2 Mbi. 8 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ntchito zina za Solomoni(1 Maf. 9.10-28)

1Ntchito yomanga Nyumba ya Chauta ndi nyumba ya mfumu idamtengera Solomoni zaka makumi aŵiri.

2Pambuyo pake adamanganso kachiŵiri mizinda imene Huramu adampatsa, nakhazikamo Aisraele.

3Kenaka Solomoni adapita ku Hamatizoba nakaulanda mzindawo.

4Adakamanga Tadimori ku chipululu, ndiponso mizinda yosungirako chuma, imene adakaimanga ku Hamati.

5Adamanganso Betehoroni wakumtunda ndi Betehoroni wakunsi, mizinda yamalinga yokhala ndi makoma, zitseko ndi mipiringidzo.

6Adamanganso Baalati ndiponso mizinda yonse yosungiramo zinthu zimene anali nazo, mizinda yonse yosungiramo magaleta ake, ndi ina yomakhalamo anthu ake okwera pa akavalo, ndi zonse zimene Solomoni adafuna kuti amange ku Yerusalemu, ku Lebanoni ndi ku madera onse amene Solomoni ankaŵalamulira.

7Koma analipo anthu ena otsalira a mitundu yosiyanasiyana: Ahiti, Aamori, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. Ameneŵa sanali Aisraele,

8ndiye kuti zidzukulu zao zidaatsalira m'dzikomo, Aisraele ataloŵamo. Onsewo Aisraele sadaŵaononge. Anthu ameneŵa Solomoni ankaŵagwiritsa ntchito yathangata. Ndipo akugwirabe ntchito imeneyo mpaka lero lino.

9Koma Aisraele Solomoni sankaŵagwiritsa ntchito yaukapolo. Iwowo anali anthu ake ankhondo, nduna zake, oyang'anira magaleta ake ndi anthu ake okwera pa akavalo.

10Ndipo akuluakulu a mfumu Solomoni analipo 250 amene ankalamulira anthu.

11Solomoni adatenga mwana wamkazi wa Farao ku mzinda wa Davide, nabwera naye ku nyumba imene adamangira mkaziyo, poti Solomoniyo ankati, “Mkazi wanga asamakhale m'nyumba ya Davide mfumu ya Israele, chifukwa chakuti malo amene kwafikira Bokosi lachipangano la Chauta ngopatulika.”

12Kenaka Solomoni adapereka nsembe zopsereza kwa Chauta pa guwa la Chauta limene adalimanga patsogolo pa khonde lapoloŵera,

13Num. 28.9, 10; Num. 28.11-15; Eks. 23.14-17; 34.22, 23; Num. 28.16—29.39; Deut. 16.16 monga momwe zinkafunikira pa tsiku lililonse. Ankapereka potsata malamulo a Mose okhudza masiku a Sabata, masiku a pokhala mwezi watsopano, ndiponso masiku achikondwerero atatu a chaka ndi chaka: Chikondwerero cha buledi wosafufumitsa, chikondwerero cha masabata ndiponso chikondwerero cha mahema.

14Potsata malangizo a Davide bambo wake, adagaŵa ansembe m'magulumagulu ndi kuŵapatsa ntchito zao. Adaikanso magulu a Alevi ndi kuŵapatsa ntchito yao yoimba nyimbo zotamanda Mulungu ndi yotumikira ansembe, monga momwe ntchito ya tsiku lililonse inkafunikira. Magulu a alonda apazipata adaŵagaŵira udindo wao pa chipata chilichonse. Paja Davide, munthu wa Mulungu, anali atalamula motero.

15Ndipo anthu sadapatukepo pa zimene mfumu idaalamula ansembe ndi Alevi, zokhudza zinthu zonsezi ndiponso zokhudza nyumba zosungiramo chuma.

16Motero ntchito zonse za Solomoni zidatha, kuyambira pamene maziko a Nyumba ya Chauta adaikidwa mpaka pamene ntchitoyo idatha. Choncho Nyumba ya Chauta idatheratu.

17Pambuyo pake Solomoni adapita ku Eziyoni-Gebere ndi ku Elati kumphepete kwa nyanja, ku dziko la Edomu.

18Tsono mfumu Hiramu adamtumizira zombo ndi anyamata ake amene ankadziŵa za zapanyanja. Anthuwo adapita ku Ofiri, pamodzi ndi anyamata a Solomoni, ndipo adakatengako golide wa makilogramu 18,000, nabwera naye kwa mfumu Solomoni.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help