1Tsono mnyamata uja Tobiyasi adanyamuka pamodzi ndi mngelo, ndipo galu wake adapita nao. Adayenda limodzi onse aŵiri, ndipo pamene usiku udagwa, adagona pafupi ndi mtsinje wa Tigrisi.
2Mnyamatayo adatsikira kumtsinjeko kuti akasambe m'miyendo. Chinsomba chidalumpha nkutuluka m'madzi, kufuna kumeza phazi lake. Mnyamatayo adakuwa.
3Mngelo uja adamuuza kuti, “Igwire nsombayo, igwiritse!” Mnyamatayo adaigwira nsombayo, nkuikokera ku mtunda.
4Apo mngeloyo adati, “Itumbule nsombayi, uchotse ndulu, mtima ndi chiŵindi, ndipo uzisunge bwino. Koma matumbo ake utaye. Nduluyi, mtimawu ndi chiŵindichi, ndi mankhwala othandiza kwambiri.”
5Tsono mnyamatayo adatumbula nsomba ija. Adatulutsa ndulu, mtima ndi chiŵindi chija, kuti azisunge. Kenaka adaotcha nsombayo, naadya, zotsala nkuziika mu mchere.
6Pambuyo pake aŵiriwo adayenda limodzi mpaka kukafika pafupi ndi dziko la Mediya.
7Tsono mnyamatayo adafunsa mngelo uja kuti, “Azariyasi, mbale wanga, kodi m'ndulu, mu mtima ndi m'chiŵindi cha nsomba, muli mankhwala otani?”
8Iye adayankha kuti, “Ukaotcha mtima ndi chiŵindi pamaso pa munthu wamwamuna kapena wamkazi amene akusautsidwa ndi demoni kapena mzimu wina woipa, utsi wake udzapirikitsa mizimuyo, ndipo sidzamvutanso munthuyo.
9Koma ndulu ukadzozera maso a munthu wakhungu, nkuuzira m'masomo, khungulo limatha.”
Mngelo uja alankhula ndi Tobiyasi zoti akwatire Sara10Pamene adaloŵa ku Mediya ndi kufika pafupi ndi Ekibatana,
11Rafaele adati, “Tobiyasi mbale wanga.” Iye adayankha kuti, “Ee, ndilikumva.” Mngeloyo adati, “Usiku walero, tikagone m'nyumba mwa Raguele.
12Munthuyo ndi iweyo muli pa chibale, ndipo ali ndi mwana wamkazi, dzina lake Sara. Alibe mwana wina, wamwamuna kapena wamkazi, koma Sara yekhayo. Mtsikanayo ndi msuweni wako, ndipo ndiwe amene uyenera kumtenga kuti akhale mkazi wako. Uyeneranso kuloŵa chuma chake chimene bambo wake adzamsiyira. Namwaliyo ndi wanzeru, wa mtima wolimba ndiponso wokongola kwambiri. Bambo wake ndi munthu wabwino.
13Ukuyeneradi kumkwatira namwaliyo. Imva mbale wanga, usiku uno ndikamba nawo bambo wake za namwaliyo, kuti umufunsire mbeta. Tsono titabwerako ku Ragesi, tidzachita phwando laukwati. Ndikudziŵa kuti Raguele sangathe kukukaniza kapena kukwatitsa mwana wake kwa wina. Atatero, angathe kuwona mlandu woyenera kuphedwa nawo, monga zidalembedwera m'buku la Mose. Iye uja akudziŵa kuti woyenera ndithu kukwatira mwana wakeyo ndiwe, osati winanso ai. Choncho undimvere, mbale wanga, usiku uno tikambe za namwaliyo ndipo umufunsira mbeta. Tsono pobwerako ku Ragesi kuja, tidzamtenga kuti adzapite nafe kunyumba kwanu.”
14Koma Tobiyasi adayankha Rafaele kuti, “Iwe Azariyasi, mbale wanga, ndidamva kuti mkaziyu adaakwatiwapo ndi amuna asanu ndi aŵiri, koma aliyense adafa usiku womwe woloŵanawo. Ankati akafuna kuti akhale naye, ankafa. Ndamva kuti ndi demoni amene ankaŵapha.
15Demoniyo samuchita kanthu Sarayo, koma amangopha okhaokha ofuna kukhala nayewo. Ndiye ine ndikuwopa kufa. Tsono poti paja atate adangobereka ine ndekha, ndikuwopa kuti iwowo ndi amai anga angadzafe ndi chisoni. Ndipo alibe mwana wina woti nkudzaŵaika m'manda.”
16Rafaele adati, “Kodi sukukumbukira malangizo a bambo wako? Suja adakulamula kutenga mkazi m'fuko la atate ako? Undimvere tsopano, mbale wanga. Usavutike nazo za demoni woipayo, umkwatire ndithu mkaziyo. Ine ndikudziŵa kuti usiku walero adzampereka kwa iwe kuti akhale mkazi wako.
17Poloŵa m'nyumba yogona, utenge chiŵindi cha nsomba chija pamodzi ndi mtima wake, uziike pa moto walubani. Fungo lake lidzakwanira ponseponse. Pamenepo demoniyo adzalimva nathaŵa, osadzamuyandikiranso namwaliyo.
18Tsono musayambe nkugona pamodzi. Nonse aŵiri muyambe mwaima nkupemphera. Mupemphe Ambuye akumwamba kuti akukomereni mtima ndi kukutchinjirizani. Usachite mantha, Mulungu adamsunga mpoyamba pomwe kuti adzakhale wako, ndipo iweyo udzamupulumutsa. Adzapita nawe, ndipo ndikukutsimikizira kuti adzakubalira ana amene adzakhala ngati abale ako. Choncho usakayike ai.”
M'mene Tobiyasi adamva Rafaele akunena zimenezi, atadziŵa kuti Sara anali msuweni wake, pa chibale ndi banja la bambo wake, adamkonda kwambiri, kotero kuti mtima wake sadathenso kuugwira.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.