1 Maf. 18 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Eliya ndi Obadiya

1Patapita nthaŵi yaitali, pa chaka chachitatu cha chilala, Chauta adauza Eliya kuti, “Pita ukadziwonetse kwa Ahabu. Ndidzagwetsa mvula pa dziko lapansi.”

2Motero Eliya adapita kukadziwonetsa kwa Ahabu. Pamenepo nkuti njala itafika pake penipeni ku Samariya.

3Mfumu Ahabu adaitana Obadiya, amene ankayang'anira zonse za ku nyumba yachifumu. (Ndiye kuti Obadiya ankatumikira Chauta.

4Ndipo pamene Yezebele ankapha aneneri a Chauta, Obadiya adaabisa aneneri 100. Aneneri 50 adaŵabisa m'phanga lina, 50 ena m'phanga linanso, namaŵapatsa chakudya ndi madzi.)

5Tsono Ahabu adauza Obadiya kuti, “Tiye tiyendere dziko lonse, tiwone akasupe onse a madzi, ndiponso tipite ku zigwa zonse. Mwina mwake tingapeze udzu womadyetsa akavalo ndi abulu kuti akhale moyo.”

6Choncho Ahabu ndi Obadiya adagaŵana dzikolo kuti aliyendere. Ahabu adapita mbali ina, Obadiya mbali inanso.

7Pamene Obadiya ankapita pa ulendo wake, adangoona mneneri Eliya akubwera kudzakumana naye. Obadiya adamzindikira Eliyayo, ndipo adamuŵeramira, namufunsa kuti, “Kodi ndinudi mbuyanga Eliya?”

8Eliya adayankha kuti, “Ndine amene. Pita ukauze mbuyako kuti Eliya wabwera.”

9Obadiya adamufunsa kuti, “Kodi ndachimwa chiyani kuti inu mundipereke ine mtumiki wanu m'manja mwa Ahabu kuti andiphe?

10Pali Chauta, Mulungu wanu wamoyo, kulibe mtundu wa anthu kapena ufumu uliwonse kumene mbuyanga Ahabu sadatumeko anthu okakufunafunani. Anthu akamuuza kuti, ‘Eliya kulibe kuno,’ Ahabu ankaŵalumbiritsa anthuwo kuti atsimikizedi ngati inu kunalibe kumeneko.

11Ndiye ine mukuti ndipite ndikamuuze mbuyanga kuti mwabwera?

12Mwina ine ndikangochoka pano, pompo mzimu wa Chauta ukuchotsani kuno kunka nanu komwe ine sindidziŵa. Tsono ndikakamuuza Ahabu, iye osadzakupezani, adzandipha, ngakhale kuti mtumiki wanune ndakhala ndikutumikira Chauta kuyambira ubwana wanga.

13Kodi inu mbuyanga simudamve zoti nthaŵi imene Yezebele ankapha aneneri a Chauta, ine ndidabisa aneneri 100 a Chauta, anthu 50 m'phanga limodzi, 50 ena m'phanga lina, ndipo kuti ndinkaŵadyetsa chakudya ndi kumaŵapatsa madzi akumwa?

14Ndiye inu mukuti, ‘Pita, kamuuze mbuyako kuti, “Eliya wabwera?” ’ Ndithu iyeyo adzandipha ine!”

15Koma Eliya adati, “Ndithudi, pali Chauta Wamphamvuzonse amene ndimamtumikira, ine lero ndikukaonekera pamaso pa Ahabu.”

16Motero Obadiya adapita kwa Ahabu kukamuuza za Eliyayo. Ndipo Ahabu adapita kukakumana ndi Eliya.

Eliya ndi Ahabu

17Tsono Ahabu ataona Eliya, adamuuza kuti, “Ha, iwe munthu wovuta anthu a ku Israele, wabweradi?”

18Eliya adayankha kuti, “Ameneyo sindine ai. Koma inuyo pamodzi ndi banja la bambo wanu, ndiye mwakhala mukuvuta anthu a ku Israele, chifukwa mwasiya malamulo a Chauta nkumatsata Abaala.

19Nchifukwa chake tsopano tumizani mau kuti musonkhanitse onse a ku Israele, kuti abwere, ndikakumane nawo ku Phiri la Karimele. Abwere ndi aneneri a Baala 450, ndiponso aneneri a fano la Asera 400, amene amadya kwa Yezebele.”

Eliya ndi aneneri a Baala

20Pamenepo Ahabu adatumiza mau kwa onse a ku Israele, ndipo adasonkhanitsa aneneri a Baala ku Phiri la Karimele.

21Eliya adasendera pafupi ndi anthu onsewo, naŵafunsa kuti, “Kodi mudzakhala anthu a mitima iŵiri mpaka liti? Ngati Chauta ndiye Mulungu, mtsateni. Koma ngati Baala ndiye Mulungu, tsatani iyeyo.” Anthuwo sadamuyankhe ndi liwu limodzi lomwe.

22Tsono Eliya adauza anthu aja kuti, “Ine ndatsala ndekha mwa aneneri a Chauta, koma aneneri a Baala alipo 450 pamodzi.

23Bwerani ndi ng'ombe zamphongo ziŵiri. Iwo asankhepo okha ng'ombe imodzi ndipo aidule nthulinthuli ndi kuziika pa nkhuni nthulizo, koma asasonkhepo moto ai. Inenso ndidula ng'ombe inayo nthulinthuli, ndi kuikanso nthulizo pa nkhuni, koma osasonkhapo moto ai.

24Inu mutame dzina la mulungu wanu mopemba, inenso nditana dzina la Chauta mopemba. Tsono Mulungu amene ayankhe potumiza moto, ameneyo ndiyedi Mulungu.” Pamenepo anthu onsewo adati, “Ai, mwanena bwino.”

