2 Maf. 9 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yehu adzozedwa kuti akhale mfumu ya ku Israele

1Masiku amenewo Elisa adaitana mmodzi wa m'gulu la aneneri, namuuza kuti, “Konzekera ulendo ndipo utenge nsupa iyi ya mafuta m'manja, upite ku Ramoti-Giliyadi.

2Ukakafika, ukafunefune Yehu, mwana wa Yehosafati, mdzukulu wa Nimisi. Utampeza ukamuuze kuti achokepo pakati pa anzake, ndipo ukaloŵe naye m'chipinda cham'kati.

3Tsono ukathire mafutaŵa pamutu pake, ndipo ukanene kuti, ‘Chauta akukudzoza kuti ukhale mfumu ya ku Israele.’ Pomwepo ukatsekule chitseko ndipo ukathaŵe, usakachedwe ai.”

4Motero mneneriyo adapita ku Ramoti-Giliyadi.

5Atafika, adapeza atsogoleri ankhondo ali pa msonkhano. Tsono iyeyo adati, “Zikomo bwana, ine ndili ndi mau oti ndikuuzeni.” Yehu adafunsa kuti, “Kodi ukunena yani mwa ifeyo?” Mneneri uja adayankha nati, “Inuyo bwana.”

61Maf. 19.16 Pamenepo Yehuyo adanyamuka nakaloŵa m'nyumba. Ndipo mneneri uja adathira mafuta pamutu pa Yehu nati, “Chauta, Mulungu wa Israele, akuti akukudzozani inu kuti mukhale mfumu ya Aisraele, anthu a Chauta.

7Tsono mukakanthe banja la Ahabu mbuyanu, kuti Chautayo alipsire Yezebele, chifukwa cha aneneri ake ndiponso atumiki ena onse amene iyeyo adaŵapha.

8Ndithu banja lonse la Ahabu lidzatha phu! Ku Israele adzapha mwamuna aliyense wa banja la Ahabu, kapolo kapena mfulu.

9Tsono Chautayo adzasandutsa banja la Ahabu kuti lifanane ndi banja la Yerobowamu mwana wa Nebati, ndiponso la Baasa mwana wa Ahiya.

101Maf. 21.23 Ndipo agalu adzamudya Yezebele ku dziko la Yezireele. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzamuike.” Atanena mau amenewo, mneneri uja adatsekula chitseko, nathaŵa.

11Tsono Yehu atatuluka kubwerera kwa atsogoleri anzake aja, iwo adamufunsa kuti, “Kodi nkwabwino? Wamsala uja anadzatani kwa inu?” Yehu adayankha kuti “Ai, mukumdziŵa munthu wotere ndi zolankhula zake zomwe.”

12Koma iwowo adati, “Iyai ndithu, mutiwuze.” Apo Yehu adati, “Iyeyo wandiwuza mau a Chauta akuti, ‘Ine ndikukudzoza iwe kuti ukhale mfumu ya ku Israele.’ ”

13Pomwepo aliyense mwa iwowo adatenga mwinjiro wake nauyala pa makwerero, kuti Yehu akhalepo, ndipo adaliza lipenga, nalengeza kuti, “Yehu ndiye mfumu.”

Kuphedwa kwa Yoramu mfumu ya ku Israele

14Motero Yehu, mwana wa Yehosafati, mdzukulu wa Nimisi, adachita chiwembu mfumu Yoramu. Pomwe zinkachitika zimenezi, nkuti Yoramu pamodzi ndi Aisraele onse akudikira Hazaele mfumu ya Asiriya ku Ramoti-Giliyadi, kuti amenyane naye nkhondo.

15Koma nthaŵiyo mfumu Yoramu anali atabwerera ku Yezireele, kuti akachire mabala amene adamlasa Asiriya aja pa nthaŵi imene ankamenyana nkhondo ndi Hazaele uja. Tsono Yehu adauza atsogoleri ankhondo anzake aja kuti, “Ngati mufuna kuti ndikhale mfumu, musalole ndi mmodzi yemwe kuti achoke mumzinda muno, kuti akanene nkhani zimenezi ku Yezireele.”

16Apo Yehu adakwera galeta lake, napita ku Yezireele poti Yoramu anali chigonere kumeneko. Ahaziya, mfumu ya ku Yuda, anali atabwera komweko kudzacheza ndi Yoramuyo.

17Tsono mlonda amene ankaimirira pa nsanja yolondera mzinda wa Yezireele, adaona gulu lankhondo la Yehu likubwera, ndipo adati, “Ndikuwona gulu lankhondo.” Pompo Yoramu adati, “Tuma munthu pa kavalo kuti akumane nawo, ndipo akafunse kuti, ‘Kodi ndi zamtendere?’ ”

18Munthu wokwera pa kavalo uja adapita kukakumana nawo nati, “Mfumu ikufunsa kuti, ‘Kodi ndi zamtendere?’ ” Yehu adayankha kuti, “Kodi iweyo nkhani ya mtendere uli nayo chiyani? Tiye, uzinditsata pambuyo.” Mlonda uja adakanena kwa mfumu Yoramu kuti, “Wamthenga uja wakafika ndithu kwa anthuwo, koma sakubwerako ai.”

