13Mau a m'kalatayo ankayenera kudziŵika m'dera lililonse kuti ndi lamulo ndithu. Motero adayenera kuŵalengeza kwa anthu a mitundu yonse. Choncho Ayuda adayenera kukonzekera kuti alipsire adani ao tsiku limenelo.
14Tsono anthu amtokomawo adakwera akavalo ao othamanga kwambiri, amene ankaŵagwiritsa ntchito potumikira mfumu. Adathamanga mofulumira, mfumu itaŵalamula kutero. Ndipo lamulolo adalilengeza mu mzinda wa Susa, likulu la dzikolo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.