Ezek. 21 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Lupanga la Chauta

1Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,

2“Iwe mwana wa munthu, tembenuka uyang'ane cha ku Yerusalemu, ndipo ulalike zodzudzula malo ake opatulika. Ulose zodzudzula dziko la Israele.

3Uliwuze dziko la Israelelo kuti Chauta akuti, ‘Ndimati ndilimbane nawe. Choncho ndidzasolola lupanga langa m'chimake kuti ndiphe anthu ako, abwino ndi oipa omwe.

4Ndithu ndidzasolola lupanga langa m'chimake kuti ndidzaphe anthu ako oipa ndi abwino omwe, ndiye kuti anthu onse kuyambira kumwera mpaka kumpoto.

5Motero anthu onse adzadziŵa kuti Ine Chauta ndasolola lupanga langa, ndipo sindidzalilonganso m'chimake.’

6“Tsono iwe mwana wa munthu, buula pamaso pao, buula kwambiri ndi mtima woŵaŵa zedi.

7Akakufunsa chifukwa chake chimene ukubuulira, uŵayankhe kuti, ‘Ndikubuula chifukwa cha nkhani zimene ndamvazi. Zikadzachitika zimenezo, mitima idzangoti fumu, ndipo manja ao onse adzalefuka, mpweya wao wonse udzaŵathera, onse m'maondo mwao mudzangoti zii. Zikubwera, zidzachitikadi!’ Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”

8Chauta adandipatsiranso uthenga uwu wakuti,

9“Iwe mwana wa munthu, ulose, ndipo unene kuti Ambuye akuti,

“ ‘Lupanga, lupanga, alinola,

ndipo alipukuta.

10Alinola kuti likaphe,

alipukuta kuti ling'anipe ngati mphezi.

Kodi tingakondwere bwanji, pamene anthu anga anyoza ndodo yanga yolangira?

11Lupanga laperekedwa kuti alipukute ndipo kuti alinyamule. Lupanga limeneli lanoledwa ndi kupukutidwa, kuti alipereke m'manja mwa munthu amene amapha.

12Ulire ndipo ufuule, iwe mwana wa munthu, chifukwa zonsezi zidzagwera anthu anga. Zidzagweranso akalonga a Aisraele. Adzaphedwa ndi lupanga pamodzi ndi anthu anga. Nchifukwa chake udzigunde pa chifuŵa mwachisoni.

13Zingalephere bwanji kuwoneka, popeza kuti akunyoza ngakhale ndodo yanga yolangira?’ Ndikutero Ine Ambuye Chauta.

14“Koma iwe mwana wa munthu, losa, ndipo uwombe m'manja. Lupangalo lidzagwe kaŵiri ngakhale katatu, ndiye kuti lupanga lophera. Ndilodi lupanga loononga anthu koopsa, limene likuŵazungulira.

15Anthu anga adzataya mtima, ndipo ambiri adzagwa. Ndaŵaikira lupanga laphuliphuli. Ha, lupanga lidapangidwadi kuti lizing'anipa ngati mphezi, ndipo azilisolola nkuphera anthu.

16Lupanga iwe, uzikapha ku dzanja lamanja, uzikapha ku dzanja lamanzere, kulikonse kumene nsonga yako yaloza.

17Inenso ndidzaomba m'manja, ndi kuziziritsa mkwiyo wanga. Ine Chauta ndatero.”

Lupanga la mfumu ya ku Babiloni

18Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,

19“Iwe mwana wa munthu, ulembe zizindikiro pa miseu iŵiri imene mfumu ya ku Babiloni ingathe kudzeramo, pobwera ndi lupanga. Iŵiri yonseyo idzakhala yochokera ku dziko limodzi. Uike chikwangwani pa mphambano ya miseu yopita ku mzinda.

20Ulembe zizindikiro pa mseu umene lupanga lidzadzere popita ku Raba wa ku Amoni, ndiponso ku Yuda ndi ku Yerusalemu, mzinda wamalinga.

21Mfumu ya ku Babiloni yaima ku njira pa mphambano ya miseu. Ikuwombeza maula ndi mivi kuti ipeze njira yoyenera kudzeramo. Ikupempha nzeru kwa milungu yake, ndipo ikuyang'ana chiŵindi cha nyama yopereka ku nsembe.

22Tsono m'dzanja lake lamanja muli muvi wa ula wolembedwa Yerusalemu. Kumeneko mfumu iyenera kukalalika za kupha anthu ndiponso kufuula mfuu wankhondo. Iyenera kupanga makina othyolera zipata, kuunda mitumbira yankhondo ndi kumanga nsanja.

23Koma kwa anthu a ku Yerusalemu zidzaoneka ngati zolosa zabodza, chifukwa cha malumbiro amene adaachita kwa mfumuyo. Koma adzaŵakumbutsa za machimo ao, kuti adzatengedwe ukapolo.

24“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta, ndikuti, Mwandikumbutsa zolakwa zanu, ndipo kundiwukira kwanu kwaonekera poyera. Mukuwonetsa machimo anu pa zochita zanu zonse. Nchifukwa chake mudzagwidwa ndi kutengedwa ukapolo.

25“Tsono iwenso, wolamulira Israele, iwe wonyozeka ndi woipa, lafika tsiku lako, ndiye kuti nthaŵi ya chilango chako chomaliza.”

26Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Vula nduŵirayo, chotsa chisoti chaufumucho. Zonse zasinthika! Otsika uŵakweze, okwera uŵatsitse.

27Chipasupasu! Chipasupasu! Mzinda ndidzaupasula, ndipo sadzaumanganso mpaka atafika amene ali woyenera kuulandira. Pamenepo ndidzaupatsa kwa iyeyo.

Achenjeza Aamoni

28 Yer. 49.1-6; Ezek. 25.1-7; Amo. 1.3-15; Zef. 2.8-11 “Tsono iwe mwana wa munthu, ulalike kuti, ponena za Aamoni ndi manyozo ao, Ine Chauta ndikuti,

“ ‘Lupanga, lupanga alisolola kuti liwononge.

Alipukuta kuti liwononge,

kuti ling'anipe ngati mphezi.

29Zimene akuti akuziwona m'masomphenya nzabodza ndiponso maula ao ndi onama. Mudzakhala pamodzi ndi anthu oipa, amene tsiku lao lafika, ndiye kuti nthaŵi ya kulangidwa kwao komaliza.

30Mulibwezerenso lupanga m'chimake. Ndidzakuweruzani kumalo kumene mudabadwira, ku dziko la makolo anu.

31Ndidzakukwiyirani ndipo ukali wanga udzakuyakirani. Ndidzakuperekani m'manja mwa anthu ankhanza, amene amadziŵa kuwononga.

32Mudzakhala ngati nkhuni pa moto. Ena adzakhetsa magazi anu m'dziko mwanu momwe. Palibe amene adzakukumbukiraninso. Ndatero Ine Chauta.’ ”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help