1Inu Mulungu, onetsani kuti ine ndine wosalakwa,
munditchinjirize pa mlandu wanga
kwa anthu osasamala za Mulungu.
Mundipulumutse kwa anthu onyenga ndi opanda chilungamo.
2Ndithu Inu ndinu Mulungu wamphamvu
amene ndimathaĊµirako.
Mwanditayiranji?
Ndiziyenderanji ndilikulira
chifukwa chondipsinja mdani wanga?
3Tumizani kuĊµala kwanu ndi choona chanu
kuti zinditsogolere.
Zindifikitse ku phiri lanu loyera,
kumalo kokhala Inu.
4Tsono ndidzapita ku guwa lansembe la Mulungu,
kwa Mulungu amene amandipatsa chimwemwe chopambana.
Ndipo ndidzakutamandani ndi pangwe,
Inu Mulungu, Mulungu wanga.
5Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga?
Chifukwa chiyani ukuvutika choncho m'kati mwanga?
Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamtamandanso,
Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.