Daniel Greek 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nebukadinezara alamula aliyense kuti apembedze fano lagolide

1Nthaŵi ina mfumu Nebukadinezara adapangitsa fano lagolide. Msinkhu wake unali mamita 27, m'mimba mwake mamita atatu. Adaliimika m'chigwa cha Dura, m'dera la Babiloni.

2Tsono adatumiza mau kuti asonkhanitse akalonga, abwanamkubwa, nduna, aphungu, asungachuma, oweruza milandu, anyakwaŵa, ndi akulu ena onse a madera a dzikolo, kuti abwere kudzachita mwambo wozulula fano limene mfumu Nebukadinezara adaliimika.

3Motero akuluakulu onse aja, akalonga, abwanamkubwa, nduna, aphungu, asungachuma, oweruza milandu ndi anyakwaŵa, adasonkhana pamodzi pamaso pa fano limene mfumu Nebukadinezara adaliimika.

4Tsono mlaliki adalengeza mokweza mau kuti, “Inu anthu a mitundu yonse, a zilankhulo zosiyanasiyana, mukulamulidwa kuti

5pamene mudzamva kulira kwa mbetete, chitolilo, zeze, nsansi, pangwe, mngoli, ndi kuimba kwamtundumtundu, mudzadzigwetse chafufumimba, ndipo mudzapembedze fano lagolide limene mfumu Nebukadinezara adaliimika

6Aliyense amene sadzadzigwetsa chafufumimba ndi kupembedza fanolo, adzaponyedwa m'ng'anjo yamoto.”

7Motero anthu onse atangomva kulira kwa zoimbaimba zija, adadzigwetsa chafufumimba, ndipo adapembedza fano lagolide limene mfumu Nebukadinezara adaaliimika.

Ayuda atatu aŵazenga mlandu

8Nthaŵi imeneyo Ababiloni ena oipa mtima adapezerapo danga loti adzaneneze Ayuda.

9Adauza mfumu Nebukadinezara kuti, “Mukhale ndi moyo wautali, amfumu.

10Inu amfumu, mwalamula kuti munthu aliyense akamva kulira kwa mbetete, chitolilo, zeze, nsansi, pangwe, mngoli, ndi kuimba kwamtundumtundu adzigwetse chafufumimba, ndipo apembedze fano lagolideli.

11Ndipo amene sachita zimenezo, aponyedwe m'ng'anjo yamoto.

12Pali Ayuda ena, Sadrake, Mesaki ndi Abedenego amene mudaŵaika kuti aziyang'anira ntchito za dera la Babiloni. Anthu ameneŵa inu mfumu sasamala lamulo lanu, satumikira milungu yanu, ndipo sapembedza fano lagolide lija limene mudaliimika.”

13Tsono Nebukadinezara adapsa mtima kwambiri, naitanitsa Sadrake, Mesaki ndi Abedenego. Ndipo adabwera nawo pamaso pa mfumu.

14Nebukadinezara adaŵafunsa kuti, “Inu, Sadrake, Mesaki ndi Abedenego, kodi nzoona kuti simutumikira milungu yanga ndi kupembedza fano lagolide lija limene ndidaliimika?

15Ngati muli okonzeka kuti mukangomva kulira kwa mbetete, chitolilo, zeze, nsansi, pangwe, mngoli, ndi kuimba kwa mtundumtundu, mudzigwetse chafufumimba ndi kupembedza fano limene ndaliimika, chabwino. Koma mukapanda kulipembedza, muponyedwe m'ng'anjo yamoto. Ndipo palibe mulungu wina aliyense amene akupulumutseni m'manja mwanga.”

16Sadrake, Mesaki ndi Abedenego adauza mfumu Nebukadinezara kuti, “Sikofunikira kuti tikuyankheni pa nkhani imeneyi.

17Mulungu amene timamtumikira ife angathe kutipulumutsa ku ng'anjo yamoto ndiponso m'manja mwanu, amfumu.

18Koma ngakhale Mulungu wathuyo asatipulumutse, mudziŵe amfumu kuti sitidzatumikirabe milungu yanu, ndi kupembedza fano lagolidelo limene mudaliimika.”

