1Pemphero la mneneri Habakuku
potsata maimbidwe a Sigionoti.
2Inu Chauta, ndamva za mbiri yanu,
Inu Chauta, ntchito zanu zandiwopsa.
Muzichitenso masiku ano,
zikhale zodziŵika makono.
Ngakhale muli okwiya, musaiŵale chifundo chanu.
3Mulungu adabwera kuchokera ku Temani,
Woyera uja adabwera kuchokera ku phiri la Parani.
Ulemerero wake udaphimba mlengalenga,
dziko lonse lapansi linkamutamanda.
4Adaŵala ngati dzuŵa,
kunyezimira kunkatuluka m'manja mwake,
m'mene adabisamo mphamvu zake.
5Kutsogolo kwake kudagwa mliri,
kumbuyo kwake kudagwa nthenda yoopsa.
6Adaimirira ndipo dziko lapansi lidagwedezeka.
Adayang'ana ndipo mitundu ya anthu idanjenjemera.
Pomwepo mapiri okhazikika adagumuka,
ndipo magomo akalekale adatera,
njira zake nzachikhalire.
7Ndidaona anthu a ku Kusani ali pa mavuto,
nawonso a ku Midiyani adaagwedezeka.
8Inu Chauta, kodi mudaakwiyira mitsinje?
Kodi mudaakalipira mifuleni?
Kodi mudaazazira nyanja?
Mutakwera pa akavalo anu
mudapambanitsa anthu anu pa nkhondo.
9Mudasolola uta wanu m'chimake,
ndipo mudatulutsa mivi m'phodo lake.
Mudang'amba dziko lapansi ndi mitsinje.
10Mapiri atakuwonani adayamba kugwedezeka.
Madzi amphamvu am'mitsinje adasefukira.
Nyanja yozama idakokoma,
mafunde ake adakwera kwambiri.
11Dzuŵa ndi mwezi zidangoti jega mu mlengalenga,
zitaona kung'anipa kwa mivi yanu,
ndi kunyezimira kwa mikondo yanu.
12Mudayendayenda m'dziko lapansi muli okwiya,
mudapondereza anthu a mitundu yonse mwaukali.
13Mudapita kukapulumutsa anthu anu,
mudabwera kudzalanditsa wodzozedwa wanu.
Mudakantha mtsogoleri wa dziko la anthu oipa,
mudaonongeratu anthu ake onse.
14Ndi mivi yanu mudalasa mtsogoleri wa ankhondo ake,
amene adaabwera ngati kamvulumvulu kuti atibalalitse.
Ankakondwerera ngati kuti akudzaononga
osauka mwachinsinsi.
15Mudapondaponda pa nyanja ndi akavalo anu,
ndipo madzi amphamvu adavwanduka.
16Izi ndazimva, ndipo thupi langa likunjenjemera,
m'kamwa fuu chifukwa cha phokosolo.
M'mafupa mwazizira,
ndipo maondo akuwombana.
Ndikudikira tsiku la chilango
chimene chidzagwera amene akutithira nkhondo.
17Ngakhale mikuyu ipande kuchita maluŵa,
mipesa ipande kukhala ndi mphesa,
mitengo ya olivi ipande kubala zipatso,
m'minda musatuluke kanthu,
ndipo nkhosa ndi ng'ombe zithe m'khola,
18komabe kwanga nkukondwerera mwa Chauta,
kwanga nkusangalala
chifukwa cha Mulungu Mpulumutsi wanga.
19 2Sam. 22.34; Mas. 18.33 Ambuye anga, Chauta, ndiwo amandipatsa mphamvu.
Amalimbitsa miyendo yanga
kuti ikhale ngati ya mbaŵala,
kuti ndikafike mpaka pamwamba pa phiri.
Kwa Woimbitsa nyimbo. Aimbire zazingwe.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.