1Pa nthaŵi imeneyo Antioko adachoka ndi manyazi ku dziko la ku Persiya.
2Adaaloŵa mu mzinda wa Persepoli, nkuyesa kulanda chuma cha m'nyumba ya milungu yao kuti akhale wolamulira wa mzindawo. Koma anthu akumeneko adamuukira ali ndi zida zao m'manja, ndipo Antioko ndi anthu ake adagonja. Eniake mzindawo adamthamangitsa, iye nkubwerera kwao ndi manyazi aakulu.
3Atafika ku Ekibatana, adamva zimene zidagwera Nikanore ndi gulu lankhondo la Timoteo.
4Adapsa mtima kwambiri, nafuna kuti alipsire Ayuda chifukwa cha manyozo amene adamchita anthu adaampirikitsa aja. Tsono adalamula woyendetsa galeta lake kuti apitirire osaima konse mpaka kukafika ku Yerusalemu. Koma chiweruzo chakumwamba chinali pa iye, chifukwa m'kunyada kwake adaati, “Tsopano ndikafika ku Yerusalemu, ndikasandutsa mzindawo kuti ukhale manda a Ayuda.”
5Koma Ambuye oonazonse, Mulungu wa Aisraele, adamulanga ndi matenda osachizika ndiponso osaoneka. Antioko adangoti atalankhula mau akewo, m'matumbo mwake mudayamba kupweteka kosalekeza, nkumamva kupota zedi m'mimbamo.
6Zimenezi zidaamuyenera chifukwa iyeyo adaazunza anthu ena pa mimba mwankhanza mwa njira zosiyanasiyana.
7Komabe sadaleke chipongwe chake, ndipo kunyada kwake kunkakulirakulira. Adakolezera moto wa mkwiyo wake pa Ayuda, nkulamula omuyendetsawo kuti afulumire. Chifukwa cha chimenecho adagwa pa galeta lake likuyenda mwaliŵiro choncho; pakugwapo ziwalo zonse m'thupi mwake zidayamba kuphwanya.
8Iye amene posachedwapa ankadzikuza kopitirira umunthu wake, namaganiza zoti nkulamula mafunde apanyanja, ndi kuŵayesa pa sikelo mapiri aatali, adagwa pansi, nachita kumnyamulira m'machira, kutsimikiza ndithu pamaso pa onse kuti Mulungu ngwamphamvudi.
9Pambuyo pake ndi m'maso mwake momwe munkatuluka mphutsi, ndipo akali moyo, minofu yake inkanyenyeka, iye nkumamva kupweteka kosaneneka. Tsono fungo la kuwolako ankhondo ake onse ankanyansidwa nalo.
10Chifukwa cha kununkha kwambiri choncho, panalibe ndi mmodzi yemwe mwa anthu ake wovomera kumnyamula munthu amene posachedwa pomwepa ankaganiza zoti nkukhudza nyenyezi zamumlengalenga.
11Pamenepo adayamba kulekako kunyada kwake kwakukulu kuja, nkuyambapo kukhalako ndi nzeru, poona kuti Mulungu akumlanga chotere, chifukwa ankamva kupweteka kosalekeza.
12Tsono popeza kuti iye yemwe adalephera kupirira fungo la kuvunda kwake komwe, adati, “Nkoyenera ndithu kugonjera Mulungu, ndipo munthu asamayerekeze kudzilinganiza ndi Mulungu.”
13Pambuyo pake munthu woipayo adapemphera kwa Ambuye Mulungu, amene ankaoneka kuti sakufunanso kumchitira chifundo;
14ndipo adanenetsa kuti adzaupatsa ufulu mzinda woyera kumene ankafulumira kukafikako, kuti ausalaziretu ndi kuusandutsa manda a Ayuda.
15Tsono Ayudawo, amene iye ankaganiza kuti ngosayenera kuŵaika m'manda, koma kungoŵataya onse ndi ana ao omwe kuti zilombo ndi mbalame ziŵadye, tsopano iye adati adzaŵalinganiza ndi anthu a ku Atene.
16Ndipo Nyumba ya Mulungu imene adaailanda ziŵiya zake, adzaikometsa ndi mphatso zabwino kwambiri. Adzabweza ziŵiya zopatulika zonse zija ndi kuwonjezera zina zoposa pamenepo. Ndipo ndalama zofunika ku nsembe adzazitapa m'bokosi lakelake.
17Adalonjezanso kuti, kuwonjezera pa zonsezo, iyeiyeyo adzasanduka Myuda, ndipo adzayendera maiko onse a anthu, kuti akalalikireko mphamvu za Mulungu.
Antioko alemba kalata kwa Ayuda18Antioko poona kuti masautso ake sakutha, malinga nkuti chiweruzo cha Mulungu chinali chitamgwera molungama, adataya mtima nalembera Ayuda kalata yokhala ngati pemphero. Kalatayo adaailemba motere:
19“Kwa Ayuda, anthu anga olemekezeka, ine Antioko, mfumu yao ndi mtsogoleri wao wankhondo, ndikuti moni, ndikukufunirani moyo wamphamvu ndi mtendere.
20“Ngati muli bwino nonse ndi ana omwe, ngati zanu zonse zikukuyenderani bwino, ndikondwera kwambiri. Ine tsopano chikhulupiriro changa chili mwa Mulungu.
21Ndikukumbukira ndi mtima wachimwemwe ulemu wonse ndi chifundo chonse zimene mwakhala mukundiwonetsa. Pobwerera kuchokera ku dera la Persiya, paja ndidayamba kudwala nthenda yoopsa. Tsono ndidaganiza zoti ndiyambepo kukonzera anthu onse mtendere.
22Sikuti ndataya mtima ai, poti ndikuyembekeza ndithu kuti ndidzachira.
23Koma ndikukumbukira kuti pamene bambo wanga ankakachita nkhondo ku madera akumtundaku, ankalozeratu woti nkumubadirisa.
24Ankatero kuti zina zitachitika mwadzidzidzi, kapena patabwera uthenga wa zovuta, anthu am'mdzikomo asadzavutike, adzangodziŵiratu kuti amene ali mfumu ndi wakutiwakuti.
25Kuwonjezera apo, ndikudziŵa kuti mafumu am'malireŵa, ndi ena onse oyandikana nawoŵa, akungoyang'ana nkumadikira kuti aone zimene zichitike. Nchifukwa chake ndaika mwana wanga Antioko kuti adzaloŵe ufumu m'malo mwanga. Pamene ndinkayendera madera akumtundaku, paja ndinkakonda kumsiya m'manja mwanu enanu kuti muzimsamala. Mwakuti iyeyo ndamlemberanso kalata yonga yomweyi.
26Tsono ndikukupemphani kuti mukumbukiredi zabwino zimene ndidakuchitirani nonsenu pamodzi kapena aliyense payekhapayekha, inunso mupitirire kutimvera chifundo ineyo ndi mwana wanga.
27Ndikukhulupirira kuti iyeyo adzatsata mchitidwe wanga ndi kukhala wofatsa ndi wokoma mtima kwa inu.”
28Motero munthu wopha anzake uja ndi wonyoza Mulungu, atasauka ndi mazunzo aakulu, ofanafana ndi omwe ankasautsa nawo ena, adafera ku dziko lachilendo pakati pa mapiri. Adafa imfa ya tsoka lalikulu.
29Filipo, bwenzi lake lakale, adatenga maliro ake kupita nawo kwao. Koma chifukwa choopa Antioko mwana wa mfumu, adathaŵira ku Ejipito kwa Ptolemeyo Filometore.
Yudasi ayeretsanso Nyumba ya MulunguWho We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.