1Ana inu, mundimvere ine bambo wanu.
Mukafuna kupulumuka,
muchite zimene ndikuuzeni.
2Ambuye adapatsa bambo ulemu woposa ana ake,
adatsimikiza mphamvu za mai pa ana ake.
3Amene amalemekeza atate ake,
amapepesa Mulungu
chifukwa cha machimo ake.
4Amene amalemekeza amai ake,
amachita ngati kudzikundikira chuma.
5Amene amalemekeza atate ake,
ana ake adzamsangalatsa,
ndipo akamapemphera,
mapemphero ake adzamveka.
6Amene amalemekeza atate ake,
adzakhala ndi moyo wautali.
Amene amamvera Ambuye,
amasangalatsa amai ake.
7Amene amaopa Ambuye,
amalemekeza atate ake,
amagwirira ntchito makolo ake
ngati mtumiki wao.
8 Eks. 20.12 Mwana wanga,
uzilemekeza atate ako ndi mau apakamwa
ndiponso ndi ntchito zako,
kuti madalitso ao akhale pa iwe.
9Pajatu madalitso a bambo
amalimbitsa mabanja a ana ake,
koma matemberero a mai
amazula maziko a mabanjawo.
10Usadzikweze pakuchititsa manyazi bambo wako.
Manyazi a bambo wako angakupatse bwanji ulemu?
11Munthu amapeza ulemu
chifukwa cholemekeza atate ake.
Ndipo kusalemekeza amai
nchinthu chochititsa ana manyazi.
12Mwana wanga, usamale bambo wako atakalamba,
usamuvute konse pa moyo wake wonse.
13Ngakhale nzeru zake zikuyamba kutha,
iwe uzimuwonetsa ndithu chifundo.
Usamnyoze chifukwa chongoti uli ndi moyo wolimba.
14Chifundo chochitira bambo wako sichidzaiŵalika,
adzachiŵerengera ngati cholipirira machimo ako.
15Pamene udzagwe m'mavuto
Mulungu adzakukumbukira,
ndipo machimo ako
adzasungunuka ngati chisanu pa dzuŵa.
16Amene sasamala bambo wake,
ali ngati munthu wonyoza Mulungu mwachipongwe.
Amene amakwiyitsa mai wake,
Ambuye amamtemberera.
Za kudzichepetsa17Mwana wanga,
ukhale wodekha pa zonse zimene umachita,
ndipo anthu okomera Ambuye adzakukonda.
18 Afi. 2.3 Ngati ndiwe wotchuka kwambiri, udzichepetse,
ukatero udzapeza kuyanja pamaso pa Ambuye.
19Pali anthu ambiri otchuka ndi amphamvu,
koma Ambuye amaulula zinsinsi zao
kwa anthu odzichepetsa.
20Pajatu mphamvu za Ambuye nzazikulu,
amalemekezedwa ndi anthu odzichepetsa.
21Usayese kumvetsa zinthu
zimene zili zapatali kwa iwe,
kapena kufufuza zinthu
zimene zili zopitirira nzeru zako.
22 Deut. 29.29 Uzilingalira kwambiri
za ntchito imene walandira,
zimene zili zobisika kwa iwe
ulibe nazo ntchito.
23Usatanganidwe ndi zinthu
zopitirira nzeru zako,
ngakhale zimene adakuphunzitsa
nzopitirira nzeru za anthu.
24Ambiri adasokera
chifukwa cholingalira zinthu zapatali,
ndipo zopeka zao zonama
zidasokeretsa maganizo ao.
Za kunyada25Ngati ulibe maso,
sungathe kupenya.
Ngati ndiwe mbuli,
usadziwonetse ngati wanzeru.
26Munthu wokanika adzatha moipa.
Munthu woseŵera ndi zoopsa,
adzataya moyo wake.
27Mtima wokanika umadzitengera mavuto ambiri,
munthu wochimwa amanka nachimwirachimwira.
28Tsoka likagwera wonyada,
palibe mankhwala,
pakuti kuipa kumakhala kutazika mizu mwa iye.
29Munthu wochenjera amalingalira bwino fanizo,
munthu wanzeru amafunitsitsa
kukhala ndi makutu atcheru.
Za Kuthandiza osauka30Monga momwe madzi amazimira moto walaŵilaŵi,
momwemonso mphatso zopatsa osauka
zimapepesera machimo.
31Amene amabwezera zabwino kwa zabwino,
amaganizira zam'tsogolo.
Pamene azidzati agwe,
anzake adzamchirikiza.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.