, alikumwa.
Mwadzidzidzi alikumva mau akuti,
Dzukani inu ankhondo,
pakani mafuta zishango zanu!
6Pakuti Ambuye andiwuza kuti,
“Pita, kaike mlonda
kuti azinena zimene akuwona.
7Akamaona anthu aŵiriaŵiri okwera pa akavalo,
okwera pa abulu ndi okwera pa ngamira,
mlondayo akhale tcheru, tcherutu zedi!”
8Apo mlondayo adafuula kuti,
“Ambuye, usana wonse ndimakhala pa nsanja,
usiku wonse ndimakhala pa malo anga olondera.
9 Chiv. 14.8; 18.2 Ndidangoona kukubwera anthu okwera pa akavalo,
akuyenda aŵiriaŵiri.
Mmodzi mwa iwo adati,
‘Ii, wagwa, wagwatu uku Babiloni!
Mafano onse a milungu yake
aphwanyikira pansi.’ ”
10Ndiye abale anga Aisraele,
inu opunthidwa ndi opetedwa ngati tirigu,
tsopano ndakuuzani uthenga
umene ndamva kwa Chauta Wamphamvuzonse,
Mulungu wa Israele.
Ulosi wonena za Edomu11Nawu ulosi wonena za Edomu:
Wina akundilankhula mofuula
kuchokera ku Edomu, akuti,
“Iwe mlonda, usikuwu utha liti?
Iwe mlonda, utha liti kodi usikuwu?”
12Mlonda akuti, “Kulikucha, koma kudanso.
Ukafuna kufunsanso, ubwerenso udzafunse.”
Ulosi wonena za Arabiya13Nawu ulosi wonena za Arabiya:
Inu anthu a ku Dedani oyenda pa gulu,
amene usiku mumagona m'malunje a ku Arabiya,
14muŵapatse madzi anthu aludzu kuti amwe.
Inu anthu a ku Tema,
muŵapatse chakudya anthu othaŵa nkhondo.
15Pakuti akuthaŵa malupanga,
malupanga osololasolola,
mauta okokakoka,
ndiponso nkhondo yoopsa.
16Ambuye adandiwuza kuti, “Chatsala chaka chimodzi, potsata m'mene amaŵerengera munthu waganyu, ndipo ulemu wonse wa anthu a ku Kedara udzatheratu.
17Mwa anthu onse amphamvu a ku Kedara okoka mauta, opulumuka adzakhala oŵerengeka.” Chauta, Mulungu wa Israele, watero.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.