1Tamvani tsono inu mafumu,
ndipo mumvetse bwino.
Phunzirani inu oweruza dziko lonse lino lapansi.
2Tcherani khutu, inu olamulira makamu a anthu,
inu amene mumanyadira kuweruza unyinji wa mafuko.
3 Aro. 13.1 Mphamvu zanu adakupatsani ndi Ambuye.
Wopambanazonse ndiye amene adakupatsani ulamuliro.
Ndiye amene adzayang'anitsitsa ntchito zanu
ndi kusanthula maganizo anu.
4Tsono ngati inu, atumiki a Ufumu wake,
simudaweruze mwachilungamo,
ngati simudamvere malamulo,
ndipo ngati simudatsate kufuna kwa Mulungu,
5Iye adzakufikirani moopsa ndi mwadzidzidzi,
chifukwa mlandu umakhala woopsa
kwa anthu olamulira anzao.
6Anthu wamba adzaŵachitira chifundo
ndi kuŵakhululukira,
koma anthu amphamvu adzafufuza kwambiri ntchito zao.
7Ambuye, mwini zinthu zonse,
saopa ndi mmodzi yemwe.
Saŵerengera kuti uyu ndi wamkulu,
chifukwa ndiye amene adalenga akuluakulu
ndi ang'onoang'ono omwe,
onse amaŵasamala chimodzimodzi.
8Koma amene ali ndi mphamvu,
Iye adzayang'anitsitsa kwambiri ntchito zao.
9Tsono inu mafumu, mau angaŵa akukhalira inu,
kuti muziphunzira luntha, osalekana nalo.
10Adzaŵaŵerengera kuti ndi oyera mtima
amene amatsata malamulo olungama ndi mtima wabwino.
Amene adaŵaphunzira, adzatetezedwa nawo.
11Tsono funafunani mau anga, muziŵakhumbira,
ndipo mudzakhala ndi luntha.
Kupeza luntha nkwapafupi12Luntha ndi loŵala,
lilibe mdima.
Kwa olikonda, nkwapafupi kuliwona,
olifunafuna amalipeza.
13Limadziwonetsa mwamsanga
kwa anthu olifuna.
14Munthu wodzuka m'mamaŵa kuti alifune, sadzavutika,
adzalipeza litakhala kale pakhomo pake.
15Kuikapo mtima pa za luntha
ndiye kumvetsa bwino zinthu.
Munthu wochita changu polifunafuna,
adzaona msanga mtendere wamumtima.
16Pajatu limayendayenda
kufunafuna oyenera kulilandira,
limadziwonetsa kwa iwowo m'njira zao,
limapezekanso ndi m'maganizo ao omwe.
17Luntha limayamba nkufunitsitsa kuphunzira,
kutekeseka ndi maphunziro ndiye kukonda luntha.
18Kulikonda ndiye kumvera malamulo ake,
kutsata malamulo akeko
kumafikitsa ku moyo wosatha,
19moyo wosathawo
umafikitsa munthu pafupi ndi Mulungu.
20Choncho kulakalaka luntha
kumafikitsa ku ufumu.
21Tsono ngati inu, mafumu a mitundu ya anthu,
mumakondwerera mipando yanu ndi ndodo zanu zaufumu,
mulemekeze luntha,
kuti ufumuwo muzikhala nawo nthaŵi zonse.
Solomoni afotokoza za luntha22Nanga luntha nchiyani?
Ndipo lidayamba bwanji?
Ndikufotokozerani,
sindikubisirani kanthu,
ndililongosola mwatsatanetsatane
kuchokera pa chiyambi chake.
Ndilifotokoza momveka,
osasiyapo choona china chilichonse.
23Sindikhala ndi nsanje pofotokoza zimenezo,
chifukwa nsanje siyanjana ndi luntha.
24Anthu aluntha akachuluka,
amadzetsa chipulumutso
pa dziko lino lapansi,
mfumu yaluntha imadzetsera anthu ake mtendere.
25Tsono phunzirani zimene nditi ndikuuzeni,
mukatero mudzapezapo phindu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.