Yes. 30 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kupusa kwa kukhulupirira Ejipito

1Chauta akuti,

“Tsoka kwa ana ondipandukira Ine!

Amachita zodzikonzera okha

osati zokonza Ine.

Amachita chipangano chaochao,

chosatsata chifuniro changa,

ndipo amanka nachimwirachimwira.

2Amapita ku Ejipito kukapempha chithandizo,

Ine osandifunsa.

Amathaŵira kwa Farao

kuti aŵatchinjirize,

amakafuna malo opulumukirako ku Ejipito.

3Koma kutchinjiriza kwa Farao

kudzakuchititsani manyazi,

ndipo malo opulumukirako a ku

Ejipitowo mudzachita nawo manyazi.

4Ngakhale kuti nduna zake zafika kale ku Zowani,

ndipo akazembe ake afika kale ku Hanesi,

5anthu onse a ku Yuda adzamva manyazi

chifukwa cha anthu opanda nawo phindu

ndipo osaŵathandiza konse,

koma ongobweretsa manyazi.”

6Nawu ulosi wonena za nyama za ku chipululu chakumwera:

Akazembe akuyenda m'dziko loopsa

m'mene muli mikango, mphiri ndi njoka zouluka.

Amasenzetsa abulu ao mphatso zamtengowapatali

ndipo chuma chao amasenzetsa ngamira zao,

kupita kwa mtundu wa anthu umene sungaŵathandize.

7Chithandizo cha Ejipito nchachabe ndi chopanda phindu,

choncho dzikolo ndalitcha dzina lakuti

“Chilombo cholibwidika.”

Za anthu osamvera

8Mulungu adandiwuza kuti,

“Tsopano pita, ukalembe zimenezi pa sileti iwo akuwona,

ukazilembenso m'buku,

kuti kutsogolo zidzakhale umboni wosatha.

9Ameneŵa ndi anthu opandukira Mulungu,

ana onama, okana kumvera malangizo a Chauta.

10Amauza oona zobisika kuti, ‘Musaonenso.’

Amauza aneneri kuti,

‘Musatiloserenso zoona.

Mutiwuze zotikomera,

mutilosere zam'mutu chabe.

11Chokani apa, osakhala pa njira.

Sitifuna kumvanso za Woyera uja wa Israele.’ ”

12Nchifukwa chake Woyera uja wa Israele akunena kuti,

“Inu mumanyozera zimene ndimakuuzani,

mumakhulupirira zopsinja anzanu

ndipo mumadalira mabodza.

13Nchifukwa chake tchimo lanuli

lidzakhala ngati mng'ankha

pa chipupa chachitali choŵinuka,

chimene kugwa kwake nkwadzidzidzi.

14Zidzakhala ngati kuphwanyika kwa mbiya,

imene ili yotekedzekeratu,

popanda ndi phale lomwe lopalira moto,

kapena lotungira madzi m'chitsime.”

15Tsono Ambuye Chauta, Woyera uja wa Israele adati,

“Ngati mutembenuka ndi kubwerera,

mudzapulumuka.

Ngati mudzinga ndi kukhulupirira,

mudzakhala amphamvu.”

Koma inu mudakana kutero.

16Mudati, “Tidzathamanga pa akavalo.”

Chabwino, mudzathaŵe!

Mudatinso,

“Tidzakwera pa magareta aliŵiro.”

Chabwino, koma okuthamangitsani

adzakhalanso aliŵiro.

17Anthu chikwi chimodzi mwa inu

adzathaŵa poona mdani mmodzi.

Asilikali asanu okha

adzakwanira kukuthamangitsani.

Otsalira mwa inu

adzakhala ngati mtengo wa mbendera wapaphiri,

ngati chizindikiro chapagomo.

18Komabe Chauta akufunitsitsa kuti akukomereni mtima.

Ali wokonzeka kuti akuchitireni chifundo,

chifukwa Chauta ndi Mulungu wachilungamo.

Ndi odala onse amene amakhulupirira Iye!

Mulungu adzadalitsa anthu ake

19Ndithudi, inu anthu a ku Ziyoni, okhala ku Yerusalemu, simudzaliranso. Mulungu adzakukomerani mtima pamene adzamva kulira kwanu, ndipo akadzangomva, pompo adzakuyankhani.

20Ngakhale Ambuye adzakuloŵetseni m'zovuta, adzakhala komweko kumakuphunzitsani, sadzabisala, mudzaŵaona.

21Pamene mupatukira kumanja kapena kumanzere, mudzamva kumbuyo kwanu mau okulozerani njira oti, “Njira ndi iyi, muyende m'menemu.”

22Pamenepo mudzatenga mafano anu, ena okutidwa ndi siliva, ena okutidwa ndi golide, ndipo mudzaŵataya ngati zinyalala, ndikunena kuti, “Zichoke zonsezi!”

23Mukamadzabzala mbeu zanu, Chauta adzakugwetserani mvula kuti zimere, ndipo mudzakolola zambiri. Tsiku limenelo ng'ombe zanu zidzapeza mabusa aakulu.

24Ng'ombe ndi abulu zokuthandizani kulima zidzadya chakudya chamchere chopapasa ndi fosholo ndi chifoloko.

25Pa tsiku limene nsanja zankhondo za adani anu zidzagwe, anthu ake naphedwa, pa phiri lililonse lalikulu ndi pa gomo lililonse lalitali, padzayenda mitsinje ya madzi.

26Mwezi udzaŵala ngati dzuŵa, ndipo dzuŵa lidzaŵala kwambiri ngati kasanunkaŵiri kuŵala kwa pa tsiku limodzi. Zimenezi zidzachitika pamene Chauta adzamange ndi kupoletsa zilonda zimene Iye yemwe adachititsa pakuŵalanga anthu ake.

Mulungu adzalanga Asiriya

27Onani, ulemerero wa Chauta

ukuwonekera kuchokera kutali.

Akuwonetsa mkwiyo m'kati mwa moto

ndi m'kati mwa chiwutsi chatolotolo.

Akulankhula mwaukali,

ndipo mau ake akutentha ngati moto woononga.

28Mpweya wake uli ngati mtsinje wosefukira,

wa madzi oyesa m'khosi.

Akusefa anthu a mitundu ina ndi sefa wosakaza.

Ngati akavalo, akuŵaika m'kamwa

chitsulo choti chiŵasokeretse.

29Koma inu anthu a Mulungu, mudzakondwa ndi kuimba monga m'mene mumachitira usiku pa chikondwerero chopatulika. Mudzasangalala ngati anthu opita naimba toliro ku phiri la Chauta, thanthwe la Israele.

30Chauta adzamveketsa liwu lake loopsa, ndipo anthu adzaona dzanja lake likutsika pa iwo, ndi ukali woopsa ndi malaŵi a moto woononga, pakati pa mphezi, namondwe ndi matalala.

31Aasiriya adzaopsedwa ndi liwu la Chauta, pamene Iye adzaŵakantha ndi ndodo yake.

32Pamene Mulungu adzakhala akuŵalanga adani aja, anthu ake adzakhala akuvina ndi ting'oma ndi azeze. Mulungu mwini adzamenyana ndi Aasiriya.

33Malo otenthera zinthu ndi okonza kale, adakonzera mfumu ya ku Asiriya. Malowo ndi ozama ndi aakulu, odzaza ndi moto ndi nkhuni. Tsono mpweya wa Chauta, wonga ngati mtsinje wa sulufure, udzakoleza motowo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help