2 Am. 5 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Nthaŵi imeneyo Antioko adakamenyana nkhondo kachiŵiri ndi dziko la Ejipito.

2Pa masiku makumi anai, mu Yerusalemu monse anthu adaona m'masomphenya ankhondo okwera pa akavalo akuthamanga m'malere atavala zagolide, mikondo ili m'manja ndi malupanga.

3Magulu a akavalowo anali pa mizere atakonzekera nkhondo. Panali kuputana nkuputana, zishango zikuwombana, mikondo ikuponyedwa ngati mvula, mivi ikuuluka.

4Tsono anthu onse ankapemphera kuti zimene ankaona m'masomphenyazo ziŵadzetsere zabwino.

Yasoni athira nkhondo mzinda wa Yerusalemu

5Pambuyo pake kudamveka mbiri yonama yonena kuti Antioko adamwalira. Tsono Yasoni adatenga anthu osachepera 1,000, nakathira nkhondo mzindawo modzidzimutsa. Atagonjetsa alonda a pa malinga, potsiriza adalanda mzinda wonse. Menelasi adathaŵira m'chinyumba chankhondo.

6Yasoni adangopitiriza kupha Ayuda anzake ambiri osaŵamvera chisoni. Sadalingalire konse kuti kugonjetsa anthu a mtundu wako ndi tsoka loopsa. Ankaganiza kuti kupambana kwake kunkatsimikiza kuti adagonjetsa adani, osaona kuti ndi abale ake omwe.

7Koma adalephera kulanda ufumu wa dziko, ndipo chiwembu chake chidamchititsa manyazi, mpaka adathaŵiranso ku dziko la Aamoni.

8Kutsirizika kwake kunali kotere: Areta, mfumu ya Aluya, adamponya m'ndende. Anthu onse ankamuzonda ngati wokana malamulo, ndipo ankamunyoza chifukwa cha kupha anthu a mtundu wake womwe. Aliyense ankamusakasaka, ndiye ankangoti nathaŵira mzinda uwu, kenaka uwu, tsono potsiriza adakabisala ku Ejipito.

9Munthu woti adaapirikitsa anthu ambiri m'dziko mwao, iye yemwe adakafera ku dziko lachilendo. Adaathaŵira mpaka ku Sparta, poganiza kuti anthu akumeneko adzamulandira, chifukwa anali a fuko limodzi, koma zidalephera.

10Motero munthu amene adapha anthu ambiri, osaŵaika m'manda, sipadaoneke ndi mmodzi yemwe wolira maliro ake, sadaulandire mwambo wamaliro, ndipo sadagone m'manda kulondola makolo ake.

Antioko athira nkhondo mzinda wa Yerusalemu

11Mfumu Antioko atamva zimene zidachitikazo, adaganiza kuti Ayuda achita chiwembu. Iye adapsa mtima nachoka ku Ejipito, nkukalanda Yerusalemu poukantha ndi mphamvu.

12Adalamula ankhondo ake kuti aphe onse amene aŵapeze, osaŵachitira chifundo, ndipo othaŵira m'nyumba aŵadule pa khosi.

13Adapha motero anyamata ndi nkhalamba, akazi ndi ana ndi atsikana, ndipo ndi ana akhanda omwe adaphedwa.

14Pa masiku atatu anthu 80,000 adaonongedwa: 40,000 adaphedwa pa nkhondo, 40,000 enawo adaŵagulitsa ku ukapolo.

15Komabe Antioko sadakhutire nazo zimenezo. Adakaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, nyumba yoyera koposa pa dziko lonse lapansi, akumtsogolera Menelasi, munthu wokana Malamulo ndi dziko lake uja.

16Adagwira zinthu zoyera ndi manja ake onyansa, nalanda zinthu zomwe mafumu ena adaapereka kuti zikulitsire ulemerero ndi ukulu wa Nyumbayo.

17Antioko adayamba kudzikuza mumtima mwake, osazindikira kuti Ambuye adaaŵakwiyira anthu amumzindamo pa kanthaŵi chabe, chifukwa cha zoipa zao. Nchifukwa chake Ambuyewo adachita ngati kuŵaiŵala malo oyerawo.

18Ayuda akadaleka kuchita zoipa zambirizo, bwenzinso Mulungu atamkwapula Antioko ndi kumletsa kuchita zachipongwe zakezo, ngati zimene adaaona Heliodoro uja, amene mfumu Seleuko adaamtuma kuti akasuzumire chuma cha m'Nyumba ya Mulungu.

19Ambuye sadasankhule anthu ake chifukwa cha malo amenewo, koma adakhazikitsa malowo chifukwa cha anthu ake.

20Nchifukwa chake malowo nawonso ataona zoipa zimene zidagwera mpingowo pambuyo pake adaona zokondweretsa zakenso. Wamphamvuzonse adaaŵasiya pa nthaŵi imene anali wokwiya. Koma Ambuye mwini zonse atayanjananso ndi anthu ake, malowo adaŵakonza, nakhalanso aulemu kwambiri.

Nkhondo ina yothira Yerusalemu

21Antioko adatenga makilogramu 62,000 a siliva m'Nyumba ya Mulungu, nabwerera mofulumira ku Antiokeya. Mumtima mwake ankaganiza monyada kuti zombo zake zitha kuyenda pa mtunda ngati pa nyanja, ndipo kuti anthu ake nkuponda pa nyanja ngati pa mtunda.

22Adasiya akapitao ake kuti azivuta anthu ku dziko lonselo. Ku Yerusalemu adasiyako Filipo wa ku Frijiya amene anali wa nkhalwe zoopsa kupambana amene adaamutuma.

23Adatumanso Androniko ku Gerizimu. Pamodzi ndi iwowo adatumanso Menelasi amene ankazunza anthu a m'dziko mwake koposa m'mene ankachitira enawo.

24Antioko ankadana ndi Ayuda kwambiri. Tsono adatuma Apoloniyo, mtsogoleri wa ku Misiya, nampatsa gulu la ankhondo okwanira 22,000. Adamlamula kuti akaphe amuna onse ndi kugulitsa ku ukapolo akazi onse ndi ana.

25Atafika ku Yerusalemu, Apoloniyo adachita ngati akufuna mtendere, nadikira mpaka pa tsiku loyera la Sabata. Tsiku limenelo, poti Ayuda ankapumula osagwira ntchito, Apoloniyo adalamula ankhondo ake kuyenda mondanda atanyamula zida zao.

26Kenaka adalamula kuti aŵaphe anthu onse amene adaatuluka kuti akaone m'mene ankhondowo akuyendera. Pambuyo pake adaloŵa mumzinda wonse ndi ankhondowo, napha anthu ambirimbiri.

27Koma Yudasi Makabeo ndi anthu asanu ndi anai adathaŵira ku chipululu. Ankakhala m'mapiri pamodzi ndi anzakewo ngati nyama zakuthengo, namadya zokhazo zomera m'thengo, kuwopa kuti angadziipitse.

Mfumu ilamula Ayuda kutsata miyambo Yachigriki
Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help