Yud. 15 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Aisraele apambana pa nkhondo

1Ankhondo atamva mbiri imeneyo ku zithando zao, adasokonezeka chifukwa cha zimene zidachitikazo.

2Onse adamwazikana ali ndi mantha aakulu, osasamalanso zokhala pamodzi, ndipo adathaŵira m'njira zosiyanasiyana kubzola zigwa ndi dziko la mapiri.

3Amene ankakhala pafupi ndi Betuliya nawonso adathaŵa. Tsono ankhondo onse a ku Israele otha kumenya nkhondo, adaŵathamangitsa.

4Uziya adatuma anthu ku Betomesitaimu, ku Bebai, ku Khoba, ndi ku Kola, ndi ku dziko lonse la Israele, kuti akalengeze zimene zidachitika nkuŵauza kuti akathamangitse adaniwo ndi kuŵaononga.

5Atamva mbiri imeneyo, aliyense wa ku Israele adakamenyana ndi Aasiriya naŵakantha mpaka ku Khoba. Anthu a ku Yerusalemu ndi a ku maiko onse amapiri nawonso adamenya nawo nkhondo, poti adaaŵauza zimene zidachitika ku zithando za adani. Anthu a ku Giliyadi ndi a ku Galileya adaŵatsekereza njira Aasiriyawo, naŵapha ambiri, mpaka kupitirira ku Damasiko ndi dziko lake lonse.

6Anthu onse a ku Betuliya adaloŵa m'zithando za Aasiriya nkuyamba kufunkha zinthu zao zonse.

7Aisraele atabwerako ku nkhondo, adatenga zimene zidatsala. Ngakhale mizinda ndi midzi yakumapiri ndi yakuzigwa idafunkha nao, poti zinthu zinali zambiri.

Aisraele athokoza chifukwa cha kupambana pa nkhondo

8Yowakimu, mkulu wa ansembe, pamodzi ndi bungwe lapamwamba la Israele, adabwera kuchokera ku Yerusalemu, kuti akadziwonere okha zazikulu zimene Ambuye anali atachitira anthu ao, kutinso adzakumane ndi Yuditi ndi kumlonjera.

9Atakumana naye, onse ndi mau amodzi omtamanda adati, “Inu ndinu ulemerero wa Yerusalemu, ndinu chisangalalo cha Israele, ndinu chinyado chachikulu cha mtundu wathu.

10Mwachita zonsezi nokha ndi dzanja lanu. Mwachitira Israele zabwino zazikulu, ndipo Mulungu zamkomera. Ambuye amphamvuzonse akudalitseni pa moyo wanu wonse.” Apo anthu onse adayankha kuti, “Inde momwemo!”

11Choncho anthu adafunkha zinthu za Aasiriyazo mwezi wathunthu. Adampatsa Yuditi hema la Holofernesi pamodzi ndi mbale zake zonse zasiliva, mipando yake, mbiya zake ndi zonse za m'nyumba mwake. Yuditi atalandira zimenezo, adasenzetsa nyulu yake, natenganso ngolo zake nkuikapo katundu.

12Akazi onse a ku Israele adasonkhana kuti amuwone. Adamuimbira nyimbo zomtamanda, ena mwa iwo nkumamuvinira. Iye adatenga nthambi zamaluŵa m'manja mwake, nkupatsako anzake amene anali nawo.

13Yuditi pamodzi ndi anzakewo adavala nsangamutu za masamba aolivi kumutu. Iye adatsogolera akazi onse aja kuvina, anthu onse akuwona. Tsono amuna onse a ku Israele, zankhondo zili m'manja, nsangamutu zamaluŵa zili kumutu, ankalondola akaziwo pambuyo, nyimbo zili pakamwa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help