1Tamandani Chauta!
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga.
2Ndidzatamanda Chauta pa moyo wanga wonse.
Ndidzaimba nyimbo zotamanda Mulungu wanga
nthaŵi zonse pamene ndili moyo.
3Musakhulupirire mafumu
kapena anthu ena amene sangathe kuthandiza.
4Pamene mpweya wa munthu uchokeratu,
munthuyo amabwerera ku dothi,
zimene ankafuna kuchita, zimatha tsiku lomwelo.
5Ngwodala munthu amene chithandizo chake
chimafumira kwa Mulungu wa Yakobe,
munthu amene amakhulupirira Chauta, Mulungu wake.
6 Ntc. 4.24; 14.15 Chauta adalenga kumwamba ndi dziko lapansi,
nyanja ndi zonse zimene zili m'menemo.
Amasunga malonjezo ake nthaŵi zonse.
7Amachitira anthu opsinjidwa zolungama,
amaŵapatsa chakudya anthu anjala.
Chauta amamasula am'ndende.
8Chauta amatsekula maso a anthu osapenya,
Chauta amakweza anthu otsitsidwa.
Chauta amakonda anthu ochita chilungamo.
9Chauta amateteza alendo,
amachirikiza mkazi wamasiye
ndiponso mwana wamasiye.
Koma njira za anthu oipa amazipotoza.
10Chauta adzakhala mfumu mpaka muyaya,
Mulungu wako, iwe Ziyoni,
adzalamulira ku mibadwo yonse.
Tamandani Chauta!
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.