Abwenzi atatu a Daniele aponyedwa m'ng'anjo yamoto

19Pamenepo mfumu Nebukadinezara adapsera mtima Sadrake, Mesaki ndi Abedenego, ndipo nkhope yake idasandulika ndi ukali. Adalamula kuti ng'anjo yamoto aisonkhezere kasanunkaŵiri kupambana masiku onse.

20Adalamulanso ena mwa anthu ake amphamvu a gulu lake lankhondo kuti amange Sadrake, Mesaki ndi Abedenego ndi kuŵaponya m'ng'anjo yamotoyo.

21Tsono asilikali adamanga anyamata atatuwo ndi kuŵaponya m'ng'anjo yamoto ali ndi zovala zao zonse, mikanjo, miinjiro, zisoti ndi zovala zina zonse.

22Chifukwa choti lamulo la mfumulo linali lofulumiza, ndipo ng'anjo yamotoyo inali yotentha kwambiri, asilikali amene adanyamula Sadrake, Mesaki ndi Abedenego adaphedwa ndi malaŵi amene ankatuluka m'ng'anjomo.

23Tsono anyamata atatuwo, Sadrake, Mesaki ndi Abedenego adagwa pakati pa ng'anjo yamotoyo ali omangidwa.

Pemphero la Azariya ndi Nyimbo ya anyamata atatu

24Anyamata atatuwo ankayenda pakati pa moto akuimbira Mulungu nyimbo ndi kutamanda Ambuye.

25Tsono Azariya ali chiimire pakati pa moto adayamba kupemphera ndi mau omveka, adati,

26“Mutamandike, Inu Ambuye,

Mulungu wa makolo athu,

ndinu oyenera kukutamandani.

Dzina lanu ndi loyenera kulilemekeza

mpaka muyaya.

27Paja ndinu achilungamo

pa zonse zimene mudatichitira.

Ntchito zanu ndi zoona,

njira zanu ndi zolungama,

ndipo mumaweruza moona.

28Chilango chonse chimene mudachigwetsa

pa ife ndi pa Yerusalemu,

mzinda wopatulika wa makolo athu,

chinali cholungama.

Ndithu mudatiweruza molungama ndi moona

pa machimo athu.

29Zoonadi tidachimwa

ndi kuswa malamulo anu pokupandukirani.

Pa zochita zathu zonse tidachimwa kwambiri,

sitidamvere malamulo anu.

30Sitidaŵasamale malamulowo,

sitidaŵasunge.

Sitidachite zimene mudatilamula

pofuna kuti tikhale pabwino.

31“Pa zilango zonse zimene mudagwetsa pa ife,

pa zonse zimene mudatichita,

kuweruza kwanu kunali kolungama.

32Mudatipereka kwa adani athu,

anthu oipadi opandukira malamulo anu,

ndi kwa mfumu yoipa kopambana m'dziko lapansi.

33Tsopano sitingathenso kunena kanthu

chifukwa cha manyazi.

Manyozo atigwera ife

amene timatumikira Inu ndi kukupembedzani.

34Chonde musatisiye mpaka muyaya,

musaphwanye chipangano chanu ndi ife,

kuti dzina lanu lilemekezedwe.

35Musaleke kutichitira chifundo,

malinga ndi zimene mudalonjeza Abrahamu,

wokondedwa wanu,

Isaki mtumiki wanu,

ndi Israele munthu wanu wosankhidwa.

36Paja mudaaŵalonjeza

kuti mudzachulukitsa zidzukulu zao

ngati nyenyezi zamumlengalenga,

kapena ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja.

37Koma tsopano Ambuye,

ife tasanduka ochepa kwambiri

kupambana mitundu ina yonse ya anthu.

Pa dziko lonse lapansi ndife onyozeka

chifukwa cha machimo athu.

38Pali pano tilibe mfumu,

mneneri kapena mtsogoleri.

Sitikuperekanso zopereka zootcha

kapena nsembe kapena mphatso kapena zofukiza,

ndipo tilibe malo operekerako nsembe kwa Inu,

kuti mutichitire chifundo.

