1Inu okondedwa, musamakhulupirira maganizo aliwonse, koma muziŵayesa maganizowo kuti muwone ngati ndi ochokeradi kwa Mulungu. Paja aneneri ambiri onama awanda ponseponse.
2Mungathe kuzindikira Mzimu wa Mulungu motere: aliyense wovomereza kuti Yesu Khristu adadzakhaladi munthu, ameneyo ndi wochokera kwa Mulungu.
3Koma aliyense wosavomereza Yesu, ameneyo ndi wosachokera kwa Mulungu. Maganizo akewo ndi ochokera kwa Woukira Khristu, yemwe uja mudamva kuti akubwerayu; ndipotu wafika kale m'dziko lapansi.
4Koma inu, ana anga, ndinu ake a Mulungu, ndipo mwaŵapambana aneneri onamawo. Pakuti Iye amene ali mwa inu, ndi wopambana iye uja amene ali mwa anthu odalira zapansipano.
5Aneneri onamawo ndi apansipano, nchifukwa chake zimene amalankhula nzapansipano, ndipo anthu odalira zapansipano amaŵamvera.
6Koma ife ndife ake a Mulungu. Munthu wodziŵa Mulungu, amatimvera. Koma iye amene sali wake wa Mulungu, satimvera. Umu ndi m'mene timasiyanitsira pakati pa maganizo oona ndi maganizo onama.
Mulungu ndiye chikondi7Inu okondedwa, tizikondana, pakuti chikondi nchochokera kwa Mulungu. Aliyense amene ali ndi chikondi, ndi mwana wa Mulungu, ndipo amadziŵa Mulungu.
8Koma munthu wopanda chikondi sadziŵa Mulungu, pakuti Mulungu ndiye chikondi chimene.
9Mulungu adaonetsa chikondi chake kwa ife motere: Iye nkukhala ndi Mwana mmodzi yekha, koma adamtuma pansi pano, kuti mwa Iye tikhale ndi moyo.
10Chikondi chenicheni ndi ichi, chakuti sindife tidakonda Mulungu ai, koma Mulungu ndiye adatikonda ifeyo, natuma Mwana wake kuti akhale nsembe yopepesera machimo athu.
11Inu okondedwa, ngati Mulungu adatikonda kwambiri chotere, ifenso tiyenera kumakondana.
12Yoh. 1.18Palibe munthu amene adaona Mulungu. Koma tikamakondana, Mulungu amakhala mwa ife, ndipo chikondi chake chafika pake penipeni mwa ife.
13Tikudziŵa kuti timakhala mwa Mulungu, ndipo Iyenso amakhala mwa ife, chifukwa adatipatsa Mzimu wake Woyera.
14Ife taona, ndipo tikuchita umboni, kuti Atate adatuma Mwana wake kuti adzakhale Mpulumutsi wa anthu a pa dziko lonse lapansi.
15Aliyense wovomereza kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu, Mulungu amakhala mwa iye, ndipo iye amakhala mwa Mulungu.
16Motero ife timadziŵa ndipo timakhulupirira ndithu kuti Mulungu amatikonda.
Mulungu ndiye chikondi, ndipo munthu wokhala ndi moyo wachikondi, amakhala mwa Mulungu, Mulungunso amakhala mwa iye.
17Pamene chikondi chafikira pake penipeni mwa ife ndi apa pakuti moyo wathu pansi pano uli wonga moyo wa Khristu, kotero kuti tingathe kukhala olimba mtima pa tsiku la chiweruzo.
18Munthu amene ali ndi chikondi, alibe mantha, pakuti chikondi changwiro chimatulutsira mantha kunja. Munthu akamachita mantha, ndiye kuti akuwopa chilango, ndipo chikondi sichidafike pake penipeni mwa iye.
19Ife timakonda Mulungu chifukwa ndiye adayamba kutikonda.
20Wina akamanena kuti, “Ndimakonda Mulungu”, komabe nkumadana ndi mbale wake, ndi wonama ameneyo. Pakuti munthu wosakonda mbale wake amene wamuwona, sangathe kukonda Mulungu amene sadamuwone.
21Lamulo limene Iye adatipatsa ndi lakuti, wokonda Mulungu azikondanso mbale wake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.