1Onse amene ali mu ukapolo aziwona ambuye ao ngati oyenera kuŵachitira ulemu ndithu, kuti anthu anganyoze dzina la Mulungu ndiponso zimene timaphunzitsa.
2Amene ambuye ao ndi akhristu, asaŵapeputse poona kuti ndi abale. Kwenikweni aziŵatumikira koposa, popeza kuti amene amapindula ndi ntchito yao, nawonso ndi akhristu, ndiponso okondedwa.
Za chiphunzitso chonyenga ndi za chuma chenicheniUziŵaphunzitsa anthu ndi kuŵalamula ntchito zimenezi.
3Angathe kupezeka munthu wophunzitsa zosiyana ndi zimenezi, wosavomereza mau oona a Ambuye athu Yesu Khristu ndi chiphunzitso chogwirizana ndi moyo wolemekeza Mulungu.
4Munthu wotere ndi wodzitukumula ndi kunyada, sadziŵa kanthu. Mtima wake ngwodwala, wongofuna zotsutsanatsutsana ndi kukangana pa mau chabe. Zimenezi zimabweretsa kaduka, kusamvana, kusinjirirana, kuganizirana zoipa,
5kupsetsana mtima kosalekeza pakati pa anthu amene nzeru zao zidaonongekeratu ndipo sazindikiranso choona. Iwo amayesa kuti kupembedza Mulungu ndi njira yopatira chuma.
6Nzoonadi, kupembedza Mulungu kumapindulitsa kwambiri, malinga munthu akakhutira ndi zimene ali nazo.
7Sitidatenge kanthu poloŵa m'dziko lino lapansi, ndipo sitingathenso kutenga kanthu potulukamo.
8Tsono ngati tili ndi chakudya ndi zovala, zimenezi zitikwanire.
9Koma anthu ofuna kulemera, amagwa m'mayeso, amagwidwa mu msampha wa zilakolako zambiri zopusa ndi zoononga. Zilakolakozo zimamiza anthu m'chitayiko choopsa.
10Pajatu kukonda ndalama ndi gwero la zoipa zonse. Chifukwa cha kuika mtima pa ndalama anthu ena adasokera, adasiya njira ya chikhulupiriro, ndipo adadzitengera zoŵaŵitsa mitima.
Za nkhondo yabwino ya chikhulupiriro11Koma iwe, munthu wa Mulungu, uzipewe zonsezi. Uzikhala ndi mtima wofunafuna chilungamo, wolemekeza Mulungu, wokhulupirika, wachikondi, wolimbika ndi wofatsa.
12Uzimenya nkhondo yabwino ya kusunga chikhulupiriro, mpaka ukalandire moyo wosatha. Paja Mulungu adakuitanira zimenezi, ndipo udavomera bwino chikhulupiriro chako pamaso pa mboni zambiri.
13Yoh. 18.37Ndikukulamula pamaso pa Mulungu amene amapatsa moyo zinthu zonse, ndiponso pamaso pa Khristu Yesu amene popereka umboni pamaso pa Ponsio Pilato, adaanena zoona zenizeni.
14Ndikukulamula kuti, mopanda cholakwa kapena chokayikitsa, utsate bwino zonse zimene udalamulidwa, mpaka Ambuye athu Yesu Khristu adzabwerenso.
15Pa nthaŵi yake Mulungu adzamuwonetsa kwa ife. Mulunguyo ngwodala ndipo Iye yekha ndiye Wolamula, ndiye Mfumu ya mafumu onse, ndiponso Mbuye wa ambuye onse.
16Ndiye yekha wosafa, ndipo amakhala m'kuŵala kosayandikizika. Chikhalire palibe munthu amene adamuwona, palibenso amene angathe kumuwona. Kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu mpaka muyaya. Amen.
Za akhristu olemera17Anthu amene ali olemera pa zinthu zapansipano, uŵalamule kuti asanyade kapena kudalira chuma chimene sichidziŵika ngati chidzakhalitsa. Koma azidalira Mulungu amene amatipatsa zonse moolowa manja kuti tisangalale nazo.
18Uŵalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, oolowa manja, ndi okonda kugaŵana zinthu zao ndi anzao.
19Pakutero adzadziwunjikira chuma chokoma ndi chokhalitsa chimene chidzaŵathandize kutsogoloko, kuti akalandire moyo umene uli moyo weniweni.
Mau otsiriza20Iwe Timoteo, usunge bwino zimene adakusungitsa. Upewe nkhani zopanda pake, zosalemekeza Mulungu, ndiponso maganizo otsutsana, amene anthu amanama kuti ndi nzeru zodziŵa zinthu.
21Anthu ena, chifukwa chovomereza nzeru zotere, adasokera nkutaya chikhulupiriro chao.
Mulungu akukomere mtima.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.