1 Tim. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za atsogoleri mu mpingo

1Aŵa ndi mau otsimikizika ndithu akuti, “Ngati munthu afuna ntchito ya kuyang'anira Mpingo, akukhumba ntchito yaulemu.”

2Tit. 1.6-9Woyang'anira Mpingo azikhala munthu wopanda chokayikitsa, akhale wa mkazi mmodzi yekha, akhale wodzigwira, wa maganizo anzeru, waulemu, wosamala bwino alendo, ndi wotha kuphunzitsa.

3Asakhale chidakwa, asakhale wandeu, koma wofatsa, wosakangana ndi anthu, ndi wosakonda ndalama.

4Akhale wodziŵa kuyendetsa bwino banja lake, ndi kulera bwino ana ake, kuti akhale omvera ndi aulemu kwenikweni.

5Ngati munthu sadziŵa kuyendetsa bwino banja lake, nanga angasunge bwanji Mpingo wa Mulungu?

6Asakhale munthu wolandiridwa mu mpingo chatsopano, kuwopa kuti angadzitukumule nkulangidwa monga momwe Satana adalangidwira.

7Kuwonjezera pamenepo, akhale munthu woti ndi akunja omwe amamlemekeza, mwinamwina nkudzayamba kunyozedwa nagwa mu msampha wa Satana.

Za atumiki mu mpingo

8Chimodzimodzinso ndi atumiki a mpingo: akhale ochita zachiukulu, osanena paŵiripaŵiri, osakhala ozoloŵera zoledzeretsa, osakonda udyo phindu la ndalama.

9Akhale anthu a mtima wopanda kanthu koutsutsa posunga zoona za chikhulupiriro zimene Mulungu adaulula.

10Iwonso ayambe ayesedwa, ndipo pambuyo pake, ngati alibe chokayikitsa, ndiye asenze udindo wa atumiki.

11Momwemonso akazi akhale ochita zachiukulu, osasinjirira, odzigwira, ndi okhulupirika pa zonse.

12Atumiki a mpingo akhale a mkazi mmodzi yekha. Akhale olera ana ao bwino, oyendetsanso bwino mabanja ao.

13Paja anthu ogwira bwino ntchito ya utumiki, amadzitengera mbiri yabwino, ndipo amalimba mtima kwenikweni pakuika chikhulupiriro chao mwa Khristu Yesu.

Za chinsinsi chachikulu

14Pamene ndikukulembera zimenezi, ndikuyembekeza kudzafika kwanuko posachedwa.

15Koma zina zikandichedwetsa, zimene ndanenazi zidzakudziŵitsa za m'mene anthu ayenera kukhalira m'banja la Mulungu, limene lili Mpingo wa Mulungu wamoyo, ndi mzati wochirikiza choona.

16Ndithudi, chinsinsi cha chipembedzo chathu nchachikulu:

“Iye uja adaonekera ali ndi thupi la munthu,

Mzimu Woyera adamchitira umboni kuti ndi wolungama,

angelo adamuwona,

adalalikidwa pakati pa anthu a mitundu yonse,

anthu a pa dziko lonse lapansi adamkhulupirira,

Iyeyo adatengedwa kunka kumwamba mu ulemerero.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help