Aro. 14 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Asamaweruza akhristu anzao

1 Akol. 2.16 Mlandireni bwino munthu amene chikhulupiriro chake nchofooka, koma osati kuti mutsutsane naye pa maganizo ake.

2Wina amakhulupirira kuti palibe choletsa kudya chakudya chilichonse. Koma wina, amene chikhulupiriro chake nchofooka, amadya zamasamba zokha.

3Amene amadya chilichonse, asanyoze mnzake amene amazisala. Amene amasala zinthu zina asaweruze mnzake amene amazidya, pakuti Mulungu wamulandira.

4Kodi iweyo ndiwe yani kuti uweruze wantchito wamwini kuti walakwa? Mbuye wake yekha ndiye aweruze ngati iye wakhoza kapena walephera pa ntchito yake. Ndipo adzakhoza, popeza kuti Ambuye angathe kumkhozetsa.

5Ena amaganiza kuti tsiku lakutilakuti ndi loposa masiku ena, koma pamene ena akuganiza kuti masiku onse nchimodzimodzi. Aliyense achite monga momwe watsimikizira kwenikweni mumtima mwake.

6Amene amasunga tsiku lakutilakuti, amatero kuti alemekeze Ambuye. Amene amadya chilichonse, amatero kuti alemekeze Ambuye, pakuti amayamika Mulungu chifukwa cha chakudyacho. Amene amasala zina, amatero kuti alemekeze Ambuye, ndipo amayamika Mulungu pakutero.

7Palibe ndi mmodzi yemwe mwa ife amene amakhala moyo chifukwa cha iye yekha, kapena kufa chifukwa cha iye yekha.

8Tikakhala ndi moyo, moyowo ndi wa Ambuye, tikafa, timafera Ambuye. Nchifukwa chake, ngakhale tikhale ndi moyo kapena tife, ndife ao a Ambuye.

9Paja Khristu adamwalira nakhalanso ndi moyo, kuti akhale Mbuye wa anthu akufa ndiponso wa anthu amoyo.

10 2Ako. 5.10 Tsono iwe, ukuweruziranji mbale wako? Kapena iwe winawe, ukunyozeranji mbale wako? Tonsefe tidzaima pamaso pa Mulungu kuti atiweruze.

11Yes. 45.23 Paja Malembo akunena kuti,

“Ambuye akuti,

‘Pali Ine ndemwe, anthu onse adzandigwadira

ndi kuvomereza kuti ndine Mulungu.’ ”

12Motero aliyense mwa ife adzadzifotokozera yekha kwa Mulungu zimene adazichita.

Asachimwitse abale ao achikhristu

13Tsono tiyeni tileke kumaweruzana. Makamaka mutsimikize kuti musachite kanthu kalikonse kophunthwitsa mbale wanu, kapena komchimwitsa.

14Pogwirizana ndi maganizo a Ambuye Yesu, ndikutsimikiza mosakayika konse kuti palibe chinthu chingadetse munthu pamaso pa Mulungu chifukwa wachikhudza. Koma ngati wina aganiza kuti chinthu nchomudetsa, kwa iyeyo chinthucho nchomudetsadi.

15Ngati ukhumudwitsa mbale wako pakudya chakudya cha mtundu wakutiwakuti, ndiye kuti sukuyendanso m'chikondi. Usamuwononge ndi chakudya chako munthu amene Khristu adamufera.

16Tsono musalole kuti anthu ena aziyese zoipa zinthu zimene inu mumaziwona kuti nzabwino.

17Mu ufumu wa Mulungu chachikulu si chakudya kapena zakumwa ai, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe, zimene Mzimu Woyera amapereka.

18Aliyense wotumikira Khristu motere, amakondweretsa Mulungu, ndipo amakhala wovomerezeka kwa anthu.

19Nchifukwa chake tsono tizifunafuna zimene zingathandize kuti pakhale mtendere ndiponso kugwirizana pakati pathu.

20Chakudya chisakuwonongetseni ntchito ya Mulungu. Zakudya zonse nzololedwa kuzidya, koma nkulakwa kudya chinthu chimene chingachimwitse anzathu.

21Nkwabwino kusadya nyama, kusamwa vinyo, ndiponso kusachita kanthu kalikonse kamene kangachimwitse mbale wako.

22Zimene iwe umakhulupirira pa zimenezi, zikhale pakati pa iweyo ndi Mulungu. Ngwodala amene mtima wake sumutsutsa pamene atsimikiza kuchita zakutizakuti.

23Koma munthu akamadya ali wokayika, waweruzidwa kale kuti ngwolakwa, popeza kuti zimene akuchita nzosagwirizana ndi zimene iye amakhulupirira kuti nzoyenera. Paja chilichonse chimene munthu achita, chotsutsana ndi zimene iye amakhulupirira, chimenecho ndi tchimo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help