1 Yer. 20.14-18 Pambuyo pake Yobe adalankhula, nayamba kutemberera tsiku lake lobadwa.
2Mphu. 23.14Adati,
3“Tsiku limene ine ndidabadwa litembereredwe,
nawonso usiku umene mai wanga
adatenga pathupi pa ine utembereredwe.
4Tsiku limenelo lisanduke lamdima.
Mulungu kumwambako asaliganizirenso tsiku limenelo,
kuŵala kusadzaonekenso pa tsikulo.
5Tsikulo likhale la mdima wabii,
likhale lamikhwithi,
mdima wake ukhale woopsa.
6Usiku umenewo ukhale wa mdima wandiweyani.
Tsiku limenelo lisakhalenso pamodzi
ndi masiku a pa chaka,
lisaŵerengedwerenso kumodzi ndi masiku a pa miyezi.
7Ndithu usiku umenewo usabweretsenso
chabwino chilichonse,
kusamvekeponso nthungulu zachikondwerero usikuwo.
8Odziŵa kutemberera masiku, alitemberere tsikulo,
ndiye kuti odziŵa kuutsa Leviyatani,
chilombo cham'nyanja chija.
9Nyenyezi zake zambandakucha zisaŵale.
Tsikulo liyembekeze kucha, koma pachabe.
Lisaonenso kuŵala kwa mbandakucha.
10Tsiku limenelo litembereredwe,
chifukwa ndi limene ndidatuluka m'mimba mwa mai wanga,
ndipo ndi limene lidandiwonetsa zovuta.
11“Bwanji sindidangobadwa wofaifa!
Bwanji sindidangoti badwu nkufa!
12Chifukwa chiyani mai wanga adandifukata?
Chifukwa chiyani adandiyamwitsa?
13Ndikadafa pobadwa pomwe,
bwenzi ndikukhala nditagona mwaphee,
kungogona tulo, ndi kumangopumula.
14Bwenzi ndikukhala limodzi
ndi mafumu ndi aphungu a pa dziko lapansi,
amene adadzimangira nyumba zikuluzikulu
pa mabwinja akale.
15Bwenzi ndikukhala limodzi ndi mafumu okhuphuka,
amene adadzaza nyumba zao ndi golide ndi siliva.
16Bwenzi sindidangokhala ngati mtayo woikidwa m'manda,
ngati makanda amene sadaonepo kuŵala kwa dzuŵa.
17Kumandako anthu oipa savutitsanso,
anthu otopa akupumula kumeneko.
18Am'ndende akupeza nawo mtendere kumeneko,
sakumvanso mau ankhanza a kapitao wa ndende.
19Anthu wamba ndi apamwamba omwe ali pamodzi kumeneko,
kapolo ndi womasuka kwa mbuyake.
20“Chifukwa chiyani dzuŵa
limamuŵalira munthu wapamavuto?
Chifukwa chiyani amakhalabe ndi moyo
munthu wa mtima woŵaŵa?
21 Chiv. 9.6 Amalakalaka imfa, koma osaiwona,
amaifunafuna kupambana chuma chobisika.
22Amakondwa ndi kusangalala kwambiri
akafa ndi kuikidwa m'manda.
23Chifukwa chiyani moyo umapatsidwa kwa munthu
amene njira ya moyo wake yabisika,
amene Mulungu wamzinga ndi mavuto ponseponse?
24M'malo moti ndidye, ndimalira,
ndipo kubuula kwanga nkosalekeza.
25Zimene ndinkaziwopa zachitika ndithu,
zimene ndinkachita nazo mantha zandigweradi.
26Ine sindipeza mtendere kapena bata,
sindiwona mpumulo, koma mavuto okhaokha.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.