1Ukakhudza phula, limakukangamira.
Ukamayanjana ndi anthu onyada, nawenso udzakhala wonyada.
2Usanyamule katundu wobzola mphamvu zako.
Usamayanjane ndi munthu woposa iwe pa mphamvu ndi chuma.
Mbiya yadothi ndi chiŵiya chachitsulo
zingayenderane bwanji?
Zitati ziwombane, mbiyayo nkuphwanyika.
3Munthu wolemera akalakwa, amakangaza kudzudzula anthu ena.
Munthu wosauka anzake akamlakwira, amayenera
kupepesa ndi iyeyo.
4Munthu wolemera amafuna chithandizo chako,
akaona kuti iyeyo apezapo phindu.
Koma iweyo ukasoŵa ch ithandizo, amakulekerera.
5Ngati uli pabwino, amakhala nawe,
ndipo adzakudyera zako zonse mtima uli zii.
6Akamakusoŵa iweyo, amakubwatika,
amakusekerera nkukulimbitsa mtima.
Amakulankhula mwaulemu nkukuuza kuti,
“Kodi ndingakuthandizeni?”
7Adzakuchititsa manyazi ndi maphwando ake,
mpaka atakokolola zako zonse moŵirikiza,
potsiriza nkumakuseka.
Pambuyo pake atakuwona adzakuthaŵa,
nkumangopukusa mutu mokunyodola.
8Uchenjere kuti angakubwatike,
pambuyo pake iwe nkunyozeka ndi kupusa kwako.
9Munthu wotchuka akakuitana kunyumba kwake,
usavomere msanga,
pamenepo adzabwerezabwereza kukuitanako.
10Usafulumire kunka patsogolo,
kuwopa kuti angakubweze pambuyo.
Komanso usanyanye kukhala pakati,
mwina nkudzakuiŵala.
11Usamamuyese ngati mnzako wolingana naye,
usakhulupirire kuchuluka kwa mau ake.
Kuchulukitsa mauko nkukuyesa chabe,
kukusekererako nkukupima chabe.
12Munthu wosasunga chinsinsi ngwankhanza,
sadzaopa kukupweteketsa ndi kukumangitsa.
13Tsono zachinsinsi zako uzisunge mu mtima
ndipo ukhale tcheru,
chifukwa chiwonongeko chako umayenda nacho limodzi.
14Ukamva zimenezi uli m'tulo, dzuka.
Uzikonda Ambuye pa moyo wako wonse,
uŵapemphe kuti akupulumutse.
15Cholengedwa chamoyo chilichonse chimakonda
mtundu wake,
munthunso amakonda anzake.
16Zolengedwa zonse zimayenderana pa mtundu wake,
munthunso amagwirizana ndi anthu onga ngati iyeyo.
17Monga mmbulu ndi mwanawankhosa sizingayanjane,
chimodzimodzinso munthu wochimwa ndi munthu wolungama.
18Monga pakati pa fisi ndi galu sipangakhale mtendere,
chimodzimodzinso pakati pa munthu wolemera ndi
munthu wosauka.
19Monga momwe mikango imadyera mbidzi ku chipululu,
momwemonso munthu wolemera amadyera masuku pa
mutu munthu wosauka.
20Munthu wonyada amadana ndi kudzichepetsa,
ndipo wolemera amanyansidwa ndi kusauka.
21Munthu wolemera akamadzandira,
abwenzi ake amamgwirira.
Koma munthu wosauka akagwa,
ndi abwenzi ake omwe amamkankhira kumbali.
22Munthu wolemera akaterereka,
anthu ambiri amamthandiza.
Ngakhale alankhule zopusa,
anthu amamuyamikabe.
Munthu wosauka akaterereka,
anthu amamdzudzula.
Ngakhale alankhule zanzeru,
anthu sasamalako.
23Munthu wolemera akamalankhula,
anthu onse amakhala chete,
amanka natamanda mau ake konsekonse.
Munthu wosauka akamalankhula,
anthu amati, “Kodi ndaninso ameneyu?”
Ndipo akangophunthwa,
anthunso amamkankhira pansi.
24Kulemera nkwabwino ngati munthu sikumchimwitsa.
Anthu osadziŵa Mulungu amati
kusauka ndi chinthu choipa.
25Nkhope ya munthu imasinthika
malinga ndi mtima wake,
mwina imaoneka bwino mwina ai.
26Nkhope yosangalala ndiye chizindikiro cha mtima wokondwa.
Koma kupeka miyambi ndi ntchito yotopetsa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.