25Tsono Eliya adauza aneneri a Baala aja kuti, “Yambani ndinu. Sankhulani ng'ombe yamphongo imodzi, muikonze, poti mwachuluka. Tsono mutame dzina la mulungu wanu mopemba, koma musasonkhe moto ai.”

26Iwowo adatenga ng'ombe yamphongo imene adaŵapatsa, naipha. Tsono adatama dzina la Baala mopemba, kuyambira m'maŵa mpaka masana, ponena kuti, “Inu a Baala, tiyankheni ife.” Aneneri a Baala aja ankalumphalumpha movina, kuzungulira guwa limene adaamangalo, koma sipadamveke ndi liwu lomwe, panalibe woyankha.

27Tsono nthaŵi yamasana ndithu Eliya adayamba kuŵaseka, naŵauza kuti, “Fuulani kwambiri, suja mukuti iyeyo ndi mulungu! Mwina mwaketu watanganidwa, kapena wapita kwina kukadzithandiza, kapena ali pa ulendo, kaya kapena ali m'tulo, ndiye kamdzutsenitu.”

28Aneneri a Baalawo ankafuula kwambiri, nadzichekacheka ndi malupanga ndi mipeni potsata miyambo yao, mpaka magazi chuchuchu m'mabalawo.

29Dzuŵa litapendeka, adakhala akufuulabe mopenga kufikira nthaŵi yoperekera nsembe idakwana. Komabe kunali zii! Osamveka ndi liwu lomwe. Panalibe woyankha, panalibe ndi mmodzi yemwe wosamalako zimenezo.

30Pamenepo Eliya adauza anthu onse aja kuti, “Senderani pafupi ndi ine.” Anthu onsewo adasenderadi kwa iyeyo. Tsono Eliya adakonza guwa la Chauta limene linali litagwetsedwa.

31Gen. 32.28; 35.10 Adatenga miyala khumi ndi iŵiri potsata chiŵerengero cha mafuko a ana a Yakobe amene Chauta adaamuuza kuti dzina lake lidzakhala Israele.

32Ndi miyalayo adamangira guwa lotamandirapo Chauta. Tsono adakumba ngalande kuzungulira guwalo. Kukula kwa ngalandeyo kunali ngati moloŵa mitsuko inai ya madzi.

33Adaika nkhuni zija m'malo mwake, nadula ng'ombe ija nthulinthuli, nkuika nthulizo pankhunipo. Pambuyo pake adauza anthu kuti, “Dzazani mitsuko inai ndi madzi, muŵathire pa nyama yansembeyo, ndi pa nkhunizo.”

34Ndipo adaŵauza kuti, “Bwerezaninso kachiŵiri.” Anthu aja adathiranso madziwo kachiŵiri. Adaŵauzanso kuti, “Thiraninso kachitatu,” nateronso kachitatu.

35Madziwo adayenderera kuzungulira guwalo, nadzaza ngalande yonse.

36Itakwana nthaŵi yake yopereka nsembe, mneneri Eliya adasendera pafupi ndi guwa nati, “Inu Chauta, Mulungu wa Abrahamu, Isaki ndi Israele, lero zidziŵike kuti Inuyo ndiye Mulungu m'dziko la Israele, ndipo kuti ine ndine mtumiki wanu, ndiponso kuti ndachita zonsezi chifukwa mwanena ndinu.

37Mundiyankhe, Inu Chauta, mundiyankhe, kuti anthu aŵa adziŵe kuti Inu Chauta ndinu Mulungu, ndipo kuti atembenuke mtima.”

38Pomwepo moto wa Chauta udagwa, nunyeketsa nsembe yopserezayo, nkhunizo, miyala ija ndi dothi lomwe. Motowo udaphwetsa ndi madzi omwe amene anali m'ngalande aja.

39Tsono anthu onse ataona zimenezo, adadzigwetsa pansi nanena mokweza kuti, “Chauta ndiyedi Mulungu! Chauta ndiyedi Mulungu!”

40Pamenepo Eliya adaŵauza kuti, “Gwirani aneneri onse a Baala. Asapulumukepo ndi mmodzi yemwe.” Motero adaŵagwira onsewo. Ndipo Eliya adatsikira nawo ku mtsinje wa Kisoni, nakaŵaphera kumeneko.

Kutha kwa chilala chija

41Pambuyo pake Eliya adauza Ahabu kuti, “Pitani mukadye ndi kumwa, pakuti kukumveka mkokomo wa mvula.”

42Yak. 5.18 Motero Ahabu adapita kukachita madyerero. Koma Eliya adakwera pamwamba pa Phiri la Karimele, ndipo adazyolikira pansi naika mutu wake pakati pa maondo ake.

43Tsono adauza mtumiki wake kuti, “Pita ukayang'ane ku nyanja.” Mtumikiyo adapita kukayang'ana, nati, “Kulibe kanthu.” Eliya adamuuza kuti, “Pitanso kasanunkaŵiri.”

44Mtumikiyo atapita kachisanu ndi chiŵiri adati, “Pali kamtambo kakang'ono konga dzanja la munthu, kakutuluka kunyanjako.” Pompo Eliya adati, “Pita kamuuze Ahabu kuti akonze galeta lake, ndipo azipita, kuti mvula ingamtsekereze.”

45Posachedwa kuthambo kudangoti bii ndi mitambo, mphepo idaomba ndipo padagwa mvula yaikulu. Ahabu adakwera galeta napita ku Yezireele.

46Mphamvu za Chauta zinali naye Eliya. Iyeyo adakwinda chovala chake, nathamanga mwaliŵiro, nkupitirira Ahabu mpaka adayambira ndiye kukafika ku chipata cha ku Yezireele.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help