1 Ako. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za malalikidwe a Paulo

1Abale, inetu pamene ndidafika kwanu kuti ndikulalikireni chinsinsi chimene Mulungu adatiwululira, sindidayese kulankhula mwaluso, ngati munthu wodziŵa zapatali.

2Koma ndidaatsimikiza kuti pamene ndili pakati panu, ndiiŵale zina zonse, kupatula Yesu Khristu yekha, koma tsono amene adapachikidwa pa mtanda.

3Ntc. 18.9 Choncho pamene ndidafika kwanuko, ndinali wofooka, ndiponso ndinkanjenjemera kwambiri ndi mantha.

4Ndipo pamene ndinkalankhula kapena kulalika, sindinkalankhula moonetsa nzeru, kuyesa kukopa anthu, koma mau anga anali otsimikizika ndi mphamvu za Mzimu Woyera.

5Ndinkachita zimenezi kuti chikhulupiriro chanu chisakhazikike pa nzeru za anthu, koma chikhazikike pa mphamvu za Mulungu.

Za nzeru zimene Mzimu Woyera amapatsa

6Komabe pakati pa anthu okhwima m'chikhulupiriro, timalankhula zanzeru. Koma nzeruzo si za masiku anozi, kapena za akulu olamulira dziko lino lapansi, amene mphamvu zao nzodzatha.

7Nzeru zimene timalankhula, ndi nzeru za Mulungu, zachinsinsi, zobisika kwa anthu. Mulungu asanalenge dziko lapansi, adaakonzeratu zimenezi kuti atipatse ulemerero.

8Bar. 3.14-17Panalibiretu wolamulira wa masiku ano wodziŵa zimenezi. Akadazidziŵa, sakadapachika Ambuye aulemerero pa mtanda.

9Yes. 64.4; Mphu. 1.9, 10Koma ndi monga Malembo anenera kuti,

“Maso a munthu sanaziwone, makutu a munthu sanazimve,

mtima wa munthu sunaganizepo konse

zimene Mulungu adaŵakonzera amene amamkonda.”

10Ifeyo Mulungu adatiwululira zimenezi mwa Mzimu Woyera. Pajatu Mzimuyo amadziŵa zinthu zonse kotheratu, ngakhalenso maganizo ozama a Mulungu.

11Kodi za munthu angazidziŵe ndani, osakhala mzimu wa mwiniwake yemweyo umene uli mwa iyeyo? Momwemonso palibe munthu amene angadziŵe za Mulungu, koma Mzimu wa Mulungu Mwini.

12Ife sitidalandire mzimu wa dziko lino lapansi, koma tidalandira Mzimu Woyera wochokera kwa Mulungu, kuti adzatithandize kumvetsa zimene Mulunguyo adatipatsa mwaulere.

13Timalankhula zimenezi osati ndi mau ophunzitsidwa ndi nzeru za anthu, koma ndi mau amene Mzimu Woyera amatiphunzitsa. Timaphunzitsa zoona zauzimu kwa anthu amene ali naye Mzimu Woyera.

14Munthu wodalira nzeru zake zokha sangalandire zimene zimachokera kwa Mzimu wa Mulungu. Amaziyesa zopusa, ndipo sangathe kuzimvetsa, popeza kuti zimalira kukhala ndi Mzimu Woyera kuti munthu azimvetse.

15Munthu amene ali ndi Mzimu Woyera angathe kuzindikira khalidwe la zonse, ndipo palibe wina amene angathe kutsutsapo ai.

16Yes. 40.13Ndi monga Malembo anenera kuti,

“Ndani adadziŵa maganizo a Ambuye,

kuti athe kuŵalangiza?”

Koma ife tili ndi maganizo a Khristu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help