Eza. 5 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ntchito yomanga Nyumba ya Mulungu iyambikanso

1 Hag. 1.1; Zek. 1.1 Nthaŵi imeneyo aneneri aŵa, Hagai ndi Zekariya mwana wa Ido, adayamba kulankhula kwa Ayuda okhala m'dziko la Yuda ndi mu Yerusalemu. Ankalankhula m'dzina la Mulungu wa Israele amene anali nawo.

2Hag. 1.12; Zek. 4.6-9 Atamva mauwo, Zerubabele mwana wa Sealatiele ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki adanyamuka nakayambanso kumanga Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Aneneri a Mulunguwo nawonso anali nawo pamodzi namaŵathandiza.

3Nthaŵi yomweyo Tatenai, bwanamkubwa wa chigawo cha Patsidya pa Yufurate ndi Setari-Bozenai, pamodzi ndi anzao adapita kwa iwowo, ndipo adalankhula nawo naŵafunsa kuti, “Adakulamulani ndani kuti mumange Nyumba imeneyi ndi kumaliza khoma lake?”

4Adaŵafunsanso kuti, “Kodi anthu amene akumanga Nyumba imeneyiŵa, maina ao ndani?”

5Koma Mulungu wao ankaŵasamalira atsogoleri a Ayuda, ndipo choncho anthu aja adaganiza zoti asaŵaletse Ayudawo kumanga mpaka atalembera mfumu Dariusi kalata, nkulandiranso yankho lake pa nkhani imeneyi.

6Nayi kalata yomwe Tatenai, bwanamkubwa wa dera la Patsidya pa Yufurate, ndiponso Setari-Bozenai ndi anzake, akazembe omwe anali m'chigawo cha Patsidya pa Yufurate, adatumiza kwa mfumu Dariusi.

7Adalemba kuti, “Kwa mfumu Dariusi, ulamuliro wanu ukhale ndi mtendere wonse.

8Inu mfumu, mudziŵe kuti ife tidaapita ku dziko la Yuda ku Nyumba ya Mulungu wamkulu. Nyumbayo ikumangidwa ndi miyala ikuluikulu, ndipo akuyalika mitengo pa makoma. Ntchito imeneyi ikuchitika mwachangu, ndipo ikuyenda bwino kwambiri poigwira anthuwo.

9Tsono tidaŵafunsa atsogoleriwo kuti, ‘Kodi adakulamulani ndani kuti mumange Nyumba imeneyi ndi kutsiriza makoma ake?’

10Tidaŵafunsanso maina ao, kuti tikalemba maina a atsogoleri ao, tidzakudziŵitseni.

11Anthuwo adatiyankha kuti, ‘Ife ndife atumiki a Mulungu wa dziko lakumwamba ndi wa dziko lapansi, ndipo tikumanganso Nyumba imene mfumu ina yamphamvu ya Israele idaamanga ndi kuimaliza zaka zamakedzana.

122Maf. 25.8-12; 2Mbi. 36.17-20; Yer. 52.12-15 Koma chifukwa choti makolo athu adaakwiyitsa Mulungu Wakumwamba, Iye adaaŵapereka kwa Nebukadinezara, Mkaldea, mfumu ya ku Babiloni. Ndiye amene adaaononga nyumba ino, natenga anthu onse kunka nawo ku ukapolo ku Babiloni.

13Eza. 1.2-11 Komabe chaka choyamba cha ufumu wa Kirusi mfumu ya ku Babiloni, Kirusiyo adapanga lamulo lakuti Nyumba ya Mulunguyi imangidwenso.

14Ndipo ziŵiya zagolide ndi zasiliva za ku Nyumba ya Mulungu zimene Nebukadinezara adaatulutsa ku Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu ndi kukazilonga m'nyumba ya milungu ya ku Babiloni, zomwezonso mfumu Kirusiyo adazitulutsa ku nyumba ya milungu ya ku Babiloniyo, nazitumiza kwa munthu wina dzina lake Sesibazara, amene mfumu idampatsa ulamuliro mu Yerusalemu.

15Tsono mfumuyo idamuuza kuti, “Tenga ziŵiyazi, ukaziike m'Nyumba ya Mulungu ya ku Yerusalemu, ndipo Nyumbayo imangidwenso pa maziko ake akale.”

16Tsono Sesibazarayo adabwera, nayamba kumanga maziko a Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Kuyambira nthaŵi imeneyo mpaka tsopano yakhala ikumangidwa, ndipo siinathebe.’

17Nchifukwa chake tsono, chikakukomerani inu mfumu, pachitike kafukufuku m'nyumba mosungira chuma ndi mabuku okhudza mbiri zakale ku Babiloniko, kuti tiwone ngati mfumu Kirusi adaaperekadi lamulo lonena za kumanganso Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Kenaka chonde, inu amfumu, mutidziŵitse zomwe zikukondwetseni kuti mugamule pa nkhani imeneyi.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help