Neh. 6 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Adani amchita chiwembu Nehemiya

1Kudangotero kuti Sanibalati, Tobiya, Gesemu Mwarabu ndiponso adani athu ena adamva kuti tidatha kumanganso khoma, ndipo kuti sipadatsale mpamodzi pomwe pogumuka, ngakhale tinali tisanaike zitseko pa zipata.

2Tsono Sanibalati ndi Gesemu adanditumizira mau onena kuti, “Mubwere, tidzakumane pa mudzi wina m'chigwa cha Ono.” Ankafuna kukandichita chiwembu kumeneko.

3Nchifukwa chake ndidaŵatumira amithenga kukaŵauza kuti, “Ine kuno ndili pa ntchito yaikulu, sindingathe kuchoka kuti ndibwere kumeneko. Kodi ntchito iime, pofuna kuti ndibwere kumeneko?”

4Tsono adanditumizira mau okhaokhawo kanai konse, ndipo ndidaŵayankha chimodzimodzi.

5Pamenepo Sanibalati adatumanso wantchito wake kachisanu kwa ine. Iye anali ndi kalata yosamata m'manja mwake.

6M'kalatamo munali mau akuti, “Pakati pa mitundu ya anthu pano pamveka mphekesera, ndiponso Gesemu akunenanso momwemo, kuti inuyo, pamodzi ndi Ayuda, mukufuna kuukira boma. Nchifukwa chake mukumanganso khoma. Mukufuna kuti mukhale mfumu yao monga m'mene zikumvekeramu.

7Mwaikanso aneneri ku Yerusalemu oti azilengeza za inu kuti, ‘Ku Yuda kuli mfumu tsopano!’ Tsono zonsezi zimveka ndithu kwa mfumu ya ku Persiya. Choncho mubwere kuti tidzakambirane tonse pamodzi.”

8Apo ndidamtumizira mau akuti, “Pa zimene mukunenazi, palibe chimene chidachitikapo. Zonsezi mukungoziganiza nokha.”

9Ndidaazindikira kuti adaniwo ankangofuna kutiwopsa, namaganiza kuti, “Ayudaŵa adzachita mantha ndipo adzaleka kugwira ntchito, motero ntchitoyo siidzatha.” Koma ine ndidapemphera kuti, “Inu Mulungu, tsopano mundilimbitse mtima.”

10Nthaŵi imeneyo ndidapita ku nyumba ya Semaya, mwana wa Delaya, mwana wa Mehetabele, amene sankatuluka m'nyumba mwake. Iye adandiwuza kuti, “Tiyeni tikabisale m'Nyumba ya Mulungu, tikatsekeko pakuti akubwera kudzakuphani. Ndithudi, akubwera usiku kudzakuphani.”

11Koma ine ndidayankha kuti, “Munthu wonga ine nkuthaŵa kodi? Ndipo munthu wonga ine, kodi nkukabisala m'Nyumba ya Mulungu, kuti ndidzipulumutse? Zimenezo ai, toto, ine sindipitako!”

12Kenaka ndidazindikira kuti Mulungu sadamtume, koma ankandinenera zimenezi chifukwa chakuti Tobiya ndi Sanibalati ndiwo adaamlemba ntchito imeneyi.

13Chimene adaamlembera ntchitoyo nkuti andichititse mantha, ineyo ndithaŵe. Motero ndikadachimwa, ndipo iwowo akadandiipitsira mbiri kuti azidzandinyodola.

14Pamenepo ndidapemphera kuti, “Inu Mulungu wanga, kumbukirani zimene Tobiya ndi Sanibalati adachita. Kumbukiraninso zimene mneneri wamkazi Nowadiya ndiponso aneneri ena aja ankachita pofuna kundichititsa mantha.”

Kutsiriza kwake kwa ntchito

15Patapita masiku 52, pa tsiku la 25 la mwezi wa Eluli, khoma lija adatsiriza kumanga.

16Adani athu onse a m'madera oyandikana nafe atamva zimenezi, adachita mantha kwambiri. Adachita manyazi pakuti iwo adaazindikira kuti ntchitoyo yachitika ndi chithandizo cha Mulungu wathu.

17Kuwonjezera apo, nthaŵi imeneyo atsogoleri a ku Yuda ankalemberana makalata ndi Tobiya,

18pakuti anthu ambiri ku Yuda adaalumbira kuti adzagwirizana naye, chifukwa chakuti anali mkamwini wa Myuda mnzao, Sekaniya, mwana wa Ara. Ndipo mwana wake, Yehohanani, anali atakwatira mwana wamkazi wa Mesulamu, mwana wa Berekiya.

19Anthu ankasimba za ntchito zabwino za Tobiyayo ine ndili pomwepo, ndipo ankamuululira mau anga. Choncho iyeyo ankalemba makalata ondichititsa mantha aja.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help