Yes. 16 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kuzingwa kwa Amowabu

1Amowabu atumiza mphatso ya mwanawankhosa

kwa wolamulira dziko.

Iwo achokera ku mzinda wa Sela,

adzera njira ya chipululu

mpaka kukafika ku phiri la Ziyoni.

2Monga momwe mbalame zimaulukira uku ndi uku

akazimwaza m'chisa,

momwemonso akazi a ku Mowabu

akuyendayenda ku madooko a Arinoni.

3Akuuza anthu a ku Yuda kuti,

“Mutiwuze chochita,

gamulani zoti tichite.

Pamene dzuŵa lili pa liwombo,

mutipatse mthunzi wabii ngati mdima.

Mutibise ife anthu opirikitsidwa,

musatipereke ife anthu othaŵa nkhondo.

4Othaŵa nkhondo a ku Mowabu azikhala pakati panu.

Mukhale populumukira pao kwa woononga uja.”

Nthaŵi ikudza pamene kupsinja

sikudzakhalaponso,

kuwononga kudzaleka,

ndipo amene amaŵapondereza adzachoka m'dzikomo.

5Pamenepo mpando wachifumu

udzakhazikitsidwa mwachikondi,

mmodzi mwa zidzukulu za Davide

adzakhalapo mokhulupirika.

Iyeyo poweruza adzatsata zachilungamo,

ndipo adzalimbikira kuchita zaungwiro.

6Anthu a ku Yuda akunena kuti,

“Kudzikuza kwa Amowabu takumva,

adadzikuza kwambiri.

Kudzitukumula kwao, kunyada kwao,

kunyodola kwao ndi kudzitama kwao,

zonse nzachabechabe.”

7Nchifukwa chake alekeni Amowabu alire kwambiri,

onsewo alire fuko lao,

Alire motaya mtima chifukwa cha makeke amphesa

amene ankadya ku Kiri-Haresefi.

8Paja minda ya ku Hesiboni idaguga,

yatha pamodzi ndi minda yamphesa ya ku Sibima.

Mphesa zake zinkaledzeretsa

olamulira anthu a mitundu ina.

Kale nthambi zake zinkafika mpaka ku

Yazere ndi ku chipululu,

ndiponso mpaka kutsidya kwa nyanja.

9Nchifukwa chake ndikulira monga m'mene

akulirira anthu a mu mzinda wa Yezere

chifukwa cha minda yamphesa ya ku Sibima.

Inu anthu a ku Hesiboni ndi Eleale

ndikukunyowetsani misozi chifukwa choti

mwalephera kupeza zokolola,

kaamba ka nkhondo imene yaononga zonse.

10Kukondwa ndi kusangalala kwalekeka ku

minda yadzinthu. Nyimbo sizikuimbidwa,

palibenso kufuula m'minda yamphesa.

Palibe wopsinya vinyo mopondera mphesa,

kufuula kwachimwemwe kwa nthaŵi yotchera

mphesa kwalekeka.

11Nchifukwa chake moyo wanga ukulira ngati pangwe,

kulira Mowabu,

mtima wanga ukubuula

chifukwa cha kuwonongeka kwa Kiriheresi.

12Ngakhale Amowabu akudzipereka pakupita ku akachisi ao namakapemphera mpaka kutopa, zimenezo sizidzaŵapindulira kanthu.

13Mau ameneŵa ndiwo amene adalankhula Chauta kalekale kunena za Mowabu.

14Koma tsopano akunena kuti, “Zisanathe zaka zitatu, potsata m'mene amaŵerengera munthu waganyu, ulemerero wa Mowabu udzakhala utatheratu. Chigulu chachikulu cha anthu ake chidzaonongeka, ndipo opulumukapo adzakhala ochepa ndi ofooka.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help