Ezek. 28 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mau odzudzula mfumu ya ku Tiro

1Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,

2“Iwe mwana wa munthu,

uza mfumu ya ku Tiro mau angaŵa akuti,

Iwe ndi mtima wako wodzikuza umanena kuti,

‘Ine ndine mulungu.

Ndimakhala ngati mfumu pa mpando wa milungu

pakati pa nyanja yozama.’

Koma chonsecho ndiwe munthu chabe, osati mulungu,

ngakhale umadziyesa wanzeru ngati mulungu.

3Ai, iwe ndiwe wanzerudi kupambana Daniele,

palibe chinsinsi chobisika kwa iwe.

4Nzeru zako ndi kumvetsa kwako zidakulemeretsa

pokupatsa chuma cha golide ndi siliva.

5Udachulukitsa chuma chako

chifukwa cha nzeru zako zoyendetsera malonda,

ndipo ukunyada chifukwa cha chuma chakocho.

6Tsono Ine Ambuye Chauta ndikuti,

Poti umadziganizira kuti ndiwe wanzeru ngati mulungu,

7Ine ndidzabwera ndi anthu achilendo

kuti adzalimbane nawe.

Iwowo ndi mtundu wa anthu ankhanza kwambiri.

Adzakuthira nkhondo kuti aononge zokoma zonse

zimene udazipata ndi nzeru zako,

ndiponso kuti athyole kunyada kwako.

8Adzakuponya ku malo a anthu akufa,

udzafa imfa yoopsa m'nyanja yozama.

9Kodi pamenepo udzanenabe kuti ndiwe mulungu

pamaso pa anthu amene akukuphawo?

Iyai, udzaoneka ngati munthu ndithu osati mulungu,

pamene udzakhala m'manja mwa okuphawo.

10Udzafa imfa ya anthu osaumbalidwa

m'manja mwa anthu achilendo.

Ine ndalankhula zimenezi.

Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”

Nyimbo yolira mfumu ya ku Tiro

11Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,

12“Iwe mwana wa munthu,

imba nyimbo ya maliro,

kulira mfumu ya ku Tiro.

Uiwuze mau angaŵa akuti,

Udaali chitsanzo cha ungwiro weniweni.

Udaali wanzeru ndiponso wokongola kwabasi.

13Unkakhala ngati ku Edeni, ku munda wa Mulungu,

ndipo unkadzikongoletsa

ndi miyala yamtengowapatali ya mitundu yonse:

karineliyoni, topazi, jasipere,

kirisoliti, berili, onikisi,

safiro, rubi ndi emeradi.

Zoikamo miyalayo zinali zagolide.

Adakupangira zonsezi pa tsiku limene udalengedwa.

14Ndidakuikira mngelo woopsa kuti azikulonda.

Unkakhala pa phiri langa lopatulika,

ndipo unkayenda pakati pa miyala yamoto.

15Makhalidwe ako anali angwiro

kuyambira tsiku limene udalengedwa

mpaka nthaŵi imene udayamba kuchita zoipa.

16Potanganidwa ndi zamalonda,

udaachulukitsa zandeu ndi kumangochimwa.

Nchifukwa chake ndidakuchotsa ku phiri langa lopatulika.

Mngelo amene ankakulonda

adakupirikitsa kuchokera ku miyala yamotoyo.

17Unkanyada chifukwa cha kukongola kwako,

udaipitsa nzeru zako chifukwa chofuna kukhala wotchuka.

Motero ndidakugwetsa pansi

kuti ukhale chenjezo kwa mafumu ena.

18Udachita zoipa zambiri pa kugula ndi kugulitsa zinthu,

ndipo choncho malo ako achipembedzo udaŵaipitsa.

Motero ndidabutsa moto pakati pako ndi kukupserezeratu.

Onse okupenya tsopano

amaona kuti ndiwe phulusa pa dziko lapansi.

19Anthu a mitundu yonse amene ankakudziŵa

akuwopsedwa ndi zimene zidakuchitikira.

Imfa yako inalidi yoopsa,

ndipo sudzakhalanso mpaka muyaya.”

Mau odzudzula mzinda wa Sidoni

20 Yow. 3.4-8; Zek. 9.1, 2; Mt. 11.21, 22; Lk. 10.13, 14 Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,

21“Iwe mwana wa munthu, utembenukire ku mzinda wa Sidoni ndipo ulose momdzudzula kuti,

22“Ine Ambuye Chauta ndikuti,

‘Ndine mdani wako, iwe Sidoni,

ndipo anthu akadzaona zimene ndidzakuchite iwe,

adzandilemekeza.

Adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndikadzakulanga

ndipo ndikadzaonetsa pakati pako kuti Ine ndine woyera.

23Ndidzakugwetsera mliri,

ndipo m'miseu yako mudzayenderera mitsinje ya magazi.

Anthu adzatha phu nkuphedwa,

nkhondo idzakuzinga mbali zonse.

Tsono anthu adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.’ ”

Israele adzadalitsidwa

24“Nthaŵi imeneyo pafupi ndi Aisraele sipadzakhalanso anthu onyoza omaŵalasa ngati mitungwi, kapena omaŵapweteka ngati minga. Apo anthu adzadziŵa kuti Ine ndine Ambuye Chauta.

25“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Nditasonkhanitsa Aisraele kuchokera ku mitundu ya anthu kumene adamwazikira, ndidzaonetsa kuyera kwanga mwa iwo, anthu a mitundu yonse akuwona. Aisraelewo adzakhalanso m'dziko lao limene ndidaapatsa mtumiki wanga Yakobe.

26Adzakhala kumeneko mwamtendere, ndipo adzamanga nyumba ndi kulima minda yamphesa. Adzakhala kumeneko mwamtendere, pamene ndidzalange anthu oyandikana nawo, amene ankaŵanyoza. Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, Mulungu wao.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help