Mphu. 12 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Malangizo okhudza ntchito zabwino

1 Mt. 7.6 Ukafuna kuchitira wina zabwino,

usankhule munthu woyenerera,

ukatero zabwino zakozo sizidzapita pachabe.

2Ukachitira zabwino munthu wokonda Mulungu,

udzalandira mphotho.

Ngati sadzakupatsa ndi munthuyo,

mosapeneka konse adzakupatsa ndi Mulungu

Wopambanazonse.

3Sangapeze zabwino munthu woumirira zoipa,

kapena munthu wosathandiza osauka.

4Uzithandiza munthu woopa Mulungu,

koma osati munthu wochimwa.

5Uzichitira zabwino munthu wodzichepetsa,

koma osampatsa kanthu munthu wosalabadira za Mulungu.

Ummane chakudya, usampatse konse,

kuwopa kuti angadzasanduke wamphamvu koposa iwe.

Adzakubwezera zoipa moŵirikiza

pamalo pa zabwino zonse zimene udamchitira.

6Mulungu Wopambanazonse amadana ndi ochimwa,

adzalanga anthu onse okonda zoipa.

7Munthu wabwino umpatseko kanthu,

koma wochimwa osamthandiza.

Za abwenzi oona ndi onyenga

8Ukakhala pabwino, abwenzi ako enieni sadziŵika,

koma ukakhala pa mavuto adani ako sachedwa kudziŵika.

9Zonse zikamakuyendera bwino, adani ako amamva chisoni,

koma pa nthaŵi ya mavuto, ngakhale abwenzi ako atha kukusiya.

10Mdani wako usamkhulupirire konse,

ali ndi chiwembu ngati dzimbiri pa chitsulo.

11Akamaoneka modzichepetsa, namachita gwadugwadu,

iwe ungoti phee, nkukhala maso.

Uchite ngati ukupukuta kalilole, udzaona kuti

kuthimbirira kwake nkosakhalitsa.

12Usakhale naye pafupi, kuwopa kuti angakukankhe

nkutenga malo ako.

Usamkhazike ku dzanja lako lamanja,

kuwopa kuti angakulande mpando wako.

Tsono potsiriza pake udzadziŵa kuti mau anga anali oona,

ndipo udzanong'oneza bondo poŵakumbukira.

13Kodi woseŵera ndi njoka amamumvera chisoni

ndani ikamuluma?

Woputa dala chilombo cholusa amamumvera chisoni

ndani chikamuluma?

14Palibe amene amamchitira chisoni

munthu woyenda ndi anthu oipa

kapena wothandizana nawo pa zoipa.

15Iye uja angathe kukhala nawe kanthaŵi pang'ono,

koma ukagwa m'zovuta, sadzakhala nawenso.

16Pakamwa pa mdani pamalankhula zabwino,

pamene mumtima mwake akuganiza zokuponya m'mbuna.

M'maso mwake misozi ili mbwembwembwe,

koma akapeza mpata, kupha sayesa kanthu.

17Tsoka likakugwera,

udzamupeza akukutsogolera,

amaoneka ngati akufuna kukuthandiza,

koma adzakutchera ndale kuti ugwe.

18Pamenepo adzasanduka wina,

adzapukusa mutu,

adzachita kuti m'manja lya!

Nkuyamba kuchita miseche.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help