Lun. 17 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mdima wa ku Ejipito ndi mtambo waŵala

1Maweruzo anu ngapatali ndi osafotokozeka,

nchifukwa chake mitima yosaphunzira idasokera.

2Pamene anthu osamvera aja ankaganiza

kuti tsopano azunza anthu anu mu ukapolo,

eniakewo anali okodwa ndi mdima

ndi omangidwa mu usiku wautali.

Anali ngati otsekedwa m'nyumba mwao

ndi osoŵa chisamaliro chamuyaya cha Mulungu.

3Pamene ankaganiza kuti machimo ao,

amene adaŵachita paseri,

anali osadziŵika ndi oiŵalika,

monga zinthu zochitikira kobisika,

eniakewo adamwazikana ndi kuchita mantha kwambiri,

ndipo adavutika poona mizukwa.

4Ngakhale m'chipinda m'mene adaathaŵiramo

sadaleke kuchita mantha,

chifukwa phokoso lodabwitsa

linkamveka ponse pozungulira.

Ndipo mizukwa yoopsa ya nkhope zoipa inkaŵaonekera.

5Moto unalibenso mphamvu zoŵaunikira,

ngakhale kuŵala kwa nyenyezi

kudalephera kuŵalitsa usiku woopsawo.

6Chokhacho chimene chinkaŵaonekera

chinali moto woopsa, wobuka wokha,

ndipo maonekedwe ake akamazimirira,

chifukwa cha mantha

ankayesa kuti zimene ankaziwonazo,

zinali zoipa koposa.

7Luso lao lamatsenga lidaoneka lopandapake,

ndipo amene ankadziyesa anzeru,

adatsutsidwa mochititsa manyazi.

8Iwo ankati adzachiritsa mitima yamantha

ndi yoda nkhaŵa,

koma ndiwo amene adadwala ndi mantha opusa.

9Chifukwa ngakhale kunalibe kanthu koti

nkuŵachititsa mantha,

komabe zilombo zongoyenda ndi njoka zolira mozaza

zinkaŵaopsa,

10ndipo ankangouma ndi mantha;

ankayesa kuleka nkuphenyula maso komwe,

koma kunali kosatheka.

11Anthu ochimwa kaŵirikaŵiri ndi amantha

umboni wao womwe umaŵatsutsa.

Munthu woipa,

mtima wake umamvuta ndi kukuza zomusautsa.

12Mantha si kanthu kena

koma kulephera kulandira chithandizo

chochokera ku luntha.

13Ndipo kusoŵa chithandizoku kukakula,

kumaonjeza mantha a anthu

osadziŵa chimene chikudzetsa zoŵazunza.

14Iwo aja ankagona tulo timodzimodzi

nthaŵi yonse ya mdima

umene unkafumira ku dziko lozama la akufa,

kwenikweni mdimawo unalibe mphamvu pa iwo.

15Koma iwo mwina ankayesa kuti

mizukwa yoopsa ikuŵapirikitsa.

Mwinanso thupi lao linkauma ndi kusoŵa mphamvu,

chifukwa mantha adzidzidzi ndi osadziŵika ankaŵagwera.

16Tsono aliyense amene anali pamenepo ankagwa pansi,

anali ngati womangidwa m'ndende yopanda chitseko.

17Ngakhale mlimi, kapena mbusa,

kapenanso munthu wogwira ntchito m'thengo,

onsewo zoipazo zidaŵagwera,

sadathe konse kuzilewa,

chifukwa onse adaamangidwa ndi unyolo umodzi

wa mdima womwewo.

18Kuwomba kwa mphepo, kuimba kokoma kwa mbalame

pa nthambi zogudira,

mkokomo wa madzi oyenda mwamphamvu,

19kapena phokoso lomveka kutali

la mathanthwe ogumuka,

kuthamanga kwa nyama zolumpha koma zosaoneka,

kubangula kwa zilombo zoopsa,

ndiponso mamvekera omveka m'mapanga a mapiri,

zonsezo zidaŵaumitsa ndi mantha.

20Nthaŵi imeneyo pa dziko lapansi pano

panali kuŵala kokoma,

ndipo anthu ankagwira ntchito zao mosavutika.

21Ochimwa okha anali pakati pa mdima wandiweyani,

umene unkafanizira mdima wodzaŵagwera tsiku lina.

Komabe iwo omwe ankadzilemeza koposa mdimawo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help