1Tsono tisangoima pa maphunziro oyamba enieni a Khristu. Tisachite kubwerezanso kuphunzitsa zomwe zili ngati maziko, monga za kutembenuka mtima kusiya ntchito zosapindulitsa moyo wosatha, za kukhulupirira Mulungu,
2za maubatizo, za kusanjika manja, za kuuka kwa akufa, ndi za chiweruzo chotsiriza. Koma tiyeni tipitirire mpaka tikafike pa kukhwima kwenikweni.
3Mulungu akalola, tidzaterodi.
4Anthu amene adataya chikhulupiriro chao, nkosatheka kuŵatsitsimutsa kuti atembenuke mtima. Iwowo kale Mulungu adaaŵaunikira, adaalaŵako mphatso yochokera Kumwamba, nkulandira nao Mzimu Woyera.
5Ndipo adazindikira kukoma kwa mau a Mulungu, ndi mphamvu za nthaŵi imene inalikudzafika.
6Tsono akamkana Mulungu tsopano, akuchita ngati kumpachika iwo omwe Mwana wa Mulungu, ndi kumnyozetsa poyera.
7Paja nthaka yolandira mvula kaŵirikaŵiri, nkubereka mbeu zopindulitsa oilima, Mulungu amaidalitsa.
8Gen. 3.17, 18 Koma ngati ibereka minga ndi nthula, ndi yachabe ndipo ili pafupi kutembereredwa. Mathero ake nkutenthedwa m'moto.
9Koma inu okondedwa anga, ngakhale tikunena zimenezi, sitikukukayikirani. Tikudziŵa kuti muli nazo zabwino, zolinga ku chipulumutso chanu.
10Paja Mulungu ngwolungama, sangaleke kusamalako za ntchito zanu, ndi chikondi chimene mudaamuwonetsa pakutumikira oyera ake, monga m'mene mukuchitirabe tsopano.
11Tikufunitsitsa kuti aliyense mwa inu apitirire kuwonetsa changu chomwechi mpaka potsiriza, kuti chiyembekezo chanu chifike pake penipeni.
12Sitifuna kuti mukhale aulesi, koma kuti mutsanzire anthu amene, pakukhulupirira ndi pakupirira, akulandira zimene Mulungu adalonjeza.
Za lonjezo lokhazikika la Mulungu13Pamene Mulungu ankamulonjeza kanthu Abrahamu, adaalumbira kuti, “Pali Ine ndemwe, Mulungune.” Adaatero, popeza kuti panalibe wamkulu koposa Mwiniwakeyo amene akadamtchula polumbirapo.
14Gen. 22.16, 17 Ndiye Mulungu adati, “Ndithudi ndidzakudalitsa kwakukulu, ndipo ndidzachulukitsa kwambiri zidzukulu zako.”
15Nchifukwa chake Abrahamu adaayembekeza molimbikira, nalandira zimene Mulungu adaamlonjeza.
16Anthu amalumbira m'dzina la wina amene akuŵaposa, ndipo lumbiro lotere lotsimikizira mau, limathetsa kutsutsana konse pakati pao.
17Mulungu pofuna kuŵatsimikizira anthu odzalandira zimene adaalonjeza, kuti Iye sangasinthe maganizo, adatsimikiza lonjezo lakelo pakulumbira.
18Motero pali zinthu ziŵirizi, lonjezo ndi lumbiro, zimene sizingathe kusinthika, ndipo Mulungu sanganamirepo. Mwa zimenezi Mulungu adafuna kutilimbitsa mtima ife amene tidathaŵira kwa Iye, kuti tichigwiritse chiyembekezo chimene adatiikira pamaso pathu.
19Lev. 16.2 Chiyembekezo chimenechi tili nacho ngati nangula wa moyo wathu. Nchokhazikika, nchosagwedezeka konse, ndipo chimabzola chochinga cha Nyumba ya Mulungu ya Kumwamba, nkukaloŵa mpaka ku Malo Opatulika am'katikati.
20Mas. 110.4 Yesu adatitsogolera kale nkuloŵamo chifukwa cha ife. Iye adasanduka mkulu wa ansembe onse wamuyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.