39Koma poti tabwera kwa Inu

ndi mtima wolapa ndi wodzichepetsa,

mutilandire lero

monga momwe mukadatilandirira

tili ndi nsembe zootcha

za nkhosa zamphongo, ng'ombe zamphongo

ndi anaankhosa onenepa 1,000.

40Nsembe yathu ikhaledi yotere pamaso panu.

Ifeyo tikutsateni ndi mtima wonse,

chifukwa anthu okhulupirira Inu

sadzachita manyazi.

41“Tsopano ndi mtima wonse

tikufunitsitsa kukutsatani,

tikufunitsitsa kumakuwopani

ndi kuyambanso kumakufunafunani.

42Musatichititse manyazi,

mutisamale moleza mtima,

moonetsa chifundo chanu chachikulu.

43Inu Ambuye, mutipulumutse

mwa njira zanu zodabwitsa,

kuti dzina lanu lilemekezedwe.

Onse ochita chiwembu anthu anu

muŵachititse manyazi.

44Muŵatsitse ndi kulanda mphamvu zao zonse,

nyonga zao zithyoke ndithu.

45Adziŵe kuti Inu nokha ndinu Ambuye Mulungu,

kuti mumalamulira dziko lonse lapansi.”

46Antchito a mfumu amene adaaponya anyamata atatu aja m'ng'anjo ya moto, ankasonkhezerasonkhezera moto uja ndi mafuta, phula, thonje ndi nsanthi za nkhuni.

47Malaŵi ake adakwera kumwamba kokwanira mamita makumi aŵiri.

48Malaŵiwo adayamba kumwazika mpaka kutentha Ababiloni amene anali pafupi ndi ng'anjo ya motoyo.

49Koma mngelo wa Ambuye adatsikira m'ng'anjo m'mene munali Azariya ndi anzake, nakankhira kunja malaŵi a moto wake.

50Kenaka adaziziritsa m'katimo ngati mwaloŵa mphepo yozizira. Motero motowo sudaŵatenthe konse, kapena kuŵapweteka.

Anyamata atatu aja aimba nyimbo yotamanda Mulungu

51Pamenepo anyamata atatu aja, onse pamodzi, adayamba kuimba nyimbo yotamanda ndi kulemekeza Mulungu m'ng'anjo ya moto muja.

52Adati,

“Mutamandike Inu Ambuye,

Mulungu wa makolo athu.

Ndinu oyenera kukutamandani

ndi kukulemekezani mpaka muyaya.

Litamandike dzina lanu

laulemerero ndi loyera.

Ndi loyenera kulitamanda

ndi kulilemekeza mpaka muyaya.

53Mutamandike m'Nyumba yanu yoyera

yoonetsa ulemerero wanu.

Ndinu oyenera kukutamandani

ndi kukulemekezani mpaka muyaya.

54Mutamandike Inu okwezedwa

pamwamba pa Akerubi

nkumayang'ana ku mapompho.

Ndinu oyenera kukutamandani

ndi kukulemekezani mpaka muyaya.

55Mutamandike pa mpando wanu waufumu.

Akuimbireni nyimbo

ndi kukulemekezani mpaka muyaya.

56Mutamandike m'thambo lakumwamba.

Akuimbireni nyimbo

ndi kukulemekezani mpaka muyaya.

57“Inu ntchito zonse za Ambuye,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

58Inu zinthu zonse zamumlengalenga

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

59Inu angelo a Ambuye,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

60Inu madzi onse akumwamba,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

61Inu zamphamvu zonse zokhala kumwamba,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

62Inu dzuŵa ndi mwezi,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

63Inu nyenyezi zakumwamba,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

64Inu mvula ndi mame,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

65Inu mphepo zonse,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

66Inu moto ndi mafundi,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

67Inu kuzizira kwachisanu

ndi kutentha kwachilimwe,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

68Inu mame ndi nkhungu,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

69Inu usiku ndi usana,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

70Inu kuŵala ndi mdima,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

71Inu madzi olimba ndiponso kuzizira,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

72Inu chipale ndi chisanu chambee,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

73Inu mphezi ndi mitambo,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

74“Iwe dziko lapansi,

tamanda Ambuye.

