Amo. 7 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Amosi aona dzombe

1Izi ndizo zimene Ambuye Chauta adandiwonetsa m'masomphenya: Chauta ankapanga dzombe pa nthaŵi yoti mfumu inali itamweta kale udzu, ndipo udzuwo unkaphukanso kachiŵiri.

2Pamene ndidaona kuti dzombelo ladya zomera zonse zam'dzikomo, ndidati,

“Inu Ambuye Chauta, ndapota nanu, khululukani.

Kodi anthu a Yakobeŵa angalimbike bwanji?

Iwoŵa ndi ofooka kwambiri.”

3Apo Chauta adakhululuka, ndipo adati,

“Zimenezi sizidzachitika konse.”

Amosi aona moto

4Zina ndi izi zimene Ambuye Chauta adandiwonetsa m'masomphenya: Ambuye Chauta ankaitana malaŵi a moto kuti alange anthu. Motowo udapsereza phompho lalikulu, nuyamba kuwononga minda yonse ya pa dziko lapansi.

5Tsono ine ndidati,

“Inu Ambuye Chauta,

ndapota nanu, basi lekani.

Kodi anthu a Yakobeŵa angalimbike bwanji?

Iwoŵa ndi ofooka kwambiri.”

6Apo Chauta adakhululuka,

ndipo adati, “Zimenezinso sizidzachitika konse.”

Amosi aona chingwe choongolera khoma

7Zina ndi izi zimene Chauta adandiwonetsa m'masomphenya: Ndidaona Iye ataima pamwamba pa khoma lomangamanga, m'manja mwake ali ndi chingwe choongolera khoma.

8Tsono Chautayo adandifunsa kuti, “Kodi iwe Amosi, nchiyani ukuwonachi?” Ine ndidayankha kuti, “Chingwe choongolera khoma.” Apo Chauta adati,

“Ndikuika chingwe chimenechi

pakati pa anthu anga Aisraele

kuti kuwoneke kukhota kwao,

choncho sindidzaŵalekereranso ai.

9Akachisi a ana a Isaki adzasanduka bwinja,

malo achipembedzo a Aisraele adzaonongedwa.

Ndipo ndidzagwetsa banja la mfumu

Yerobowamu pa nkhondo.”

Amosi ndi Amaziya

10Ku Betele kunali wansembe wina dzina lake Amaziya. Iyeyo adatumiza mthenga kwa Yerobowamu, mfumu ya ku Israele kuti, “Amosi akukuutsirani chiwembu pakati pa anthu a ku Israele. Anthu sangathe kuvomera zonse zimene iye akunenazo.

11“Amosiyo akunena kuti,

‘Yerobowamu adzafa pa nkhondo,

ndipo Aisraele adzatengedwa

kunka ku ukapolo,

kutali ndi dziko lao.’ ”

12Tsono Amaziya adauza Amosi kuti, “Mlosi iwe, choka kuno! Thaŵira ku dziko la Yuda! Uzikalosa kumeneko, ndipo anthu akumeneko azikakudyetsa.

13Koma usakalosenso ku Betele poti kumeneko ndi malo opatulika a mfumu, ndiponso ndi Nyumba ya Mulungu ya m'dziko lino.”

14Amosi adayankha Amaziya kuti, “Ine sindine mneneri konse, kapenanso wa m'gulu la aneneri. Inetu ndine woŵeta nkhosa, ndiponso wolima nkhuyu.

15Chauta adachita kukanditenga, kundileketsa ntchito yoŵeta nkhosa, nandiwuza kuti, ‘Pita, ukalalikire anthu anga, Aisraele.’

16“Nchifukwa chake tsono imva mau

amene Chauta akunena.

Iweyo ukundiwuza kuti ndisalose zotsutsa Israele,

ndisalalike zotsutsa banja la Isaki.

17Tsono zimene akunena Chauta ndi izi:

‘Mkazi wako adzasanduka mkazi wadama mumzindamu.

Ndipo ana ako aamuna ndi aakazi adzaphedwa pa nkhondo.

Dziko lako adzaligaŵagaŵa kugaŵira anthu ena.

Iweyo ukafera ku dziko lachikunja.

Ndipo Aisraele adzatengedwa kunka ku

ukapolo kutali ndi dziko lao.’ ”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help