19Tsono Yoramu adatumanso munthu wachiŵiri wokwera pa kavalo, amene adakafika kwa anthuwo nakaŵafunsanso kuti, “Mfumu ikufunsa kuti, ‘Kodi ndi zamtendere?’ ” Apo Yehu adayankhanso kuti, “Kodi iweyo nkhani ya mtendere uli nayo chiyani? Tiye, uzinditsata pambuyo.”

20Mlonda uja adakanenanso kuti, “Amene ujanso wakafika kwa anthuwo, koma sakubwerako ai. Ndipo kuthamanga kwa mtsogoleri wa gululo nkoopsa, ndi ngati m'mene amathamangira Yehu mwana wa Nimisi.”

21Atamva zimenezo Yoramu adati, “Konzekani.” Pomwepo anthuwo adakonza galeta lake. Tsono Yoramu mfumu ya ku Israele, pamodzi ndi Ahaziya mfumu ya ku Yuda, adanyamuka, wina m'galeta mwake, winanso mwake, ndipo adakumana ndi Yehu pa munda wa Naboti wa ku Yezireele uja.

22Yoramu ataona Yehu, adafunsa kuti, “Iwe Yehu, kodi ndi zamtendere?” Iyeyo adayankha kuti, “Kodi pangakhale mtendere bwanji pamene za kupembedza mafano ndi zanyanga zimene adayamba mai wako zikupitirirabe?”

23Apo Yoramu adabwevuka nathaŵa, ndipo adafuulira Ahaziya uja kuti, “Iwe Ahaziya, atiwukira anthuŵa.”

24Tsono Yehu adakoka uta ndi mphamvu zake zonse nalasa Yoramu kumsana pakati pa mapewa, kotero kuti muvi udaloŵa mpaka ku mtima, ndipo adagwera m'galeta momwemo.

25Pompo Yehu adauza Bidikari kapitao wake kuti, “Mnyamule, umponye m'munda wa Naboti wa ku Yezireele. Kumbukira kuti muja ine ndi iwe tinkayenda pambuyo pa Ahabu atate ake a Yoramu, Chauta adaamtemberera kuti,

261Maf. 21.19‘Ndithudi monga m'mene ndidaonera kuphedwa kwa Naboti ndi ana ake dzulo, ndikukuuza kuti Ine ndidzakubwezera choipa chimenechi pamunda pompano.’ Nchifukwa chake tsono, mtengeni, mumponye m'mundamu, potsata zimene Chauta adaanena.”

Kuphedwa kwa Ahaziya mfumu ya ku Yuda

27Tsono Ahaziya mfumu ya ku Yuda ataona zimenezi, adathaŵira ku Betehagani. Koma Yehu adamlondola nati, “Nayenso mlaseni.” Ndipo adamlasira m'galeta pa chitunda cha Guri, pafupi ndi Ibleamu. Tsono Ahaziya adathaŵira ku Megido, nakafera komweko.

28Nduna zake zidamnyamulira m'galeta kunka naye ku Yerusalemu, ndipo zidamuika m'manda momwe adaikidwa makolo ake mu mzinda wa Davide.

29Pa chaka cha 11 cha ufumu wa Yoramu mwana wa Ahabu, mpamene Ahaziya adaayamba kulamulira Yuda.

Kuphedwa kwa Yezibele

30Yehu atafika ku Yezireele, Yezibele adamva zimene zidachitika. Ndipo adapaka maso ake utoto, naluka tsitsi lake, namasuzumira pa windo.

31Tsono pamene Yehu ankaloŵa pa chipata, Yezibeleyo adamkuwira nati, “Inu aZimuri, amene mudapha mbuyanu, kodi ndi zamtendere?”

32Yehu adayang'ana ku zenera nati, “Kodi akugwirizana ndi ine ndani?” Tsono atumiki aŵiri kapena atatu a ku bwalo la mfumu adayang'ana Yehu uja.

33Iyeyo adaŵalamula kuti, “Mponyeni pansi mkaziyo.” Pomwepo iwo adamponya pansi, ndipo magazi ake ena adafalikira pa khoma ndi pa akavalo. Kenaka Yehu adayendetsa akavalo ake nkumpondereza mkaziyo.

34Pambuyo pake Yehu adaloŵa m'nyumba yaufumu naadya ndi kumwa. Kenaka adati, “Kamtoleni mkazi wotembereredwa uja, mukamuike, pakuti ndi mwana wa mfumu.”

35Koma pamene ankapita kuti akamuike, sadapezepo nkanthu komwe koma chibade, mapazi ndi zikhatho za manja ake basi.

361Maf. 21.23 Atabwererako anthuwo ndi kukamuuza Yehu, iyeyo adati, “Ameneŵa ndiwo mau a Chauta amene adalankhula kudzera mwa Eliya mtumiki wake wa ku Tisibe, kuti, ‘Agalu adzadya mtembo wa Yezibele ku dziko la Yezireele.

37Motero mtembo wakewo udzakhala ngati ndoŵe pa munda m'dziko la Yezireele, kotero kuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzatha kunena kuti, “Uyu ndi Yezibele.” ’ ”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help