1 Ntc. 16.12 Ndife, Paulo ndi Timoteo, atumiki a Khristu Yesu. Tikulembera onse a mu mzinda wa Filipi, amene ali anthu ake a Mulungu mwa Khristu Yesu. Tikulemberanso oyang'anira Mpingo ndi atumiki ao.
2Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere.
Paulo apempherera mpingo wa ku Filipi3Ndimayamika Mulungu wanga nthaŵi zonse ndikamakukumbukirani.
4Nthaŵi zonse pamene ndikukupemphererani nonsenu, ndimapemphera mokondwa.
5Ndiyeneradi kuthokoza chifukwa mwakhala mukugwirizana nane ndi kundithandiza kufalitsa Uthenga Wabwino, kuchokera tsiku limene mudayamba kukhulupirira mpaka tsopano.
6Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.
7Ndikuyeneradi kuganiza zotere za nonsenu, popeza kuti ndimakukondani kwambiri. Pakuti nonsenu ndinu ogwirizana nane ndithu, pamene ndili m'ndende ndiponso pamene ndikugwira ntchito iyi imene Mulungu adandipatsa mwa kukoma mtima kwake, ntchito ya kuteteza ndi kukhazikitsa Uthenga Wabwino.
8Mulungu akundichitira umboni kuti ndimakulakalakani kwambiri, pakuti ndimakukondani ndi mtima wonse, motsanzira chikondi cha Khristu Yesu mwini.
9Pemphero langa ndi lakuti chikondi chanu chinke chikukulirakulira pamodzi ndi nzeru ndi kumvetsetsa zinthu mozama.
10Pamenepo mudzadziŵa kusankha zimene zili zabwino kotheratu. Apo pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu mudzapezeka oyera mtima, ndi opanda cholakwa chilichonse.
11Ndipo moyo wanu udzakhala wodzaza ndi zipatso za chilungamo zimene mudzaonetsa mothandizidwa ndi Yesu Khristu, kuti anthu onse alemekeze ndi kutamanda Mulungu.
“Kwa ine moyo wanga ndi Khristu”12Abale, ndikufuna kuti mudziŵe kuti zimene zandigwera, zathandiza ndithu kufalitsa Uthenga Wabwino.
13Ntc. 28.30Mwakuti asilikali onse olonda nyumba ya mfumu, ndi ena onse kuno, adziŵa kuti ndili m'ndende chifukwa cha Khristu.
14Tsono chifukwa choti ndili m'ndende, abale ochuluka akulimba mtima mwa Ambuye, ndipo akulalika mau a Mulungu mopanda mantha.
15Alipodi ena amene amalalika Khristu chifukwa cha kaduka ndi kukonda mikangano. Koma aliponso ena amene amamlalika ndi mtima woona.
16Otsirizaŵa amamlalika chifukwa cha chikondi, popeza kuti amadziŵa kuti Mulungu adandikhazika muno kuti ndigwire ntchito yoteteza Uthenga Wabwino.
17Koma oyamba aja salalika Khristu moona. Amangodzikonda okha, ndipo amafuna kundiwonjezera zoŵaŵa pamene ndili m'ndende muno.
18Zili nkanthu ngati! Kaya amalalika mwachiphamaso, kaya moona, malinga nkuti Khristu akulalikidwa, pamenepo ine ndikukondwa.
19Ndipo sindidzaleka kukondwa podziŵa kuti chifukwa cha mapemphero anu ndiponso chithandizo cha Mzimu wopatsidwa ndi Yesu Khristu ndidzamasulidwa.
20Motero ndikuyembekeza ndi kukhulupirira ndi mtima wonse kuti sipadzakhala konse manyazi. Koma ndikuyembekeza kuti ndidzalimba mtima kulankhula poyera, kuti tsopanonso, monga nthaŵi zonse, Khristu alemekezedwe mwa ine, ngakhale ndikhale moyo, kapena ndimwalire.
21Kwa inetu moyo ndi Khristu amene, ndipo nayonso imfa ili ndi phindu.
22Koma ngati kukhalabe moyo kungandipatse mwai woti ndigwire ntchito yoonetsa zipatso, sindidziŵa kaya ndingasankhe chiti.
23Ndagwira njakata. Kwinaku ndikulakalaka kuti ndisiye moyo uno ndikakhale pamodzi ndi Khristu, pakuti chimenechi ndiye chondikomera koposa.
24Koma kwinakunso nkofunika kwambiri kuti ndikhale moyo chifukwa cha inuyo.
25Mosakayika konse ndikudziŵa kuti ndidzakhalapobe. Ndidzapitiriza kukhala nanu nonsenu, kuthandiza kuti chikhulupiriro chanu chizikula, ndipo chikupatseni chimwemwe koposa kale.
26Motero pamene ndidzafikanso kwanuko, mudzakhala ndi zifukwa zochuluka zonyadira Khristu Yesu chifukwa cha ine.
Paulo aŵachenjeza kuti azipirira27Chachikulu nchakuti mayendedwe anu akhale oyenerana ndi Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Ngakhale ndibwere kudzakuwonani, kapena ndikhale kutali, ndikufuna kumva kuti mukulimbika ndi mtima umodzi. Ndikufunanso kumva kuti momvana ndi mothandizana mukumenya nkhondo chifukwa chokhulupirira Uthenga Wabwino,
28osalola kuti adani anu azikuwopsezani pa kanthu kalikonse. Zimenezi zidzaŵatsimikizira kuti iwowo adzaonongeka, koma inu mudzapulumuka. Mulungu ndiye amene adzakuchitirani zimenezi.
29Paja Iye adakupatsani mwai, osati wakungokhulupirira Khristu ai, komanso wakumva zoŵaŵa chifukwa cha Iye.
30Ntc. 16.19-40Inunso mukumenya nkhondo yomwe ija imene mudandiwona ine ndikuimenya, yomwenso ndikumenyabe tsopano, monga mukumveramu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.