Aimbire nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

75Inu mapiri ndi magomo,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

76Inu zomera zonse za pa dziko lapansi,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

77Inu akasupe,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

78Inu nyanja ndi mitsinje,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

79Inu dzinsomba dzikuludzikulu

ndi zolengedwa zina zonse zam'nyanja,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

80Inu mbalame zonse zamumlengalenga,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

81Inu ng'ombe ndi nyama zonse zakuthengo,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

82“Inu anthu onse a pa dziko lapansi,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

83Inu Aisraele,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

84Inu ansembe a Ambuye,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

85Inu atumiki a Ambuye,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

86Inu mizimu ya anthu olungama,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

87Inu anthu onse oyera mtima

ndi odzichepetsa,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

88Inu, Hananiya, Azariya ndi Misaele,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵalemekeza mpaka muyaya.

Pajatu adatipulumutsa ku dziko la akufa,

adatilanditsa ku dzenje la imfa.

Adatipulumutsa m'ng'anjo ya moto,

adatilanditsa pakati pa moto.

89Thokozani Ambuye chifukwa ndi abwino,

ndipo chifundo chao nchosatha.

90Inu nonse opembedza Ambuye,

Mulungu wa milungu yonse,

tamandani Ambuye.

Aimbireni nyimbo yotamanda

ndi kuŵathokoza,

chifukwa chifundo chao nchosatha.”

91Akuwona zimenezo, mfumu Nebukadinezara adadabwa kwambiri. Adaimirira mofulumira nafunsa nduna zake kuti, “Kodi suja taponya anthu atatu m'ng'anjo yamoto ali omangidwa?” Iwowo adayankha kuti, “Ndi choncho kumene amfumu.”

92Mfumuyo idati, “Komabe ndikuwona anthu anai akungoyenda m'moto mwaufulu, osapsa. Ndipo wachinaiyo akuwoneka ngati mwana wa milungu.”

Anthu atatu aja aŵatulutsa naŵaika pa malo a ulemu

93Tsono Nebukadinezara adasendera ku khomo la ng'anjo yamoto, nati, “Sadrake, Mesaki ndi Abedenego, atumiki a Mulungu Wopambanazonse, tulukani bwerani kuno.” Pomwepo Sadrake, Mesaki ndi Abedenego adatuluka m'motomo.

94Ndipo, akalonga aja, abwanamkubwa, ndi aphungu a mfumu adasonkhana moŵazungulira, naona kuti moto sudathe kuŵatentha anthu amenewo. Tsitsi lao silidakwinyike, zovala zao sizidapse ndipo sizinkanunkha utsi mpang'ono pomwe.

95Apo Nebukadinezara adati, “Atamandike Mulungu wa Sadrake, Mesaki ndi Abedenego. Watuma mngelo wake kuti adzapulumutse atumiki amene amamkhulupirira, nakana kumvera lamulo la mfumu. Iwowo adadzipereka ku ng'anjo yamoto chifukwa chosafuna kutumikira ndi kupembedza mulungu wina aliyense, koma Mulungu wao yekha.

96Tsono ndikukhazikitsa lamulo ili: Munthu wina aliyense, kaya ndi wa mtundu wanji kaya ngwolankhula chilankhulo chanji, akadzanyoza Mulungu wa Sadrake, Mesaki ndi Abedenego, ndidzamkadzulakadzula ndipo nyumba yake ndidzaisandutsa bwinja. Palibetu mulungu wina aliyense amene angathe kupulumutsa anthu mwa njira yotere.”

97Ndipo mfumu idakweza Sadrake, Mesaki ndi Abedenego m'dera la Babiloni.

Maloto achiŵiri a Nebukadinezara

98Mfumu Nebukadinezara adatumiza mau kwa anthu a maiko onse, a mitundu yonse, olankhula zilankhulo zosiyanasiyana pa dziko lonse lapansi. Adati,

99“Mtendere ukule pakati panu. Chandikomera kuti ndikuuzeni zizindikiro ndi zodabwitsa zimene Mulungu Wopambanazonse wandiwonetsa.

100“Zizindikiro zake ndi zazikulu,

zodabwitsa zake ndi zamphamvu.

Ufumu wake ndi wamuyaya,

ulamuliro wake ndi wa mibadwo yonse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help