1 Eks. 4.22; Mt. 2.15 Chauta akuti,
“Pamene Israele anali mwana, ndinkamukonda.
Mwana wangayo ndidamuitana
kuti atuluke ku Ejipito.
2Ine ndikamakangaza kumuitana,
iye ndiye kumandithaŵa kunka kutali.
Ankaperekabe nsembe kwa Baala
ndi kulitenthera lubani fanolo.
3Komabe ndine amene ndidaphunzitsa Aefuremu kuyenda.
Ndidaŵalera, koma sadavomereze
kuti amene ndidaŵasamala ndine.
4Ndidaŵakokera kwa Ine mwachifundo ndi mwachikondi.
Ndidaŵanyamula nkuŵatsamiza kutsaya kwanga.
Ndidaŵerama, nkuŵadyetsa.
5“Tsono anthuwo adzabwereranso ku ukapolo ku Ejipito.
Aasiriya adzakhala oŵalamulira,
pakuti iwo akana kubwerera kwa Ine.
6Nkhondo idzaononga mizinda yao.
Adani adzaphwanya zipata za malinga ao ndi kuŵaononga,
chifukwa chotsata nzeru zaokha.
7Anthu anga akangamira zondipandukira Ine.
Tsono adzalira chifukwa cha goli lachilango
limene lili pa iwo,
koma palibe amene adzaŵachotsere.
8 Deut. 29.23 “Kodi ndingakusiye bwanji iwe Efuremu?
Kodi ndingathe kukutaya bwanji iwe Israele?
Kodi ndingathe bwanji kukusandutsa ngati Adima?
Kodi ndingathe kukuwononga ngati Zeboimu?
Mtima wanga wakana kutero,
chifundo changa chikukula.
9Sindidzalekerera kuti mkwiyo wanga ukulangitse,
sindidzamuwononganso Efuremu,
pakuti Ine ndine Mulungu osati munthu.
Ine, Woyera uja, ndili nawe,
ndipo sindidzabwera kudzakuwononga.
10“Ndidzaŵabangulira ngati mkango,
ndipo anthu anga adzanditsata.
Ndidzabanguladi,
ndipo adzathamangira kwa Ine ali njenjenje
kuchokera kuzambwe.
11Adzabwera akunjenjemera ngati mbalame
kuchokera ku Ejipito,
adzabwera ngati njiŵa kuchokera ku Asiriya.
Motero ndidzaŵabwezeranso kwao.
Ndikutero Ine Chauta.”
Israele ndi Yuda aimbidwa mlandu12Chauta akuti,
“Anthu a ku Efuremu andizinga ndi mabodza.
Banja limeneli la Israele nlonama kwambiri.
Nawonso anthu a ku Yuda akundipandukirabe Ine Mulungu,
Woyera ndi wokhulupirika.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.