1 Eks. 27.1, 2 Solomoni adapanga guwa lamkuŵa, m'litali mwake mamita asanu ndi anai, m'mimba mwake asanu ndi anainso, ndipo msinkhu wake pafupi mamita anai ndi theka.
2Pambuyo pake adapanga thanki. Thankilo linali loulungika. Pakamwa pake panali pa mamita anai ndi theka, kuyesa modutsa pakati pake. Msinkhu wake unali wa mamita aŵiri nkanthu, ndipo kuzungulira m'thunthu mwake munali mamita 13 ndi theka.
3M'munsi mwa milomomu adaazokotamo tizikho kuzunguliza thunthu lonse la thankilo, ndiye kuti dera lonse la mamita 13 ndi theka. Tizikhoto tinali m'mizere iŵiri, ndipo adaatipangira kumodzi ndi thankilo pamene ankalipanga.
4Adalisanjika pa ng'ombe zamkuŵa khumi ndi ziŵiri: zitatu kuyang'ana kumpoto, zitatu kuyang'ana kuzambwe, zitatu kuyang'ana kumwera, zitatu kuyang'ana kuvuma. Thankilo linali litakhazikika pa ng'ombezo, ndipo miyendo yonse yam'munsi ya ng'ombezo idaaloza cham'kati.
5Thankilo kuchindikira kwake kunali ngati chikhatho. M'milomo mwake munkaoneka ngati m'milomo mwa chikho, ngati duŵa la kakombo. Munkaloŵa madzi okwanira malitara 60,000.
6Eks. 30.17-21 Adapanganso mabeseni khumi osambiramo. Kumwera adaikako asanu ndipo kumpoto adaikakonso asanu. M'menemo ndimonso ankatsukiramo zinthu zimene ankagwiritsa ntchito popereka nsembe zopsereza. Koma m'thanki lalikulu lija ndimo m'mene ankasambiramo ansembe.
7 Eks. 25.31-40 Eks. 25.23-30 Pambuyo pake adapanga zoikapo nyale khumi zagolide monga momwe kudaalembedwera, ndipo adaziika m'Nyumba ya Chauta, zisanu kumwera, zisanu zina kumpoto.
8Adapanganso matebulo khumi, ndipo adaŵaika m'Nyumba ya Chauta, asanu kumwera, asanu ena kumpoto. Ndipo adapanga mabeseni agolide okwanira 100.
9Adapanga bwalo la ansembe, bwalo lalikulu, ndiponso zitseko za bwalo, nazikuta ndi mkuŵa.
10Ndipo adaika thanki lija pa ndonyo yakumwera ya Nyumbayo.
11Huramu adapanganso mikhate, mafosholo ndi mabeseni ambiri. Motero Huramu adamatsiriza ntchito ya Nyumba ya Chauta imene ankagwirira mfumu Solomoni:
12ndiye kuti kumanga nsanamira ziŵiri zija, kupanga makapotolosi aŵiri aja okhala pamwamba pa nsanamirazo, ndiponso maukonde aŵiri aja ophimba ziwaya ziŵiri zija za kunsonga kwa makapotolosi aja okhala pamwamba pa nsanamira. Adapanganso maukonde aŵiri ovundikira pamwamba pa mbale ziŵiri za pa mitu imene inali pamwamba pa nsanamira ija.
13Adatsirizanso kupanga makangaza 400 amaukonde aŵiri aja, mizere iŵiri ya makangaza pa ukonde uliwonse, kuphimbira ziwaya ziŵiri zija za ku kunsonga kwa makapotolosi okhala pamwamba nsanamira zija.
14Ndiponso adatsiriza maphaka ndi mbiya zokhala pa maphakawo,
15thanki lija, ndipo ng'ombe khumi ndi ziŵiri zosanjikapo thankilo.
16Mikhate, mafosholo, mafoloko ndiponso zipangizo zonse zofunikira pa zimenezi, Huramuabi adazipanga za mkuŵa wonyezemira, kupangira mfumu Solomoni ku Nyumba ya Chauta.
17Mfumu idapangitsa zimenezi m'chigwa cha Yordani, ku malo amtapo amene ali pakati pa Sukoti ndi Zereda.
18Solomoni adapangitsa zinthu zimenezo zochuluka kwambiri, kotero kuti kulemera kwa mkuŵawo sikudadziŵike ai.
19Solomoni adapangitsanso zinthu zonse zimene zinali m'Nyumba ya Mulungu: ndiye kuti guwa lagolide, matebulo a buledi woperekedwa kwa Mulungu.
20Zoikaponyale pamodzi ndi nyale zake za golide weniweni, kuti ziziyaka m'kati mwenimweni mwa malo opatulika, monga kudaalembedwera.
21Adapangitsa maluŵa, nyale ndiponso mbano za golide weniweni.
22Zozimira nyale, mabeseni, mbale zofukiziramo lubani ndiponso ziwaya zopalira moto, zonsezi za golide weniweni. Ndipo adapangitsa zomangira zitseko za Nyumba ya Chauta ija, zitseko zam'kati zoloŵera ku malo opatulika kopambana, ndiponso zitseko zoloŵera m'Nyumba ya Chauta, zonsezo zinali zagolide.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.