Yer. 7 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Chipembedzo chabodza ndi chilango chake

1Chauta adauza Yeremiya mau aŵa akuti,

2“Ima pa chipata cha Nyumba ya Chauta ndipo kumeneko ukalalike kuti: Imvani mau a Chauta, inu nonse anthu a ku Yuda, amene mumaloŵa pa chipata ichi kudzapembedza Chauta.

3Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akukuuzani kuti, Konzani makhalidwe ndi zochita zanu, ndipo ndidzakulolani kumakhala pa malo ano.

4Musamangodzinyenga ndi maganizo akuti muli pabwino ponena kuti, ‘Malo ano ndi Nyumba ya Chauta, Nyumba ya Chauta, Nyumba ya Chauta!’

5“Konzani makhalidwe anu ndi zochita zanu. Muzichitirana zolungama.

6Musazunze alendo kapena ana amasiye kapena akazi amasiye. Musaphe anthu osachimwa pa malo ano. Musamatsate milungu ina, kuti ingakuwonongeni.

7Mukamvera mau anga, ndidzakulolani kuti mukhale pa malo ano, m'dziko limene ndidapatsa makolo anu mpaka muyaya.

8“Koma onani, inu mumakhulupirira mabodza.

9Mumaba, mumapha, mumachita zigololo, mumalumbira zonama, mumapereka nsembe zopsereza kwa Baala, mumatsata milungu ina imene kale simunkaidziŵa.

10Pambuyo pake mumabwera kudzaima pamaso panga m'Nyumba ino, Nyumba imene imadziŵika ndi dzina langa. Mumanena kuti, ‘Tapulumuka ife,’ koma mumapitirirabe kumangochita zonyansa zonsezi.

11Mt. 21.13; Mk. 11.17; Lk. 19.46 Kodi tsopano Nyumba ino, Nyumba imene imadziŵika ndi dzina langayi, yasanduka phanga lobisalamo mbala zachifwamba, inu mukuwonerera? Mwiniwakene ndaziwona zonsezi,” akuterotu Chauta.

12Yos. 18.1; Mas. 78.60; Yer. 26.6 “Pitani ku malo anga ku Silo, malo amene poyamba ankadziŵika ndi dzina langa. Mukaone zimene ndidachita kumeneko chifukwa cha kuipa kwa anthu anga Aisraele.

13Munkachita zoipa zonsezi, mudakana kundimvera nditakulankhulani kosalekeza, ndipo simudayankhe pamene ndidakuitanani.

14Nchifukwa chake zomwe ndidachita ku Silo, ndidzachitanso ku Nyumba ino, imene imadziŵika ndi dzina langa, malo amene inu mumaŵakhulupirira, malo amene ndidakupatsani inu pamodzi ndi makolo anu.

15Ndidzakuchotsani pamaso panga monga momwe ndidachotsera abale anu onse, zidzukulu zonse za Efuremu.

Za kusamvera kwa anthu

16“Iwe Yeremiya, usaŵapempherere anthu ameneŵa. Usaŵapepesere kwa Ine kapena kuŵadandaulira mondiwumiriza chifukwa Ine sindikumvera.

17Kodi sukuwona zimene zikuchitika m'mizinda ya ku Yuda ndi m'miseu ya m'Yerusalemu?

18Yer. 44.17-19 Ana akutolera nkhuni, atate akusonkha moto, akazi akukanda ufa kuti aphike makeke, kuchitira ulemu amene amati ndi mfumukazi yakumwamba. Iwowo amathira nsembe yazakumwa kwa milungu ina, kuti andipsetse mtima.

19Amati atani! Amayesa kuti akuvuta Ine, koma akungodzivuta okha ndi kumadzichititsa manyazi.

20Nchifukwa chake ndidzaŵalanga koopsa mwaukali. Mkwiyo wanga udzagwera Nyumba yangayi, anthu, nyama, mitengo ndi mbeu zomwe. Mkwiyowo udzayaka ngati moto wosazimika.”

21Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, “Muwonjeze zopereka zanu zopsereza pa nsembe zanu zinazo, ndipo mudye nyama yake.

22Pamene ndidatulutsa makolo anu ku dziko la Ejipito, sindidaŵalamule kuti azipereka nsembe zopsereza kapena nsembe zina.

23Koma chimene ndidaalamula nchimodzi, ndidati, ‘Mukamandimvera, ndidzakhala Mulungu wanu, ndipo inu mudzakhala anthu anga. Muzitsata malamulo anga onse kuti zinthu zikukomereni!’

24Koma anthuwo sadamvere, sadasamaleko, ndipo adapitirira kukhala osamvera ndi mitima yao yoipa. Adayang'ana zam'mbuyo osati zakutsogolo.

25Kuyambira tsiku limene makolo anu adatuluka ku dziko la Ejipito mpaka lero lino, ndakhala ndikukutumizirani atumiki anga aneneri kaŵirikaŵiri.

26Komabe inu simudandimvere, simudasamaleko. Ndi mitima yanu yokanika, mwaipa kupambana makolo anu.

27“Iwe ungaŵauze zimenezi, sadzakumvera. Ungaŵaitane, sadzakuyankha.

28Nchifukwa chake udzaŵauze kuti, ‘Uwu ndi mtundu wa anthu uja sadamvere mau a Chauta Mulungu wao, ndipo sadafune kukonzeka. Mau oona atheratu ndipo pakamwa pamangonena zonama zokhazokha.’

Machimo a m'chigwa cha Benihinomu

29“Meta tsitsi lako, ndipo ulitaye.

Ulire kwambiri pa zitunda zopanda zomera,

poti Chauta waukana mbadwo uwu umene wamkwiyitsa.

Anthu amenewo Iye waŵasiyadi.”

30Chauta akuti, “Anthu a ku Yuda achita zoipa Ine ndikuwona. Aimika mafano ao onyansa m'Nyumba ino imene imadziŵika ndi dzina langa, ndipo aiipitsa.

312Maf. 23.10; Yer. 32.35; Lev. 18.21 Amanga nsanja yotchedwa Tofeti m'chigwa cha Benihinomu, kuti atenthereko ana ao aamuna ndi aakazi. Zimenezo sindidalamule konse, ngakhale kuziganiza komwe.

32Nchifukwa chake nthaŵi ikubwera pamene malo ano sadzatchedwanso Tofeti, kapena za Chigwa cha Benihinomu, koma za Chigwa cha Chipheiphe, pakuti anthu akufa adzaŵaika ku Tofeti, chifukwa choti sikudzapezekanso malo owaika.

33Tsono mitembo ya anthu ameneŵa idzakhala chakudya cha mbalame zamumlengalenga ndi zilombo zakuthengo. Ndipo palibe wina amene adzazipirikitse.

34Yer. 16.9; 25.10; Bar. 2.23; Chiv. 18.23 Sikudzamvekanso mau achisangalalo ndi achimwemwe ku mizinda ya ku Yuda ndi ku miseu ya mu Yerusalemu. Sikudzamvekanso mau achikondwerero, a mkwati wamwamuna ndi wamkazi. Ndithudi dzikolo lidzasanduka chipululu.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help