Gen. 45 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yosefe adziwulula kwa abale ake

1 Ntc. 7.13 Pamenepo Yosefe sadathenso kudzigwira pamaso pa onse omtumikira aja. Adanena mokweza mau kuti, “Onse atuluke muno.” Motero panalibe ndi mmodzi yemwe wotsalira pamene Yosefe ankadziwulula kwa abale ake aja.

2Adalira momveka kotero kuti Aejipito adamva ndithu, ndipo mbiri ya zimenezo idakafika mpaka kwa mfumu.

3Yosefe adauza abale ake kuti, “Ine ndine Yosefe. Kodi bambo wanga akali moyo?” Koma abale akewo adadzazidwa ndi mantha, kotero kuti sadathenso nkumuyankha komwe.

4Tsono Yosefe adaŵauza kuti, “Chonde senderani pafupi.” Onse atabwera pafupi, Yosefe adati, “Ine ndine mbale wanu uja Yosefe, amene mudamgulitsa ku Ejipito.

5Koma tsopano musataye mtima kapena kuvutika, popeza kuti Mulungu mwiniwake ndiye amene adanditumiziratu kuno, kuti motero apulumutse moyo wanu.

6Chaka chino ndi chaka chachiŵiri cha njala. Koma zakhalabe zaka zisanu, ndipo pa zaka zimenezi anthu sadzalima kapena kukolola.

7Mulungu adanditumiziratu ine kuno kuti ndikupulumutseni, kuti choncho ziwoneke zidzukulu zanu zambiri.

8Motero sindinu amene mudanditumiza kuno ai, koma Mulungu. Iye wandisandutsa nduna yaikulu ya Farao. Dziko lonse lino lili m'manja mwanga. Ejipito yense ndikulamulira ndine.

9Ntc. 7.14 Tsopano fulumirani, bwererani kwa bambo wanga, mukamuuze kuti mwana wanu Yosefe akunena kuti, ‘Mulungu wandikuza mpaka kukhala wolamulira Ejipito yense, tsono bwerani kuno, musachedwe.

10Mungathe kudzakhala kuno ku dziko la Goseni, kuti mukhale pafupi ndi ine. Mudzakhale kuno inuyo, ana anu, zidzukulu zanu, nkhosa zanu ndi mbuzi zomwe, ng'ombe zanu pamodzi ndi zonse zimene muli nazo.

11Mukadzakhala ku Goseni, ine ndizidzakusamalani. Zaka za njala zikalipobe zisanu. Sindifuna kuti inu musauke pamodzi ndi banja lanu, ndi onse amene muli nawo.’

12Tsono nonsenu ndi Benjamini, mng'ono wangayu, mungathe kuwona kuti ndinedi amene ndikulankhula nanu.

13Muuzeni bambo wanga kuti ndili pa ulemerero waukulu ku Ejipito kuno. Mukamuuzenso bambo wanga zonse zimene mwaonazi ndipo fulumirani, mubwere naye kuno.”

14Atatero adakumbatira Benjamini, mng'ono wake uja, nayambanso kulira. Benjamini nayenso adayamba kulira atangomkumbatira.

15Pambuyo pake adaŵampsompsona abale ake onse aja akulira. Kenaka abale ake aja adayamba kucheza naye Yosefe.

16Zitamveka kunyumba kwa Farao kuti abale a Yosefe abwera, Faraoyo ndi antchito ake onse adakondwa kwambiri.

17Ndipo Farao adauza Yosefe kuti, “Uŵauze abale ako kuti asenzetse nyama zao katundu, ndipo abwerere ku Kanani.

18Tsono kumeneko akatenge bambo wao ndi mabanja ao, ndipo adzabwere kwa ine kuno. Ndidzaŵapatsa dziko lachonde ku Ejipito kuno, ndipo azidzadya za m'dziko lino.

19Uŵauze kuti atenge ngolo za kuno ku Ejipito, kuti akazi ao akakwerepo pamodzi ndi ana omwe. Ndithu akamtenge bambo wao akabwere kuno.

20Asakade nkhaŵa kuti asiya katundu wao kumeneko, chifukwa dziko lokoma lachonde la ku Ejipito kuno lidzakhala lao.”

21Tsono ana a Israele adachitadi zimenezo. Yosefe adaŵapatsa ngolo monga Farao adaalamulira, naŵapatsa phoso lapaulendo.

22Adapatsanso aliyense zovala zachikondwerero, koma Benjamini adampatsa mashikeli asiliva okwana 300, ndi zovala zisanu zachikondwerero.

23Bambo wake adamtumizira abulu khumi osenza zipatso zokoma za ku Ejipito, ndi abulu khumi osenza tirigu, buledi ndi zakudya zina za bambo wake zapaulendo.

24Tsono adaŵauza abale akewo kuti azipita, ndipo ponyamukapo adanena kuti, “Musakangane pa njira.”

25Tsono iwo adachoka ku Ejipito, kubwerera ku Kanani kwa bambo wao Yakobe.

26Atafika, adauza bambo wao kuti, “Yosefe ujatu ali moyo! Ndiye wolamulira Ejipito yense!” Yakobe adachita ngati wakomoka, pakuti sadakhulupirire zonena zaozo.

27Komabe iwo atamuuza zonse zimene Yosefe adaaŵauza, ndipo iye ataona ngolo zimene Yosefe adaatumiza kuti iye akwerepo popita ku Ejipito, Yakobe adayamba kutsitsimuka.

28Tsono adati, “Basi chabwino, mwana wanga Yosefe akali moyo. Ndipita ndikamuwone ndisanafe.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help