1Mzinda umene Chauta adamanga maziko ake,
uli pa phiri loyera.
2Chauta amakonda mzinda wa Ziyoni
amaukonda kupambana kwina kulikonse
kumene zidzukulu za Yakobe zimakhala.
3Iwe mzinda wa Mulungu,
anthu amakamba zambiri zotamanda iwe.
4Amati, “Pakati pa amene amandidziŵa,
ndikutchula Rahabu ndi Babiloni.
Ponena za dziko la Filistiya, Tiro ndi Etiopiya,
anthu amati, ‘Uje adabadwira kumeneko.’ ”
5Koma ponena za Ziyoni adzati,
“Onse adabadwira kumeneko,”
chifukwa Wopambanazonse mwini wake
ndiye amene adzaulimbitsa mzindawo.
6Tsono polemba maina a mitundu yonse ya anthu,
Chauta adzati,
“Wakutiwakuti adabadwira ku Ziyoni.”
7Oimba ndi ovina adzati,
“Ziyoni ndiwe kasupe wa madalitso athu onse.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.