1Mulungu akutsogolera msonkhano wakumwamba.
Akugamula mlandu milungu ya pansi pano.
2Akuti,
“Mudzakhalabe mukuweruza mopanda chilungamo mpaka liti?
Bwanji mukupitirizabe kumakondera anthu oipa?
3Inu tetezani anthu ofooka ndi amasiye mwachilungamo.
Weruzani molungama ozunzika ndi amphaŵi.
4“Landitsani ofooka ndi osoŵa.
Apulumutseni kwa anthu oipa.”
5Iwo sadziŵa kanthu ndiponso alibe nzeru,
amangoyenda m'chimbulimbuli.
Maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.
6 Yoh. 10.34 Ine ndikuti, “Inu ndinu milungu,
nonsenu ndinu ana a Mulungu Wopambanazonse.
7Komabe mudzafa ngati anthu onse,
ndipo mudzagwa ngati kalonga wina aliyense.”
8Dzambatukani, Inu Mulungu, weruzani dziko lapansi,
popeza kuti mitundu yonse ya anthu ndi yanu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.