1Ine ndemwe ndine munthu woti ndidzafa
monga anthu ena onse.
Ndine chidzukulu cha munthu woyamba uja,
amene adampanga ndi dothi uja.
Thupi langa lidapangidwa m'mimba mwa amai anga.
2Pa miyezi khumi magazi a amaiwo
adalimbitsa thupi langali.
Ndidafumira m'mbeu ya mwamuna
ndi m'chisangalatso cha ukwati.
3Inenso nditabadwa,
ndidayamba kupuma mpweya monga wa ana onse,
ndidagwa pansi pamene amaponda anthu onse.
Ndipo monga anzanga onse,
mau anga oyamba anali olira.
4Adandifunditsa nsalu
ndi kundilera mondisamala.
5Palibe mfumu ndi imodzi yomwe
imene idaona chiyambi china cha moyo wake,
6Mabadwidwe onse ndi amodzi,
mafedwenso ndi amodzi.
Solomoni adapeza luntha pakupemphera7 1Maf. 3.6-9; Lun. 9.1-18 Tsono ine ndidapemphera,
ndipo adandipatsa nzeru.
Ndidapemphera kwa Mulungu,
ndipo mzimu wa luntha udaloŵa mwa ine.
8Ndinkakonda luntha kupambana ndodo yaufumu
ndi mipando yachifumu,
chuma ndidachiyesa chachabe
nditachilinganiza ndi luntha.
9Sindidalilinganize ndi miyala yamtengowapatali,
chifukwa golide yense wa pansi pano
ndi kamchenga chabe pafupi ndi luntha,
ndipo siliva ali ngati fumbi
poyerekeza ndi luntha.
10Ndinkakonda luntha
kupambana moyo ndi kukongola.
Ndinkakonda kukhala nalo
kupambana kukhala ndi kuŵala kwa dzuŵa,
chifukwa kuŵala kwa lunthalo nkosalekeza.
11Zabwino zonse zidandidzera pamodzi ndi luntha,
m'luntha muli chuma chosaŵerengeka.
12Ndidakondwera nazo zabwino zonsezo,
chifukwa zidabwera ndi luntha lomwelo.
Koma sindinkadziŵa
kuti manthu wa zabwino zonsezo anali luntha.
13Monga ndidaphunzira za luntha mosadzikonda,
ndiziphunzitsanso mosamana.
Sindibisa zabwino zake,
14chifukwa luntha ndi chuma chosatha kwa anthu.
Okhala ndi lunthalo amapalana chibwenzi ndi Mulungu,
ndipo Mulungu amaŵakonda
chifukwa cha mphatso zobwera ndi luntha.
Solomoni apempha chithandizo cha Mulungu15Mulungu andithandize kufotokoza monga kuyenera,
maganizo anga akhale oyenera mphatso
zimene ndidazilandira.
Ndiye amene amatsogolera luntha,
ndiye amene amaongolera anthu anzeru.
16Ife pamodzi ndi mau athu tili m'manja mwake,
monganso luntha lonse ndi luso logwirira ntchito.
17Ndiye amene adandipatsa nzeru
zomvetsa bwino zinthu m'mene ziliri,
ndiye amene adandidziŵitsa mapangidwe onse
a dziko lapansi ndi makhalidwe a zinthu zokhalamo.
18Ndiye amene adandiphunzitsa chiyambi,
mathero ndi mphindikati za nthaŵi,
za mayendedwe a dzuŵa
ndiponso za masinthidwe a nyengo za chaka.
19Ndiye amene adandidziŵitsa za zigawo za chaka
ndi za magulu a nyenyezi.
20Ndiye amene adandiphunzitsa
za chilengedwe cha nyama
ndi za ukali wa zilombo.
Ndiye amene adandiwuza za mphamvu za mizimu
ndi za maganizo a anthu,
ndiye amene adandiwuza za mitundu ya mbeu
ndi mphamvu za mizu yake.
21Zonse zobisika ndi zonse zodziŵikiratu ndidaphunzira,
chifukwa luntha limene lidapanga zonse
ndiye limene lidandiphunzitsa.
Ayamikira luntha22Pajatu m'luntha muli mzimu wanzeru ndi woyera,
mzimu umodzi wokha ndi wogwira ntchito zambiri,
wosagwirika,
woyenda mwaufulu ndi woloŵerera m'zonse,
wosaipa, wapawokha, wosasinthika, wokonda zabwino,
watcheru, wosatheka kulimbana nawo.
23Mzimu umenewu ndi wachifundo,
wokonda anthu, wokhulupirika,
wosapeneka, ndi wabata,
wamphamvuzonse ndi woyang'anira zonse,
woloŵa m'mitima yonse yanzeru,
yoyera ndi yomvetsa zapatali.
24Pajatu lunthali ndi loyenda kwambiri
koposa liŵiro lina lililonse,
chifukwa chakuti ndi langwiro ndithu,
limaloŵa m'katikati mwa zinthu zonse.
25Luntha ndi mpweya wa mphamvu za Mulungu,
luntha nkunyezimira kwa ulemerero wa Wamphamvuzonse.
Nchifukwa chake koipa kalikonse sikangaloŵe m'luntha.
26Luntha nkuyera kosonyeza kuŵala kwamuyaya,
ndi kalilole kopanda maanga
koonetsa ntchito za Mulungu,
ndi chitsanzo cha ubwino wake.
27Luntha limakhoza zonse,
ngakhale lili lokha.
Limakometsanso zonse,
ngakhale ndi losasinthika.
Limaloŵa m'mitima yoyera
ya anthu a mbadwo uliwonse,
limaŵasandutsa abwenzi a Mulungu ndi aneneri.
28Pajatu amene Mulungu amaŵakonda kwambiri
ndi anthu okhala pamodzi ndi luntha.
29Pajatu luntha ndi lokongola kupambana dzuŵa,
limapambananso magulu a nyenyezi.
Limaposa kuŵala kwa usana,
30poti usiku umatsatana ndi usana,
koma zoipa sizingapambane luntha.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.