1 Yes. 19.1-25; Yer. 46.2-26 Pa tsiku lakhumi ndi chiŵiri la mwezi wakhumi, chaka chakhumi cha ukapolo, Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2“Iwe mwana wa munthu, umuimbe mlandu Farao, mfumu ya ku Ejipito, ndipo ulose modzudzula iyeyo pamodzi ndi dziko lake lonse.
3Umuuze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti,
“ ‘Ndikukuimba mlandu iwe Farao mfumu ya ku Ejipito,
iwe ching'ona chogona m'mitsinje mwako.
Wanena kuti, mtsinje wa Nailo ndi wako,
udaulenga ndiwe.
4Koma ndidzakukola ndi mbedza m'kamwa mwako,
nsomba za m'mitsinje mwako zidzakangamira ku mamba ako.
Tsono ndidzakutulutsa mumtsinjemo
pamodzi ndi nsomba zimene zakukangamira.
5Ndidzakutaya ku chipululu,
iweyo pamodzi ndi nsomba za m'mitsinje yako.
Udzagwera ku thengo popanda wina wokutola
kuti aike maliro ako.
Ndidzakusandutsa chakudya cha zilombo ndi mbalame.’
6 Yes. 36.6 “Motero onse okhala ku Ejipito adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta. Iwe Ejipito unali ngati ndodo yabango kwa Aisraele.
7Ndodoyo idaphwanyikira m'manja ataigwira, ndipo idaŵacheka pa mapewa. Ataitsamira, iyo idathyoka, ndipo m'chiwuno mwao monse mudagwedezeka.
8“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndikubweretsera nkhondo kuti idzaononge anthu pamodzi ndi nyama zomwe.
9Dziko la Ejipito lidzasanduka chipululu, lopanda anthu. Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
“Zoona, iwe udati, ‘Nailo ndi wanga, ndidamlenga ndine.’
10Tsono Ine ndikudana ndi iweyo, pamodzi ndi mitsinje yakoyo. Ndipo Ejipito ndidzamsandutsa bwinja, kuyambira ku mzinda wa Migidoli mpaka ku mzinda wa Siyene, kukafika ku malire a Etiopiya.
11Palibe phazi la munthu kapena la nyama limene lidzapondapo. Kudzakhala kopanda anthu pa zaka makumi anai.
12Dziko la Ejipito ndidzalisandutsa bwinja kupambana mabwinja a maiko ena onse. Pa zaka makumi anai mizinda yakenso idzakhala yopasuka kupambana mizinda ina yopasuka. Aejipitowo ndidzaŵamwaza pakati pa mitundu ya anthu, ndi kuŵabalalitsa pakati pa maiko ena.
13“Komabe Ine Ambuye Chauta ndikuti, Pomatha zaka makumi anaizo, ndidzasonkhanitsa Aejipito kuchokera ku mitundu ya anthu kumene adamwazikira.
14Ndidzaŵachotsa ku ukapolo, ndipo ndidzaŵabwezera ku Patirosi kumene adachokera. Kumeneko adzakhala ndi ufumu wotsika.
15Ufumuwo udzasanduka wofooka kupambana maufumu ena onse, ndipo sudzadzikuzanso pakati pa mitundu ya anthu. Ndithudi Aejipito ndidzaŵachepetsa kwambiri, kotero kuti sadzatha kulamuliranso mitundu ina.
16Aisraele sadzadaliranso Ejipito. Ndipo chilango chimenechi chidzaŵakumbutsa kuchimwa kwao kuja pamene ankapempha Aejipito kuti aŵathandize. Motero Aisraele adzadziŵa kuti Ine ndine Ambuye Chauta.”
Mfumu Nebukadinezara adzagonjetsa Ejipito17Pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, chaka cha 27 cha ukapolo, Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
18“Iwe mwana wa munthu, kale Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, idaagwiritsa ntchito ankhondo ake pokathira nkhondo mzinda wa Tiro, mpaka munthu aliyense adachita dazi chifukwa chosenza katundu, ndipo adanyuka pa phewa. Komabe ngakhale iyeyo, kapena gulu lake lankhondo, sadaphulepo kanthu pa ntchito yonse imene adaigwirayo polimbana ndi mzindawo.
19Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloniyo, ndidzampatsa Ejipito. Adzatenga chuma chake nadzachifunkha nkupita nacho. Zimenezi zidzakhala malipiro a gulu lake lankhondo.
20Ndampatsa dziko la Ejipito kuti akhale malipiro ake, chifukwa iye ndi ankhondo ake adandigwirira ntchito. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
21“Pa nthaŵi imeneyo, Aisraele ndidzaŵapatsa mphamvu zatsopano, ndipo iwe Ezekiele ndidzakulimbitsa kuti udzathe kulankhula pakati pao. Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.