1“Ngati munthu apereka nsembe yachiyanjano kwa Chauta, nsembe yake ikakhala ya ng'ombe yamphongo kapena yaikazi, ikhale yopanda chilema.
2Munthuyo asanjike dzanja lake pamutu pa ng'ombeyo, ndipo aiphere pa khomo la chihema chamsonkhano. Pomwepo ansembe, ana a Aroni, aliwaze magazi guwa molizungulira.
3Ndipo pa nsembe yachiyanjanoyo, yopereka kwa Chauta ndi yoyenera kuitentha pa moto, atapepo mafuta okuta matumbo.
4Apatulenso imso ziŵiri, pamodzi ndi mafuta ake omwe, ndiponso mphumphu ya mafuta akuchiŵindi, ochotsa pamodzi ndi imso zija.
5Tsono ana a Aroni atenthe zonsezo pa guwa, pamodzi ndi nsembe yopsereza imene ili pa nkhuni pamotopo. Imeneyo ndiyo nsembe yotentha pa moto, ya fungo lokomera Chauta.
6“Ngati munthu apereka nsembe yachiyanjano kwa Chauta, nsembe yake ikakhala nkhosa yamphongo kapena yaikazi, ikhale yopanda chilema.
7Akapereka nkhosa kuti ikhale nsembe, abwere nayo pamaso pa Chauta.
8Asanjike dzanja lake pamutu pa nkhosayo, ndipo aiphere pa khomo la chihema chamsonkhano. Pambuyo pake ana a Aroni aliwaze magazi guwa molizungulira.
9Tsono pa nsembe yachiyanjanoyo yopereka kwa Chauta ndi yoyenera kuitentha pa moto, atapepo mafuta onse a nkhosayo, ndiye kuti mchira wonona wathunthu, ataudula m'tsinde pafupi ndi msana, mafuta okuta matumbo, mafuta ena onse okhala pamatumbopo,
10impso ziŵiri pamodzi ndi mafuta ake omwe, ndiponso mphumphu ya mafuta akuchiŵindi, ochotsa pamodzi ndi imso zija.
11Tsono wansembe atenthe zonsezo pa guwa, kuti zikhale chakudya chotentha pa moto, chopereka kwa Chauta.
12“Ngati munthu akuti apereke mbuzi, abwere nayo pamaso pa Chauta.
13Asanjike dzanja lake pamutu pa mbuziyo, ndipo aiphere pakhomo pa chihema chamsonkhano. Pambuyo pake ana a Aroni aliwaze magazi guwa molizungulira.
14Tsono pa nsembe yopereka kwa Chautayo ndipo yoyenera kuitentha pa moto, atapepo mafuta okuta matumbo ndi mafuta ena onse okhala pamatumbopo.
15Apatulenso imso ziŵiri pamodzi ndi mafuta ake omwe cham'chiwunomu, ndiponso mphumphu ya mafuta akuchiŵindi, ochotsa pamodzi ndi imso zija.
16Wansembe atenthe zonsezo pa guwa, kuti zikhale chakudya chotentha pa moto, cha fungo lokoma. Mafuta onse nga Chauta.
17Limeneli likhale lamulo lamuyaya pa mibadwo yanu yonse, kuti musadzadye mafuta kapena magazi kulikonse kumene mudzakhale.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.