1Balamu adauza Balaki kuti, “Mundimangire maguwa asanu ndi aŵiri pano, ndipo mundikonzere ng'ombe zamphongo zisanu ndi ziŵiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziŵiri.”
2Balaki adachitadi monga momwe adamuuzira Balamu. Ndipo Balaki pamodzi ndi Balamu adapereka ng'ombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo pa guwa lililonse.
3Apo Balamu adauza Balaki kuti, “Imani pafupi ndi nsembe yanu yopsereza, tsono ine ndipite, mwina mwake Chauta abwera kudzakumana nane. Chilichonse chimene andiwonetse ndidzakuuzani.” Choncho adapita pamwamba pa phiri.
4Mulungu adakumana ndi Balamu, ndipo Balamuyo adati, “Ndakonza maguwa asanu ndi aŵiri, ndipo pa guwa lililonse ndaperekapo ng'ombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo.”
5Tsono Chauta adauza Balamu kuti “Bwerera kwa Balaki, ukamuuze izi! Izi”
6Balamu adabwerera kwa Balaki, nampeza iyeyo pamodzi ndi akalonga onse a Amowabu ataima pafupi ndi nsembe yake yopsereza.
7Apo Balamu adayamba kulankhula mau auneneri, adati,
“Balaki mfumu ya ku Mowabu yandiitana
kuchokera ku Aramu,
ku mapiri akuvuma, kuti,
‘Bwerani, dzatemberereni Yakobe m'malo mwanga,
bwerani mudzamfunire Israele zoipa.’
8Koma ine ndingathe bwanji kumtemberera
amene Mulungu sadamtemberere?
Ndingathe bwanji kumufunira zoipa
amene Chauta sadamfunire zoipa?
9Pamene ndikuŵaona kuchokera pamwamba pa phiri,
pamene ndikuŵayang'ana kuchokera ku mapiri,
ndikuwona anthu okhala paokha,
osadziŵerengera kumodzi ndi mitundu ina.
10Ndani angathe kuŵerenga zidzukulu,
zidzukulu za Yakobe zochuluka ngati fumbi,
kapena kuŵerenga ngakhale chimodzi
mwa zigawo zinai za fuko lonse la Israele?
Lekeni ine ndife imfa ya anthu amene mudaŵalungamitsa,
matsiriziro anga akhale onga a anthu amenewo.”
11Balaki adafunsa Balamu kuti, “Mwandichitira zotani? Suja ndidakuitanani kuti mudzatemberere adani anga, koma m'malo mwake mwangoŵadalitsa.”
12Iye adayankha kuti, “Kodi sindiyenera kulankhula zokhazo zimene Chauta adaika m'kamwa mwanga?”
Mau achiŵiri auneneri a Balamu13Balaki adamuuzanso kuti, “Tiyeni tipite limodzi ku malo ena kumene mungathe kuŵaona Aisraelewo. Mukangoona okhawo amene ayandikira pafupi, koma simukaona onse. Tsono muŵatemberere m'malo mwanga, mutaima pamenepo.”
14Adapita naye ku munda wa Zofimu pamwamba pa phiri la Pisiga, namangapo maguwa asanu ndi aŵiri, ndipo adapereka nsembe ya ng'ombe yamphongo ndi nsembe ya nkhosa yamphongo pa guwa lililonse.
15Balamu adauza Balaki kuti, “Imani pano pafupi ndi nsembe yanu yopsereza, ine ndipite ndikakumane ndi Chauta apo.”
16Chauta adakumana naye Balamu namuuza kuti, “Bwerera kwa Balaki, ndipo umuuze izi! Izi!”
17Tsono adabwerera kwa Balaki, ndipo adangoona akuimirira pafupi ndi nsembe yake yopsereza, ali ndi akalonga a ku Mowabu aja. Balaki adamufunsa kuti, “Nanga Chauta wakuuzani zotani?”
18Apo Balamu adayamba kulankhula mau auneneri, adati,
“Dzukani, Balaki, ndipo mumve,
mundimvere inu mwana wa Zipori.
19Mulungu sali ngati munthu kuti angathe kunama,
si munthu kuti angathe kusintha maganizo ake.
Kodi sadzachitadi zomwe adanena?
Kapena sadzachitadi zimene adalankhula?
20Ndithu, ndalandira lamulo kuti ndidalitse.
Iye wadalitsa, ndipo ine sindingathe kusintha kanthu.
21Iye sadaone choipa mwa Yakobe,
sadaone chovuta mwa Israele.
Chauta wao ali nawo,
ndipo pakati pao pali kufuula
kuti Iye ndi mfumu yao.
22Mulungu adaŵatulutsa m'dziko la Ejipito,
ali ndi mphamvu zonga za njati.
23Zanyanga sizingamchite kanthu Yakobe,
zamaula sizingathe kulimbana ndi Israele.
Tsono anthu polankhula za Yakobe ndi za Israele adzati,
‘Onani zimene Mulungu wachita.’
24Onani Aisraele,
kudzuka kwanu kuli ngati kwa mkango waukazi,
kudzambatuka kwanu kuli ngati kwa mkango waumuna,
umene sugona pansi mpaka utagwira nyama
ndi kuidya ndi kumwa magazi ake a nyama yojiwayo.”
25Balaki adauza Balamu kuti, “Musaŵatemberere, ndipo musaŵadalitse.”
26Koma Balamu adafunsa Balakiyo kuti, “Kodi sindidakuuzeni kuti ndiyenera kuchita zonse zimene Chauta wandiwuza?”
Mau achitatu auneneri a Balamu27Balaki adauza Balamu kuti, “Tiyeni limodzi tipite ku malo ena. Mwina mwake zidzamkondwetsa Mulungu kuti muŵatemberere m'malo mwanga, mutaima pamenepo.”
28Choncho Balaki adatenga Balamu, napita naye pamwamba pa phiri la Peori loyang'anana ndi chipululu cham'munsi.
29Tsono Balamu adauza Balaki kuti, “Mundimangire maguwa asanu ndi aŵiri pano, ndipo mundikonzere ng'ombe zamphongo zisanu ndi ziŵiri ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziŵiri.”
30Balaki adachitadi monga momwe adamuuzira Balamu, napereka ng'ombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo pa guwa lililonse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.