1Yehosafati adamwalira, naikidwa m'manda momwe adaaikidwa makolo akewo mu mzinda wa Davide. Tsono Yehoramu mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Yehoramu aloŵa ufumu(2 Maf. 8.17-24)2Abale ake, ana a Yehosafati, anali aŵa: Azariya, Yehiyele, Zekariya, Azariyahu, Mikaele ndi Sefatiya. Onseŵa anali ana a Yehosafati, mfumu ya ku Yuda.
3Atate ao adaaŵapatsa mphatso zambiri za siliva, golide, ndi zinthu zamtengowapatali, pamodzi ndi mizinda yamalinga ya ku Yuda. Koma ufumu adapatsa Yehoramu, chifukwa chakuti anali mwana wachisamba.
4Yehoramu ataloŵa ufumu, nakhazikika pa mpando waufumu wa atate akewo, adapha abale ake onse ndi lupanga, ngakhalenso atsogoleri ena a ku Israele.
5Yehoramu anali wa zaka 32 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka zisanu ndi zitatu ku Yerusalemu.
6Ankatsata makhalidwe a mafumu a ku Israele, monga m'mene linkachitira banja la Ahabu, pakuti adaakwatira mwana wa Ahabu. Tsono ankachita zoipa zilizonse pamaso pa Chauta.
71Maf. 11.36 Komabe Chauta sadafune kuononga banja la Davide, chifukwa cha chipangano chimene adaachita ndi Davide, ndiponso poti adaalonjeza kuti adzampatsa nyale Davide ndi zidzukulu zake mpaka muyaya.
8Gen. 27.40 Pa nthaŵi yakeyo anthu a ku Edomu adaukira ulamuliro wa Yuda, ndipo adadzisankhira mfumu yao.
9Tsono Yehoramu adapita pamodzi ndi atsogoleri ake ankhondo ndi magaleta ake onse. Adanyamuka usiku nakaŵakantha Aedomu amene adaamzinga iyeyo pamodzi ndi atsogoleri a magaleta ake.
10Choncho Aedomu ngoukira ulamuliro wa Yuda mpaka lero lino. Pa nthaŵi imeneyo, mzinda wa Libina nawonso udaukira ulamuliro wa Yehoramuyo, chifukwa chakuti adaasiya Chauta, Mulungu wa makolo ake.
11Kubzolera pamenepo adayambitsa akachisi opembedzerako mafano ku dziko lamapiri la ku Yuda, ndipo adatsogolera anthu a ku Yerusalemu kuti akhale osakhulupirika, nasokeza anthu a ku Yuda.
12Tsono adalandira kalata kwa mneneri Eliya, yonena kuti, “Chauta, Mulungu wa Davide, kholo lanu, akunena kuti, ‘Sudatsate chitsanzo cha Yehosafati bambo wako, kapenanso cha Asa, mfumu ya ku Yuda,
13koma watsata chitsanzo cha mafumu aku Israele. Watsogolera anthu a ku Yuda pamodzi ndi anthu a mu Yerusalemu kuti akhale osakhulupirika, monga m'mene linkachitira banja la Ahabu pochimwitsa anthu a ku Israele. Wapha abale ako a pa banja la atate ako, amene anali abwino kupambana iwe.
14Chifukwa cha zonsezi Chauta adzaŵagwetsera mliri anthu ako, ana ako, akazi ako, ndi zinthu zako zonse.
15Ndipo iweyo udzadwala nthenda yoopsa ya m'mimba imene izidzakulirakulira tsiku ndi tsiku mpaka matumbo ako adzasololoka.’ ”
16Tsono Chauta adamuutsira Yehoramuyo mkwiyo wa Afilisti ndi mkwiyo wa Arabu amene ali pafupi ndi Aetiopiya.
17Motero iwowo adadzalimbana ndi anthu a ku Yuda naŵathira nkhondo. Ndipo adalanda zinthu zonse zimene adazipeza ku nyumba ya mfumu, pamodzinso ndi ana ake aamuna ndi akazi ake, kotero kuti panalibe mwana ndi mmodzi yemwe wamwamuna amene adatsala, kupatula Ahaziya mzime wake.
18Pambuyo pake Chauta adamkantha ndi nthenda ya m'mimba yosachizika.
19Patapita nthaŵi ndithu, pomatha chaka chachiŵiri, matumbo ake adayamba kusololoka chifukwa cha nthendayo, ndipo adafa imfa yopweteka kwambiri. Anthu sadasonkhe moto kuti amchitire ulemu monga m'mene ankachitira ndi makolo ake.
20Iyeyo anali wa zaka 32 pamene ankayamba ufumu wake, ndipo adalamulira zaka zisanu ndi zitatu ku Yerusalemu. Adafa popanda munthu womumvera chisoni. Adamuika mu mzinda wa Davide, koma osati m'manda a mafumu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.