1Nthaŵi ya ufumu wa Davide kunali njala ya zaka zitatu motsatanatsatana. Ndiye Davide adapempha nzeru kwa Chauta, ndipo Chauta adamuuza kuti, “Saulo ndi banja lake adakali nawobe mlandu uja wopha Agibiyoniwu.”
2Yos. 9.3-15 Choncho mfumuyo idaitana Agibiyoni. Agibiyoniwo sanali Aisraele, koma Aamori otsalira. Ngakhale Aisraele anali atalumbira kuti sadzaŵapha Agibiyoniwo, komabe Saulo adafuna kuŵaonongeratu chifukwa cha chikondi chake pa Israele ndi pa Yuda.
3Tsono Davide adafunsa Agibiyoni aja kuti, “Kodi ndikuchitireni chiyani? Ndingapepese bwanji kuti mutipemphere kwa Chauta kuti atidalitse?”
4Agibiyoniwo adauza Davide kuti, “Mlandu umene ulipo pakati pa ife ndi Saulo kapena banja lake, si woti nkulipira ndi golide kapena siliva, ndiponso sikuti kapena ife tikufuna kulipira pakupha wina aliyense m'dziko la Israele ai.” Apo Davide adafunsanso kuti, “Nanga tsono mukuti ndikuchitireni chiyani?”
5Iwo adayankha kuti, “Saulo adaafuna kutiwonongeratu, ndipo adaakonza zoti titheretu m'dziko lonse la Israele.
6Tsono mwa zidzukulu zake mutipatse anthu asanu ndi aŵiri, kuti ife tikaŵanyonge pamaso pa Chauta ku Gibiyoni, ku mzinda wa Saulo munthu wosankhidwa wa Chauta.” Apo mfumuyo idayankha kuti, “Chabwino, ndidzaŵapereka.”
7 1Sam. 20.15-17; 2Sam. 9.1-7 Koma mfumu idasunga Mefiboseti, mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, chifukwa cha kulumbira kumene mfumu Davideyo ndi Yonatani mwana wa Saulo adaachita pamaso pa Chauta.
81Sam. 18.19 Choncho mfumuyo idatenga Arimoni ndi Mefiboseti winanso, ana a Rizipa, mwana wamkazi wa Aya amene adambalira Saulo. Idatenganso ana aamuna asanu amene Merabi, mwana wamkazi wa Saulo, adambalira Adriyele mwana wa Barizilai Mmehola,
9naŵapereka kwa Agibiyoni. Tsono onsewo adaŵanyonga pa phiri, pamaso pa Chauta, ndipo asanu ndi aŵiri onsewo adafera pamodzi. Iwowo adaphedwa masiku oyamba akholola, nthaŵi yoyamba kudula barele.
10Tsono Rizipa, mwana wamkazi wa Aya, adatenga chiguduli nadziyalira pathanthwe pamene panali mitembo ya anthuwo, kuyambira pa chiyambi cha kholola mpaka mvula idayambanso kugwa. Mkaziyo sadalole kuti pa mitemboyo pafike mbalame masana kapena zilombo zakuthengo usiku.
11Davide atamva zimene Rizipa mwana wa Aya, mzikazi wa Saulo adachita,
121Sam. 31.8-13 adapita kukatenga mafupa a Saulo ndi mafupa a Yonatani mwana wa Saulo. Adaŵachotsa m'manja mwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi, amene adaaba mafupawo ku bwalo la ku Beteseani, kumene Afilisti adaaŵanyonga, tsiku limene Afilistiwo adapha Saulo ku Gilibowa.
13Davide adatenga mafupa a Saulo ndi a Yonatani mwana wake naŵachotsa kumeneko. Kenaka adasonkhanitsanso mafupa a anthu aja amene adaŵanyongera paphiri paja.
14Ndipo adaika mafupa a Saulowo pamodzi ndi mafupa a Yonatani mwana wake, m'dziko la Benjamini ku Zela, m'manda a Kisi bambo wake wa Saulo, potsata zonse zimene mfumu idaalamula. Pambuyo pake Mulungu adamvera mapemphero opempherera dzikolo.
Nkhondo ndi ziphona zachifilisti.(1 Mbi. 20.4-8)15Nthaŵi ina Afilisti adamenyananso nkhondo ndi Aisraele. Davide adapita ndi ankhondo ake, nakamenyana nawo nkhondo Afilistiwo, ndipo iyeyo adatopa kwambiri.
16Tsono Isibi-Benobi, mmodzi mwa zidzukulu za ziphona zija zotchedwa Arefaimu, amene mkondo wake unkalemera makilogramu atatu ndi theka, ndiponso amene anali ndi lupanga latsopano m'lamba, adaganiza zoti aphe Davide.
171Maf. 11.36; Mas. 132.17Koma Abisai, mwana wa Zeruya, adabwera kudzathandiza Davide, nalimbana ndi Mfilistiyo mpaka kumupha. Tsono anthu a Davide adamlonjeza molumbira Davideyo kuti, “Tsopano inu simudzapita nafenso ku nkhondo, kuwopa kuti mungaphedwe. Inu ndinu amene Aisraele onse amagonerapo.”
18Pambuyo pake nkhondo idabukanso ndi Afilisti ku Gobu. Pamenepo Sibekai Muhusa, adapha Safu, amene analinso mmodzi mwa zidzukulu za Arefaimu.
19Kenaka nkhondo inanso idabuka ndi Afilisti omwewo ku Gobu. Tsono Elihanani, mwana wa Yaare-Oregimu wa ku Betelehemu, adapha Lahimi, mbale wa Goliyati wa ku Gati uja, amene thunthu la mkondo wake linali lalikulu ngati mtanda woombera nsalu.
20Kudabukanso nkhondo ina ku Gati, kumene kunali munthu wina wamtali, wa zala zakumanja uku zisanu ndi chimodzi uku zisanu ndi chimodzi, zakumwendonso uku zisanu ndi chimodzi uku zisanu ndi chimodzi, zonse pamodzi zala 24. Iyeyonso anali mmodzi mwa zidzukulu za Arefaimu.
21Pamene iye ankanyoza Aisraele, Yonatani mwana wa Simea, mbale wa Davide, adamupha.
22Anthu anaiwo anali zidzukulu za Arefaimu a ku Gati, ndipo adaphedwa ndi Davide ndi ankhondo ake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.