Mt. 9 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yesu achiritsa munthu wa ziwalo zakufa(Mk. 2.1-12; Lk. 5.17-26)

1Yesu adaloŵa m'chombo naoloka nyanja, nkukafika ku mzinda wakwao.

2Kumeneko anthu ena adabwera kwa Iye ndi munthu wa ziwalo zakufa ali chigonere pa machira. Poona chikhulupiriro chao, Yesu adauza munthu wa ziwalo zakufayo kuti, “Limba mtima, mwana wanga, machimo ako akhululukidwa.”

3Apo aphunzitsi ena a Malamulo adayamba kudzifunsa mumtima mwao kuti, “Munthu ameneyu akuchita chipongwe Mulungu.”

4Koma Yesu adaadziŵa zimene iwo ankaganiza, motero adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukuganiza zoipa mumtima mwanu?

5Chapafupi koposa nchiti, kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Dzuka, yamba kuyenda?’

6Koma kuti mudziŵe kuti Mwana wa Munthu ali nazo mphamvu pansi pano zokhululukira machimo, onani.” Pamenepo adauza wofa ziwalo uja kuti, “Iwe, dzuka, tenga machira ako, uzipita kumudzi.”

7Munthu uja adadzukadi namapita kwao.

8Anthu onse aja ataona zimenezi, adachita mantha, ndipo adatamanda Mulungu amene adapatsa anthu mphamvu zotere.

Yesu aitana Mateyo(Mk. 2.13-17; Lk. 5.27-32)

9Yesu atachoka pamenepo, adaona munthu wina, dzina lake Mateyo, ali pa ntchito m'nyumba ya msonkho. Adamuuza kuti, “Iwe, unditsate.” Iye adanyamuka nkumamutsatadi.

10 Chifukwa akatero, matumbawo amaphulika, vinyoyo natayika, matumbawo nkutha ntchito. Koma vinyo watsopano amamuthira m'matumba atsopanonso. Apo zonse ziŵiri zimasungika bwino.”

Yesu achiza mwana wa Yairo ndi mai wina(Mk. 5.21-43; Lk. 8.40-56)

18Pamene Yesu ankakamba zimenezi, munthu wina wamkulu adadzamgwadira nati, “Mwana wanga wamkazi wamwalira tsopano apa. Chonde bwerani mudzamsanjike manja, kuti akhale ndi moyo.”

19Pamenepo Yesu adanyamuka, namtsatira pamodzi ndi ophunzira ake.

20Tsono panali mai wina amene adakhala akuvutika ndi matenda a msambo pa zaka khumi ndi ziŵiri. Iyeyu adafika cha kumbuyo kwa Yesu, nakhudza mphonje ya chovala chake.

21Mumtima mwake ankaganiza kuti, “Ndikangokhudza ngakhale chovala chake chokhacho, ndichira.”

22Pamenepo Yesu adacheuka, naona maiyo, ndipo adati, “Limbani mtima mai, chikhulupiriro chanu chakuchiritsani.” Nthaŵi yomweyo mai uja adachiradi.

23Pamene Yesu adafika kunyumba kwa mkulu uja, adaona anthu oimba zitoliro, ndiponso anthu ambiri obuma.

24Tsono Iye adaŵauza kuti, “Tatulukani! Mtsikanayutu sadamwalire ai, ali m'tulo chabe.” Pamenepo anthuwo adayamba kumseka monyodola.

25Koma onsewo atatulutsidwa, Yesu adaloŵa, nagwira mtsikanayo pa dzanja, iye nkuuka.

26Mbiri imeneyi idawanda m'dera lonselo.

Yesu achiritsa anthu aŵiri akhungu

27Pamene Yesu ankachoka kumeneko, anthu aŵiri akhungu adamtsatira. Ankafuula kuti, “Inu Mwana wa Davide, mutichitire chifundo.”

28Yesu ataloŵa m'nyumba, akhungu aja adadzampeza, Iye nkuŵafunsa kuti, “Kodi mukukhulupirira kuti ndingathe kuchita zimenezi?” Iwo adati, “Inde, Ambuye.”

29Apo Yesu adakhudza maso ao nati, “Zikuchitikireni monga momwe mwakhulupiriramo.”

30Pamenepo maso ao adaphenyuka. Tsono Yesu adaŵalamula mwamphamvu kuti, “Wina aliyense asazidziŵetu zimenezi.”

31Koma iwo adachoka pamenepo nkumakawanditsa mbiri yake ku dera lonselo.

Yesu achiritsa munthu wosatha kulankhula

32Pamene iwowo ankatuluka m'nyumbamo, anthu ena adabwera kwa Yesu ndi munthu wosatha kulankhula, chifukwa chogwidwa ndi mzimu woipa.

33Yesu atatulutsa mzimu woipawo, munthu uja adayamba kulankhula. Apo anthu onse adazizwa nati, “Nkale lonse Aisraele sadaziwone zotere.”

34Mt. 10.25; 12.24; Mk. 3.22; Lk. 11.15Koma Afarisi adati, “Ameneyu amatulutsa mizimu yoipa ndi mphamvu zomupatsa mfumu ya mizimu yoipa ija.”

Za chifundo cha Yesu

35 Mt. 4.23; Mk. 1.39; Lk. 4.44 Yesu adayendera mizinda ndi midzi yonse. Adanka naphunzitsa m'nyumba zao zamapemphero, nkumalalika Uthenga Wabwino wonena za Ufumu wakumwamba. Ndiponso ankachiritsa nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam'thupi.

36Num. 27.17; 1Maf. 22.17; 2Mbi. 18.16; Ezek. 34.5; Mk. 6.34Pamene adaona makamu a anthu, adaŵamvera chifundo, chifukwa iwo anali olema ndi ovutika ngati nkhosa zopanda mbusa.

37Lk. 10.2Tsono adauza ophunzira ake kuti, “Dzinthu ndzochulukadi, achepa ndi antchito.

38Nchifukwa chake mupemphe Mwini dzinthu kuti atume antchito okatuta dzinthu dzakedzo.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help