Deut. 7 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Anthu ake a Chauta(Eks. 34.11-16)

1 Ntc. 13.19 Chauta, Mulungu wanu, adzakufikitsani m'dziko limene mukudzakhalamolo, ndipo mitundu ina yonse ya anthu adzaipirikitsa m'dzikomo. Iye adzachotsamo mitundu isanu ndi iŵiri ya anthu otchuka ndi amphamvu kupambana inu. Mitunduyo ndi iyi: Ahiti, Agirigasi, Aamori, Akanani, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi.

2Chauta, Mulungu wanu, akadzapereka anthu ameneŵa kwa inu ndipo mukadzaŵagonjetsa, mudzaŵaononge onsewo. Musakayanjane nawo, kapena kuŵachitira chifundo.

3Musakakwatirane nawo, ndiye kuti musakalole ana anu kukwatirana nawo,

4kuti angadzaŵasokeretse kuŵachotsa kwa Chauta, Mulungu wanu, namakapembedza nawo milungu ina. Mukadzatero, Chauta adzakukwiyirani, ndipo adzakuwonongani mwamsanga.

5Deut. 12.3 Anthu amenewo mudzaŵachite izi: mudzaphwanye maguwa ao, mudzaphwanye miyala yoimiritsa yopembedzapo, mudzagwetse mafano ao aja a Aserimu, ndipo mudzatenthe mafano ao osema.

6 Eks. 19.5; Deut. 4.20; 14.2; 26.18; Tit. 2.14; 1Pet. 2.9 Inu ndinu mtundu wopatulika wa Chauta, Mulungu wanu. Mulungu adasankha inu kuti mukhale anthu ake pakati pa anthu onse a pa dziko lapansi.

7Mulungu pokukondani ndi kukusankhani inu, sadachitire kuti munkaposa anthu ena onse pakuchuluka. Paja mudaali ochepa ndinuyo pakati pa mitundu yonse.

8Koma Chauta adakukondani, ndipo adafunadi kusunga malumbiro amene adaachita ndi makolo anu. Nchifukwa chake adakupulumutsani ndi mphamvu zake, nakusandutsani mfulu, kukuchotsani m'dziko laukapolo kwa mfumu ya ku Ejipito ija.

9Eks. 20.5, 6; 34.6, 7; Num. 14.18; Deut. 5.9, 10 Nchifukwa chake mudziŵe kuti Chauta, Mulungu wanu, ndiye yekha Mulungu, ndipo ndi Mulungu wokhulupirika. Iye adzasungadi chipangano chake ndipo adzaonetsa chifundo chake chosasinthika kwa anthu a mibadwo zikwi zambirimbiri amene amakonda Iye namamvera malamulo ake.

10Koma onse amene amadana ndi Mulungu, adzaŵabwezera pakuŵaononga. Sadzamlekerera munthu wodana naye, koma adzamubwezera pakumlanga ndithu.

11Motero, muzimvera mosamala malangizo ndi malamulo amene ndikukulamulani leroŵa.

Madalitso chifukwa cha kumvera(Deut. 28.1-14)

12 Deut. 11.13-17 Ngati mumvera ndi kutsata mokhulupirika malamulo onse mwamvaŵa, Chauta, Mulungu wanu, adzapitirirabe kusunga chipangano chake chimene adachita ndi inu, ndipo adzapitiriranso kukukondani, monga momwe adalonjezera makolo anu.

13Adzakukondani ndi kukudalitsani, kotero kuti mudzachuluka ndi kubereka ana ambiri. Minda yanu adzaidalitsa, kotero kuti tirigu, vinyo ndi mafuta, mudzakhala nazo zonsezo. Adzakudalitsaninso pa zoŵeta pokupatsani ng'ombe zambiri ndi zoŵeta zina zomwe. Madalitso onseŵa, adzakupatsani muli m'dziko limene adalonjeza makolo anu.

14Pa dziko lapansi, palibe anthu amene adzakhale odala ngati inu. Sipadzaoneka mwamuna kapena mkazi wosabala pakati panu, ndiponso pakati pa zoŵeta zanu.

15Chauta adzakutchinjirizani pa matenda onse. Iye sadzalolanso kuti matenda oopsa a ku Ejipito amene mumaŵadziŵa aja, afikenso pa inu, koma Mulungu adzadzetsa matenda ameneŵa pa adani anu onse.

16Mitundu yonse imene Chauta, Mulungu wanu, aipereke kwa inu, muiwononge mopanda chifundo. Musapembedze milungu yao, popeza kuti kuteroko nkugwa mu msampha.

17Musanene kuti anthu ameneŵa achuluka kupambana inu, ndipo kuti simungathe kuŵapirikitsa.

18Musaŵaope. Kumbukirani zimene Chauta, Mulungu wanu, adam'chita Farao mfumu ya ku Ejipito, pamodzi ndi anthu ake omwe.

19Kumbukirani miliri yoopsa ija imene mudaiwona ndi maso anu. Mudaona zozizwitsa ndi zodabwitsa zomwe, ndiponso zinthu zazikulu zamphamvu. Zimenezi Chauta, Mulungu wanu, adazichita ndi dzanja lake lamphamvu, kuti akumasuleni. Anthu onse amene mumaŵaopaŵa, Chauta Mulungu wanu adzaŵaononga monga momwe adaonongera Aejipito.

20Ndiponsotu adzatumiza mliri wa mavu pakati pao, umene udzaononga onse othaŵa ndi obisala.

21Musaŵaope anthu ameneŵa. Chauta Mulungu wanu ali nanu. Iyeyo ndiye Mulungu wamkulu woyeneradi kumuwopa.

22Inu mukamayenda, Iye adzapirikitsa mitundu imeneyi pang'onopang'ono. Komatu simudzaŵatha onse nthaŵi imodzi. Mukadatero, nyama zakuthengo zikadachuluka ndi kumakuwopsani.

23Chauta adzapereka adani anuwo kwa inu, ndipo adzaŵasokoneza kwambiri mpaka atatha onse.

24Mafumu onse adzaŵapereka kwa inu. Mudzaŵapha onse, ndipo adzaiŵalika. Palibe amene adzakuletseni, mpaka mudzaŵaononga onsewo.

25Mudzatenthe mafano ao ofanizira milungu yao. Musadzakhumbire siliva kapena golide amene iwo adapangira mafanowo. Musadzatengeko zimenezi kuti mungagwe mu msampha, popeza kuti zimenezo zimamnyansa Chauta, Mulungu wanu.

26Musadzaloŵe nazo m'nyumba mwanu zimenezi, kuti tsoka limene lili pa iwowo lingadzakhale pa inu. Mudzadane ndi mafanowo ndi kuŵanyoza, chifukwa Chauta adaŵatemberera.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help