1Inu Mulungu, patsaniko mfumu nzeru zoweruzira,
patsaniko mwana wa mfumu mtima wokonda chilungamo.
2Motero mfumuyo idzaweruza anthu anu molungama
ndiponso anthu anu osauka mosakondera.
3Mapiri adzabweretsa madalitso kwa anthu,
magomo adzadzetsa mphotho ya chilungamo.
4Mfumu idzateteza anthu osauka,
idzapulumutsa anthu osoŵa,
koma idzaononga anthu ozunza anzao.
5Idzakhala moyo pa mibadwo yonse,
nthaŵi zonse pamene dzuŵa ndi mwezi zikuŵala
mu mlengalenga.
6Idzakhala madalitso
ngati mvula yogwa pa minda
ngati mvula yowaza pa nthaka!
7Pa masiku ake chilungamo chidzakula,
mtendere udzachuluka, mpaka mwezi utaleka kuŵala!
8 mpaka ku mathero a dziko.
9Amaliwongo akuchipululu adzaiŵeramira,
adani ake adzadya fumbi.
10Mafumu a ku Tarisisi ndi akuzilumba adzaipatsa mitulo,
mafumu a ku Sheba ndi a ku Seba adzabwera ndi mphatso.
11Mafumu onse adzaigwadira
ndipo mitundu yonse ya anthu idzaitumikira.
12Ndithu iyo idzalanditsa anthu osoŵa amene amaiitana,
idzapulumutsa anthu osauka ndiponso opanda woŵathandiza.
13Idzamvera chisoni anthu ofooka ndi osoŵa,
ndipo idzapulumutsa moyo wa anthu aumphaŵi.
14Idzaombola moyo wao kwa anthu oŵapsinja
ndi kwa oŵachita zankhanza,
pakuti magazi ao ndi amtengowapatali pamaso pake.
15Ikhale ndi moyo wautali!
Golide wa ku Sheba apatsidwe kwa mfumuyo.
Anthu aipempherere nthaŵi zonse,
aipemphere madalitso kosalekeza.
16M'dziko mukhale chakudya chambiri,
pamwambanso pa mapiri pakhale dzinthu.
Zipatso zake zichuluke ngati za ku Lebanoni,
anthu ake achuluke m'mizindamo ngati udzu wakuthengo.
17Dzina lake lisaiŵalike konse,
mbiri yake ikhalepobe
monga momwe limakhalira dzuŵa.
Anthu alandire madalitso chifukwa cha iyo,
a mitundu yonse aitche yodala.
18Atamandike Chauta, Mulungu wa Israele.
Iye yekha ndiye amene amachita zinthu zodabwitsa.
19Dzina lake laulemerero litamandike mpaka muyaya.
Ulemerero wake udzaze dziko lonse lapansi.
Inde momwemo. Inde momwemo.
20Ano ndiwo mathero a mapemphero a Davide,
mwana wa Yese.
BUKU LACHITATU(Mas. 73—89)Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.